Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Maso a Kangaude

Maso a Kangaude

PALI akangaude ena omwe ali ndi maso osaona patali ndipo maso amenewa ndi amene amawathandiza kuona akafuna kudumpha. Kodi kangaudeyu amatha bwanji kuchita zimenezi?

Taganizirani izi: Kangaudeyu ali ndi maso anayi, awiri aakulu ndipo awiri enawo ndi aang’ono. Akafuna kudumpha kuti agwire chinachake, amagwiritsa ntchito maso aakuluwo. M’kati mwa diso lililonse lalikulu muli kachiwalo komwe kamathandiza disolo kuona ndipo kali ndi timinofu tingapo tosanjikizana. Timinofu tina takachiwaloka timathandiza kangaudeyo kuti aziona kuwala kwagirini pomwe timinofu tina timachititsa kuti asamaone bwinobwino chinthu chimene akufuna kugwira. Chinthucho chikakhala kuti chili pafupi kwambiri kangaudeyu samachiona bwinobwino. Zimene maso amenewa amachita zimathandiza kangaudeyu kuyeza kutalika kwa malo kuchokera pamene ali ndi pamene pali chinthu chimene akufuna kugwiracho.

Asayansi akufuna kupanga makamera amphamvu kwambiri komanso maloboti otha kuyeza kutalika kwa malo kuchokera pamene ali ndi pamene pali chinthu chinachake. Webusaiti ina yotchedwa ScienceNOW inanena kuti maso a kangaude ameneyu “atithandiza kumvetsa mmene maso a tizilombo tina tomwe tili ndi ubongo waung’ono ngati wantchentche, amagwirira ntchito.”

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti maso a kangaude ameneyu azigwira ntchito chonchi, kapena pali winawake amene anachititsa kuti zimenezi zizichitika?