Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Muyenera Kudziwa Ponena za Matenda a Khunyu

Zimene Muyenera Kudziwa Ponena za Matenda a Khunyu

TIYEREKEZE kuti mnzanu wagwa pansi mwadzidzidzi ndipo wakomoka. Thupi lake lalimba gwaa ndipo kenako akuyamba kuphupha. Ngati mutakhala kuti mukudziwa zoti munthuyo amagwa khunyu, mukhoza kumuthandiza podikira kuti anthu ena akuthandizeni. Anthu ambiri sawamvetsa matendawa. Choncho, tiyeni tione zinthu zina zomwe muyenera kudziwa ponena za matenda a khunyu.

Kodi khunyu ndi chiyani? Khunyu ndi matenda amene amachititsa kuti munthu azikomoka. Nthawi zambiri munthu amakomoka kwa mphindi pafupifupi 5. Zimene tafotokoza kumayambiriro kwa nkhaniyi ndi zina mwa zimene zimachitika kwa anthu amene amaphupha akagwa khunyu.

Kodi chimachititsa kuti munthu agwe khunyu n’chiyani? Ochita kafukufuku amakhulupirira kuti maselo a mu ubongo wa munthu amene amagwa khunyu amakhala ngati agwidwa shoko ndipo zimenezi n’zimene zimachititsa kuti akomoke. Koma chimene chimachititsa kuti maselowo agwidwe shoko sichikudziwikabe mpaka pano.

Ngati nditapeza mnzanga akuphupha, kodi ndiyenera kutani? Buku lina linanena kuti: “Anthu amene ali pafupi ndi munthu amene wagwa khunyu ayenera kungomusiya mpaka asiye kuphupha. Angafunike kuchotsa zinthu zomwe zingamuvulaze komanso kuonetsetsa kuti munthuyo akupuma. Koma ayenera kumutengera kuchipatala ngati akupitirizabe kuphupha kwa mphindi zopitirira 5, kapena ngati atakomokanso pambuyo poti wadzuka kapenanso ngati sakudzuka pambuyo poti wasiya kuphupha.”—The Encyclopedia of the Brain and Brain Disorders.

Kodi ndingamuthandize bwanji munthu amene wagwa khunyu? Mungachite bwino kumuikira chinachake chofewa choti atsamiritsepo mutu wake ndipo ngati pali zinthu zina zomwe zikhoza kumuvulaza, zichotseni. Munthuyo akasiya kuphupha, mugonekeni cham’mbali potsatira zimene zili patsamba 13.

Kodi ndingamuthandize bwanji munthuyo akadzuka? Choyamba mutsimikizireni kuti akhala bwino. Muthandizeni kuimirira komanso kupeza malo abwino oti angapumepo. Anthu ambiri akadzuka amasokonezeka maganizo komanso amafuna kugona, koma ena amangodzuka n’kupitiriza zimene amachita asanagwe.

Kodi anthu onse amene amadwala matendawa amaphupha akakomoka? Ayi. Ena samagwa koma amangopezeka kuti kwa kanthawi sakudziwa chimene chikuchitika, kenako amayamba kuganiza komanso kuchita zinthu bwinobwino ngati palibe chimene chachitika. Anthu ena omwe ali ndi matenda a khunyu koma osati amphamvu kwambiri, amatha kumangolimbana ndi zinthu zinazake kwa mphindi zingapo. Akhoza kumangozungulira pa malo amodzimodzi, kumakoka zovala zawo kapena kumachita zinthu zodabwitsa. Mwinanso amamva chizungulire  pambuyo poti ayamba kuganiza bwinobwino.

Kodi anthu amene amadwala matenda a khunyu amakumana ndi mavuto otani? Anthu ambiri amene ali ndi matenda a khunyu amakhala ndi mantha chifukwa sadziwa nthawi komanso malo amene angayambire kudwala, ndipo zimenezi n’zomveka. Chifukwa cha zimenezi amapewa kukhala pagulu.

Kodi ndingamuthandize bwanji munthu amene amadwala matenda a khunyu? Muzimulimbikitsa kuti azikuuzani mmene akumvera ndipo muzimumvetsera mwatcheru akamalankhula. Mukhozanso kumufunsa zimene angafune kuti muchite akayamba kudwala. Popeza anthu ambiri odwala khunyu sangachite okha zinthu zina, mwina mungachite naye limodzi zinthuzo kapena mukhoza kungomuchitira.

Kodi munthu angatani kuti asamadwale matendawa pafupipafupi? Pali zinthu zina zomwe zingapangitse kuti munthu azidwala matendawa pafupipafupi, monga kuvutika maganizo komanso kusagona mokwanira. N’chifukwa chake akatswiri a matendawa amalimbikitsa kuti anthu akhunyu azipuma mokwanira komanso kuti azichita masewera olimbitsa thupi n’cholinga choti azichepetsa nkhawa. Anthu ena amamwa mankhwala kuti asamadwale pafupipafupi.