Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 85

Pamakhala Chisangalalo Munthu Wochimwa Akalapa

Pamakhala Chisangalalo Munthu Wochimwa Akalapa

LUKA 15:1-10

  • FANIZO LA NKHOSA KOMANSO NDALAMA YOTAIKA

  • ANGELO AMASANGALALA KUMWAMBA

Pa nthawi imene Yesu ankachita utumiki wake anafotokoza mobwerezabwereza kufunika kokhala wodzichepetsa. (Luka 14:8-11) Iye ankafuna atapeza amuna ndi akazi omwe ankafunitsitsa kutumikira Mulungu modzichepetsa. Komabe ena mwa anthuwa anali akuchitabe machimo akuluakulu.

Afarisi ndi alembi anaona kuti anthu amene iwowo ankawaona ngati opanda ntchito ndi amene ankachita chidwi ndi Yesu komanso uthenga wake. Iwo ananena kuti: “Munthu uyu amalandira anthu ochimwa ndi kudya nawo limodzi.” (Luka 15:2) Afarisi ndi alembi amenewa ankadziona kuti anali apamwamba ndipo ankaona anthu wamba ngati fumbi la kumapazi awo. Posonyeza kuti ankawanyoza komanso kuwaona kuti ndi anthu otsika, atsogoleriwa ankatchula anthu amenewa ndi mawu Achiheberi akuti ‘amuharetsi,’ kutanthauza eni dziko.

Koma mosiyana ndi alembi ndi Afarisi, Yesu ankalemekeza anthu amenewa, kuwachitira chifundo komanso ankawamvera chisoni. Zimenezi zinachititsa kuti anthu otsika komanso anthu ena omwe ankadziwika kuti amachita machimo azichita chidwi ndi uthenga wa Yesu. Koma kodi Yesu anamva bwanji komanso anatani atazindikira kuti anthu akumunyoza chifukwa chothandiza anthu otsikawa?

Fanizo logwira mtima limene Yesu ananena limayankha funso limeneli. Fanizoli ndi lofanana ndi limene ananena ali ku Kaperenao. (Mateyu 18:12-14) M’fanizoli Yesu anafotokoza ngati kuti Afarisi anali anthu olungama komanso otetezeka m’khola la Mulungu. Pomwe anthu otsika anawafotokoza ngati anthu omwe ali kunja kwa khola ndipo ndi osochera. Yesu ananena kuti:

“Ndani wa inu amene atakhala ndi nkhosa 100, imodzi n’kutayika, sangasiye nkhosa 99 zinazo m’chipululu, n’kupita kukafunafuna imodzi yotayikayo kufikira ataipeza? Ndipotu akaipeza amainyamula paphewa pake ndipo amakondwera. Akafika kunyumba amasonkhanitsa mabwenzi ake ndi anthu oyandikana naye n’kuwauza kuti, ‘Kondwerani nane limodzi, chifukwa ndapeza nkhosa yanga imene inatayika ija.’”—Luka 15:4-6.

Kodi mfundo ya Yesu inali yoti chiyani m’fanizoli? Iye anafotokoza kuti: “Ndithu ndikukuuzani, kumwamba kudzakhalanso chisangalalo chochuluka chifukwa cha munthu mmodzi wochimwa amene walapa kuposa cha anthu 99 olungama osafunika kulapa.”—Luka 15:7.

Yesu atanena za kulapa, Afarisiwo ayenera kuti anadabwa kwambiri chifukwa iwo ankadziona kuti ndi anthu olungama ndipo sankafunika kulapa. Ndipo zaka zingapo m’mbuyomo Afarisi ena anadzudzula Yesu chifukwa choti ankadya ndi anthu okhometsa msonkho komanso ochimwa. Pa nthawiyo Yesu anawayankha kuti: “Sindinabwere kudzaitana anthu olungama, koma ochimwa.” (Maliko 2:15-17) Afarisi omwe ankadziona ngati olungamawo sanaone kufunika koti alape ndipo chifukwa cha zimenezi, Mulungu komanso angelo sanasangalale nawo. Komatu Mulungu komanso angelo amasangalala ngati munthu wochimwa walapa kuchokera pansi pamtima.

Pofuna kuthandiza anthu kumvetsa mfundo yoti munthu wochimwa komanso amene wasochera akalapa kumakhala chisangalalo kumwamba, Yesu anafotokoza fanizo lina. Fanizo limeneli limanena zimene zinkachitika nthawi imeneyo. Iye ananena kuti: “Ndi mayi uti amene atakhala ndi ndalama zokwana madalakima 10, imodzi n’kumutayika, sangayatse nyale ndi kusesa m’nyumba n’kuifufuza mosamala mpaka ataipeza? Ndipo akaipeza amasonkhanitsa amayi ena amene ndi mabwenzi ake ndi oyandikana nawo, n’kuwauza kuti, ‘Kondwerani nane limodzi, chifukwa ndapeza khobidi la dalakima linanditayika lija.’”—Luka 15:8, 9.

Mfundo ya m’fanizoli inali yofanana ndi mfundo ya m’fanizo la nkhosa yosochera. Kenako Yesu ananena kuti: “Choncho ndikukuuzani, kumakhala chisangalalo chochuluka kwa angelo a Mulungu chifukwa cha munthu mmodzi wochimwa amene walapa.”—Luka 15:10.

N’zochititsa chidwi kwambiri kuti angelo a Mulungu amasangalala kwambiri anthu ochimwa akalapa. Mfundo imeneyi ndi yofunika kwambiri kuiganizira chifukwa ochimwawo akalapa akhoza kukhala ndi mwayi wokalamulira nawo mu Ufumu wa Mulungu kumwamba, womwe ndi udindo waukulu kwambiri poyerekeza ndi udindo umene angelowo ali nawo. (1 Akorinto 6:2, 3) Komatu angelo sachita nsanje ndi zimenezi. Ndiye kodi ifeyo tiziona bwanji munthu amene walapa ndi mtima wonse n’kubwerera kwa Mulungu?