Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | MWAMUNA NDI MKAZI WAKE

Ngati Banja Lanu Silikuyenda Bwino

Ngati Banja Lanu Silikuyenda Bwino

VUTO LIMENE LIMAKHALAPO

Musanakwatirane, inu ndi mwamuna kapena mkazi wanu munkaona kuti mumakonda zofanana. Koma tsopano mwazindikira kuti mukusiyana pa zinthu zambiri. Choncho simukuonanso mkazi kapena mwamuna wanuyo ngati mnzanu koma mukungomuona ngati munthu wokhala naye m’nyumba imodzi basi.

Komatu musataye mtima chifukwa zinthu zikhoza kuyamba kuyenda bwino. Koma choyamba mungafunike kudziwa chimene chikupangitsa kuti musamagwirizane.

ZIMENE ZIMACHITITSA

Zochitika pa moyo. Zinthu monga ntchito za tsiku ndi tsiku, kulera ana komanso kuchita zinthu ndi akuchimuna kapena akuchikazi, zingabweretse mavuto ena m’banja. Mavuto osayembekezereka monga a zachuma kapena kusamalira mwana kapenanso wachibale amene akudwala matenda aakulu kukhozanso kubweretsa mavuto ena.

Kusiyana zokonda. Anthu ena akakhala pa chibwenzi, amatha kudziwa kuti amakonda zosiyana koma amangozinyalanyaza. Koma akakwatirana, amazindikira kuti ndi osiyana kwambiri pa nkhani monga, njira zolankhulirana, kugwiritsa ntchito ndalama komanso kuthetsa mavuto. Mavuto amene poyamba ankangowanyalanyaza aja, amayamba kuwaona kuti ndi aakulu moti sangathenso kuwapirira.

Ngati aliyense akungoyendera yake. Pakapita nthawi mawu komanso zochita zosaganizirana, kuphatikizapo mavuto osiyanasiyana osathetsedwa, zimapangitsa mwamuna ndi mkazi wake kuti asamauzane zakukhosi. Zimenezi zingapangitsenso kuti wina kapena onse ayambe kugwirizana kwambiri ndi munthu wina n’cholinga choti apeze womamuuza mavuto ake.

Ngati zimene munkayembekezera si zimene zikuchitika. Anthu ena amalowa m’banja ndi maganizo oti apeza munthu wabwino kwambiri amene Mulungu wawapatsa kuti amange naye banja. Ngakhale kuti anthu amakhala ndi maganizo amenewa chifukwa chotengeka ndi chikondi, maganizowa akhoza kubweretsa mavuto m’banja. Mavuto akangoyamba, maganizo oti ndinu oyenerana aja amathera pomwepo ndipo aliyense amayamba kuganiza kuti analakwitsa pokwatirana ndi mnzakeyo.

 ZIMENE MUNGACHITE

Muziganizira kwambiri makhalidwe abwino amene mnzanuyo ali nawo. Tayesani izi: Lembani makhalidwe abwino atatu omwe mwamuna kapena mkazi wanuyo ali nawo. Mwina mungawalembe kuseli kwa chithunzi cha ukwati wanu kapena m’foni yanu. Nthawi zonse muziona makhalidwe amenewa kuti azikukumbutsani chimene chinakuchititsani kukwatirana ndi mnzanuyo. Kuganizira za makhalidwe abwino a mwamuna kapena mkazi wanu kumathandiza kuti muzikhala mwamtendere m’banja. Kungakuthandizeninso kuthetsa kusiyana maganizo kapena mavuto amene mukukumana nawo.—Lemba lothandiza: Aroma 14:19.

Muzipeza nthawi yochitira limodzi zinthu zina. Musanakwatirane, n’zoonekeratu kuti munkapeza nthawi yochitira zinthu limodzi. Pa nthawi imene munali pa chibwenzi muyenera kuti munkasangalala, ndipo simunkalola kuti chinachake chikusokonezeni. Mungachite bwino kuchitanso chimodzimodzi. Musalole kuti chilichonse chisokoneze banja lanu. Muzipeza nthawi yochitira zinthu limodzi ngati mmene munkachitira muli pa chibwenzi. Kuchita zimenezi kudzakuthandizani kuti muzigwirizana kwambiri komanso kuti muzithetsa mosavuta mavuto amene amabwera mosayembekezereka.—Lemba lothandiza: Miyambo 5:18.

Muziuzana zakukhosi. Ngati mwakhumudwa ndi zimene mnzanuyo wachita kapena kunena, mwina mukhoza kungoinyalanyaza nkhaniyo. Koma ngati mukuona kuti simungathe kuinyalanyaza, ndi bwino kukambirana nkhaniyo m’malo mongokhala chete. Musalole kuti padutse nthawi yaitali musanakambirane nkhaniyo, ndipo ngati n’kotheka kambiranani tsiku lomwelo, koma muyenera kuchita zimenezi modekha.—Lemba lothandiza: Aefeso 4:26.

Ngati mwakhumudwa ndi zimene mnzanu wachita kapena kunena, mwina mukhoza kungoinyalanyaza nkhaniyo

Muzikumbukira kuti mnzanuyo sachita kufuna kuti akukhumudwitseni. N’zodziwikiratu kuti nthawi zambiri, palibe mwamuna kapena mkazi amene angafune kukhumudwitsa dala mnzake. Mukakhumudwitsa mwamuna kapena mkazi wanu, m’pepeseni kuchokera pansi pamtima ndipo mutsimikizireni kuti simunachite mwadala. Ndiyeno kambiranani zinthu zimene nonsenu muyenera kupewa kuti musamakhumudwitsane. Tsatirani malangizo a m’Baibulo akuti: “Khalani okomerana mtima, achifundo chachikulu, okhululukirana ndi mtima wonse.”—Aefeso 4:32.

Dziwani kuti muzikumanabe ndi mavuto. Baibulo limanena kuti anthu onse apabanja “adzakhala ndi nsautso.” (1 Akorinto 7:28) Mukamakumana ndi mavuto oterewa, musafulumire kuganiza kuti munakwatirana ndi munthu wolakwika. M’malomwake nonse muyenera kuyesetsa kuthetsa mavutowo komanso ‘kupitiriza kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse.’—Akolose 3:13.