Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zoti Banja Likambirane

Zoti Banja Likambirane

Zoti Banja Likambirane

Kodi Pachithunzipa Pakusoweka Chiyani?

Werengani Danieli 6:1-24. Ndiyeno onani chithunzichi. Kodi pakusoweka chiyani? Lembani mayankho anu pamizere imene ili m’munsiyi. Kenako malizitsani kujambula chithunzichi pojambula zinthu zimene zikusowekapo komanso muchichekenire.

1. ․․․․․

2. ․․․․․

KAMBIRANANI:

N’chifukwa chiyani Danieli anaponyedwa m’malo amenewa? Kodi munayamba mwavutikapo chifukwa chochita zabwino? Fotokozani zimene zinachitika. Kodi n’chifukwa chiyani ndi bwinobe kuchita zabwino ngakhale kuti zingakupezetseni mavuto?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani 1 Petulo 2:19-21.

KODI MUKUDZIWA ZOTANI ZOKHUDZA MTUMWI MATEYU?

3. Kodi Mateyu ankadziwikanso ndi dzina lotani?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Mateyu 9:9; Maliko 2:14.

․․․․․

4. Kodi Mateyu analolera kusiya chiyani kuti akhale wotsatira wa Yesu?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Luka 5:27, 28.

․․․․․

KAMBIRANANI:

Kodi mungafunike kusiya chiyani kuti mukhale wophunzira wa Yesu? Ndipo kodi mungapeze zinthu zotani?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Maliko 10:28-30.

ZITHUNZI ZOTI ANA APEZE

Pezani zithunzi izi m’magazini ino. Kenako fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

KUCHOKERA M’MAGAZINI INO

Yankhani mafunsowa, ndipo lembani vesi kapena mavesi a m’Baibulo omwe akusowapo.

TSAMBA 6 Kodi ndani anapanga zinthu zonse? Aheberi 3:․․․

TSAMBA 7 Kodi anthu oipa chidzawachitikire n’chiyani? Miyambo 2:․․․

TSAMBA 20 Kodi anthu amafika kwa Atate kudzera mwa ndani? Yohane 14:․․․

TSAMBA 21 Kodi tizipempherera ndani? Yakobo 5:․․․

● Mayankho ali pa tsamba 12

MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 31

1. Mikango.

2. Mngelo.

3. Levi.

4. Anasiya zonse.