Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | KULERA ANA

Kodi Mungatani Kuti Musamangopatsa Mwana Wanu Chilichonse Chimene Akufuna?

Kodi Mungatani Kuti Musamangopatsa Mwana Wanu Chilichonse Chimene Akufuna?

VUTO LIMENE LIMAKHALAPO

Tiyerekeze kuti mwana wanu akufuna kuti mum’patse zinazake ndipo mwamukaniza. Koma akukakamirabe ngakhale kuti mwayesera umu ndi umu kumuletsa. Zimenezi zikukupsetsani mtima ndipo mukuganiza zongom’patsa zimene akufunazo kuti asiye kukuvutitsani.

Komatu n’zotheka kukaniza mwana zimene akufuna ngakhale atakhala kuti akukakamira. Choyamba tiyeni tikambirane zimene muyenera kudziwa pa nkhaniyi.

ZIMENE MUYENERA KUDZIWA

Kukaniza mwana zinazake, si nkhanza. Makolo ena amaona kuti si bwino kungokaniza mwana zimene akufuna. Amaona kuti ndi bwino kuchita kumupempha kapena kukambirana naye n’kumufotokozera bwinobwino chifukwa chake akumukaniza. Amaonanso kuti kukaniza mwana zinazake kungakwiyitse mwanayo.

N’zoona kuti mwana sasangalala mukamukaniza zimene akufuna. Komabe zimamuphunzitsa mfundo yofunika kwambiri yakuti, si zinthu zonse zomwe munthu amafuna zimene zimatheka. Koma mukamangopatsa mwana wanu chilichonse chifukwa choti akuumirira, zingapangitse kuti asamakumvereni ndipo akafuna chinthu akhoza kumakuvutitsani podziwa kuti pamapeto pake muvomera. Zimenezi zingapangitse kuti mwanayo asamakulemekezeni poona kuti simuchedwa kusintha maganizo.

Kukaniza mwana zinazake kungadzamuthandize akadzakula. Mwana akamakanizidwa zimene akufuna zimamuthandiza kuti akhale wodziletsa. Zimenezi zingamuthandize kuti akamakula asamangotengera zochita za anzake monga kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo kapena kuchita chiwerewere.

Mukamapewa kupatsa mwana wanu chilichonse chimene akufuna, zingadzamuthandize akadzakula. David Walsh ananena kuti: “Anthu akuluakulufe sitipeza chilichonse chimene tikufuna. Choncho si bwino kupatsa ana athu chilichonse chomwe akufuna, chifukwa tikamachita zimenezi ndiye kuti tikuwaphunzitsa kuti angathe kupeza chilichonse chimene akufuna.” *

 ZIMENE MUNGACHITE

Cholinga chanu chizikhala kuthandiza mwanayo kuti akule bwino. Makolo ambiri amafuna kuphunzitsa mwana wawo kuti akadzakula adzakhale wodziletsa. Koma ngati mumapatsa mwana wanu chilichonse chimene akufuna, cholinga chimenechi sichingakwaniritsidwe. Baibulo limasonyeza kuti munthu ‘wosasatitsidwa kuyambira ali mwana, akadzakula adzakhala wosayamika.’ (Miyambo 29:21) Choncho njira ina yophunzitsira mwana, ndi kusam’patsa zimene akufuna. Mwanayo sangafe kapena kudwala chifukwa cha zimenezi. M’malomwake zidzamuthandiza akadzakula.—Lemba lothandiza: Miyambo 19:18.

Mukamamuletsa zinazake, muzinena motsimikiza. Musaiwale kuti inu ndi mwana wanuyo si inu ofanana. Choncho palibe chifukwa choti mukafuna kumukaniza kanthu, muzitsutsanatsutsana za nkhaniyo. Sikuti iyeyo amafunika kuvomereza kaye. N’zoona kuti akamakula adzafunika ‘kuphunzitsa mphamvu zake za kuzindikira kuti azitha kusiyanitsa choyenera ndi chosayenera.’ (Aheberi 5:14) Choncho palibe vuto ngati nthawi zina mutamakambirana naye. Komabe palibe chifukwa choti nthawi zonse mukafuna kukaniza mwana wanuyo zinazake muzikambirana naye. Mukamakangana kapena kutsutsana kwambiri pa nkhani inayake, mwanayo amayamba kuganiza kuti mukumupempha ndipo ali ndi ufulu wokana ngati sakugwirizana nazo.—Lemba lothandiza: Aefeso 6:1.

Musamasinthe maganizo. Mukakaniza mwana wanu zinazake, angayambe kuvuta kapena kuchonderera pofuna kudziwa ngati mwatsimikizadi. Kodi zikatere mungatani? Buku lina linati: “Mungachite bwino kuchokapo. Mwinanso mungamuuze kuti, ‘Ngati ukufuna kulira palibe vuto, koma usalilire pano chifukwa sindikufuna kuti uzindisokosera. Upeze malo oti uzikalilirako ndipo ukamabwera kuno ukhale utatonthola.’” (Loving Without Spoiling) Poyamba zingakhale zovuta kumuuza mwana zimenezi. Nayenso mwanayo angaone ngati mukumuchitira nkhanza. Koma akaona kuti mwatsimikiza, sangachitenso makani.—Lemba lothandiza: Yakobo 5:12.

Musamakanize mwana chinthu pongofuna kusonyeza kuti ndinu kholo lake

Musamangomukaniza zilizonse. Komabe si bwino kukaniza mwana chinthu pongofuna kusonyeza kuti ndinu kholo lake. M’malomwake muzikhala wololera. (Afilipi 4:5) Nthawi zina mungam’patse zimene akufuna. Mungachite izi ngati mukuona kuti simukuchita zimenezi chifukwa choti mwanayo akuvutitsa kapenanso ngati zimene akufunazo sizolakwika.—Lemba lothandiza: Akolose 3:21.

^ ndime 10 Mawu amenewa achokera m’buku lakuti, No: Why Kids—of All Ages—Need to Hear It and Ways Parents Can Say It.