Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Amachita Zinthu Bwinobwino Ngakhale Kuti Ndi Osaona

Amachita Zinthu Bwinobwino Ngakhale Kuti Ndi Osaona

Mayi wina wosaona dzina lake Paqui, yemwe mwamuna wakenso ndi wosaona, anati: “Vuto langali linayamba nditangobadwa kumene. Madokotala anandithira mankhwala amphamvu kwambiri m’maso moti kungoyambira nthawi imeneyo mpaka ndili wachinyamata, ndinkaona movutikira kwambiri. Kenako ndinasiyiratu kuona. Zimenezi zinachititsa kuti ndiyambe kuvutika maganizo.”

PALI zifukwa zambiri zimene zimachititsa kuti anthu aziona movutikira komanso kuti akhale osaona. Nthawi zina vutoli limayamba chifukwa cha matenda kapena chifukwa chovulala. Munthu amasiya kuona, mitsempha yotumiza zithunzi ku ubongo kapena mbali ya ubongo yomwe imathandiza kuti munthu aziona ikawonongeka. Anthu ambiri amene amavutika kuona komanso amene saoneratu, safuna kuvomereza kuti sangathe kuchita zinthu zina ndipo nthawi zambiri sasangalala komanso amakhala amantha. Komatu pali anthu ambiri amene amachitabe zinthu bwinobwino ngakhale kuti ndi osaona.

Zinthu zambiri zimene timadziwa, timakhala kuti tinachita kuziona. Ndiye munthu akasiya kuona, amadalira kumva mawu, phokoso komanso fungo. Amadaliranso manja ndi zala zake kuti adziwe zinthu.

Magazini ina inanena kuti asayansi atulukira kuti zinthu zikasintha, “ubongo wathunso umasintha.” (Scientific American) Magaziniyi inanenanso kuti: “Munthu akasiya kuona, ubongo wake umasintha moti amatha kugwiritsa ntchito ziwalo zina kuti achite zomwe maso akanachita.” Kodi zimenezi zimachitika bwanji?

Amamva mawu kapena phokoso: Osaona amatha kuona zinthu m’maganizo mwawo akamva mawu a munthu kapena phokoso linalake. Mwachitsanzo bambo wina wosaona, dzina lake Fernando, anati: “Ndimatha kuzindikira munthu, pongomva mawu ake kapena mtswatswa.” Nawonso a Juan, omwe ndi osaona, anati: “Anthu osaonafe timazindikira munthu tikangomva mawu ake.” Kuwonjezera pamenepa, osaona amadziwa mmene munthu akumvera akamva mmene munthuyo akulankhulira. Mwachitsanzo amatha kuzindikira ngati munthuyo wakwiya, akudandaula kapena ngati akusangalala.

Wosaona amathanso kugwiritsa ntchito zimene wamva kuti adziwe malo amene ali, kumene zinthu zikulowera, kukula kwa chipinda komanso ngati patsogolo pake pali chinthu chomwe chingamugwetse.

Amamva fungo: Wosaona akhoza kudziwa zimene zikuchitika komanso malo amene ali, akangomva fungo linalake. Mwachitsanzo, akamayenda n’kumva kafungo kabwino ka chakudya, amadziwa kuti pamene akudutsapo pakuphikidwa chakudya. Kenako amagwirizanitsa kafungoko ndi zimene akumva n’kudziwa kuti mwina pamalopo pali lesitilanti, moti akamadzadutsanso malo omwewo, amatha kukumbukira mmene angayendere.

Amagwiritsa ntchito manja komanso zala: Bambo wina wosaona, dzina lake Francisco, anati: “Manja angawa ndiye maso anga.” Nthawi zambiri anthu osaona amagwiritsa ntchito manja awo kuti adziwe kumene akupita ndipo akamayenda amagwiritsa ntchito ndodo. A Manasés omwe anabadwa osaona anayamba kugwiritsa ntchito ndodo ali mwana. Iwo anati: “Ndodoyi imandithandiza kudziwa malo amene ndili. Ndimatha kukumbukira kuti njira imene ndikuyendayo ndinaidutsapo pongoyendetsa ndodoyi.”

Akuwerenga Nsanja ya Olonda ya zilembo za anthu osaona

Anthu ambiri osaona amagwiritsa ntchito zala zawo powerenga mabuku a zilembo za anthu osaona. Masiku ano pali mabuku ambiri othandiza anthu osaona kuti adziwe zambiri za Baibulo komanso kuti azikhala ndi moyo wabwino. N’zosangalatsanso kuti pali mabuku, magazini komanso timapepala tomwe tinajambulidwa n’cholinga choti anthu osaona azimvetsera. Palinso makompyuta omwe anakonzedwa kuti azithandiza osaona kuwerenga. Zinthu zimenezi zikuthandiza kwambiri osaona kuti azitha kuwerenga Baibulo komanso mabuku ena ofotokoza Baibulo. *

Mabuku amenewa anathandiza kwambiri a Paqui komanso amuna awo, omwe tawatchula kale aja. Iwo amasangalala kwambiri komanso sakhala ndi nkhawa chifukwa amadziwa kuti mavuto amene akukumana nawo ndi osakhalitsa. Anthu a mumpingo wawo wa Mboni za Yehova, amawathandizanso kwambiri. A Paqui anati: “Panopa zinthu zimatiyendera kwabasi ndipo timaona kuti tili ndi moyo wabwino kwambiri kuposa poyamba.”

N’zoona kuti anthu osaona amakumana ndi mavuto ambiri. Koma m’nkhaniyi taona kuti akhoza kumachita zinthu bwinobwino komanso kumakhala mosangalala.

^ ndime 10 A Mboni za Yehova amapanga mabuku a zilembo za anthu osaona m’zinenero zoposa 25.