Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Dzina la Mulungu Ndi Ndani?

Kodi Dzina la Mulungu Ndi Ndani?

Mukafuna kumudziwa munthu, nthawi zambiri mumayamba ndi kumufunsa kuti, “Dzina lanu ndani?” Ndiye mutati mufunse Mulungu funso limeneli, kodi angayankhe kuti chiyani?

“Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli.”​Yesaya 42:8.

Kodi dzina limeneli ndi lachilendo kwa inu? Mwinadi ndi lachilendo, chifukwa anthu ambiri omasulira Mabaibulo sanaike dzina la Mulungu m’malo ambiri, pomwe ena sanaliike n’komwe. Nthawi zambiri pamene panali dzinali anaikapo dzina laudindo lakuti, “AMBUYE.” Komatu m’mipukutu yoyambirira ya Baibulo dzinali linkapezekamo pafupifupi ka 7,000. Dzinali limakhala ndi makonsonanti achiheberi 4 omwe ndi ofanana ndi YHWH ndipo m’Chichewa lakhala likumasuliridwa kuti “Yehova.”

Dzina la Mulungu limapezeka kambirimbiri mu zolemba zachiheberi komanso m’Mabaibulo ambiri

Mpukutu wa Masalimo wa ku Nyanja Yakufa 30-50 C.E., CHIHEBERI

Baibulo la Tyndale 1530, CHINGELEZI

Baibulo la Reina-Valera 1602, CHISIPANISHI

Baibulo la Union Version 1919, CHITCHAINIZI

N’CHIFUKWA CHIYANI DZINA LA MULUNGU LILI LOFUNIKA?

Mulungu mwiniwake amaona kuti dzinali ndi lofunika. Palibe amene anamupatsa dzina lakuti Yehova. Mulungu anadzipatsa yekha dzinali. Yehova anati: “Limeneli ndilo dzina langa mpaka kalekale, ndipo ndicho chondikumbukirira ku mibadwomibadwo.” (Ekisodo 3:15) M’Baibulo, dzina la Mulungu limapezekamo kwambiri kuposa mayina ake audindo monga Wamphamvuyonse, Atate, Ambuye kapena Mulungu. Limapezekanso kwambiri kuposa mayina a anthu ngati Abulahamu, Mose, Davide kapena Yesu. Komanso Yehova amafuna kuti anthu adziwe dzina lakeli. Baibulo limati: “Anthu adziwe kuti inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, Inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, wolamulira dziko lonse lapansi.”​—Salimo 83:18.

Yesu amaona kuti dzinali ndi lofunika. M’pemphero limene anthu ambiri amalitchula kuti Pemphero la Atate Wathu kapena Pamphero la Ambuye, Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti azipempha Mulungu kuti: “Dzina lanu liyeretsedwe.” (Mateyu 6:9) Komanso iye anapemphera kwa Mulungu kuti: “Atate lemekezani dzina lanu.” (Yohane 12:28) Yesu ankaona kuti nkhani yolemekeza dzina la Mulungu ndi yofunika kwambiri. N’chifukwa chake anatha kunena m’pemphero kuti: “Ine ndachititsa kuti iwo adziwe dzina lanu ndipo ndidzapitiriza kuwadziwitsa dzinalo.”​—Yohane 17:26.

Anthu amene amadziwa Mulungu amaona kuti dzinali ndi lofunika. Anthu a Mulungu akale ankadziwa kuti dzina la Mulungu linkathandiza kuti azitetezedwa komanso kupulumutsidwa. “Dzina la Yehova ndi nsanja yolimba. Wolungama amathawira mmenemo ndipo amatetezedwa.” (Miyambo 18:10) Komanso “aliyense woitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.” (Yoweli 2:32) Baibulo limasonyezanso kuti dzina la Mulungu limatithandiza kusiyanitsa anthu amene samutumikira ndi amene amamutumikira. Limati: “Mtundu uliwonse wa anthu udzayenda m’dzina la mulungu wake. Koma ife tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu mpaka kalekale, inde mpaka muyaya.”​—Mika 4:5; Machitidwe 15:14.

KODI DZINA LA MULUNGU LIMATITHANDIZA KUDZIWA ZINTHU ZITI?

Dzinali limatithandiza kudziwa kuti iye ndi wosiyana ndi milungu ina. Akatswiri ambiri a maphunziro amati dzina la Yehova limatanthauza kuti: “Amachititsa Zinthu Kuchitika.” Yehova Mulungu anatithandiza kumvetsa tanthauzo la dzina lake pamene anauza Mose kuti iye ndi: “Ndidzakhala Amene Ndidzafune Kukhala.” (Ekisodo 3:14) Choncho sikuti dzina la Mulungu limangotiuza za udindo wake monga Mlengi amene anachititsa kuti zinthu zonse zikhaleko. Dzinali limatanthauzanso kuti iye angathe kudzichititsa yekha kapena kuchititsa zinthu zimene analenga kuti zikhale chilichonse chimene akufuna, kuti akwaniritse cholinga chake. Mayina ake audindo aja amangotiuza za udindo, ulamuliro kapena mphamvu zake. Koma dzina lake lokha loti Yehova ndi limene limafotokoza zonse zokhudza iyeyo komanso zimene angakwanitse kuchita.

Dzinali limatithandiza kudziwa kuti Mulungu amatikonda. Tanthauzo la dzina la Mulungu limasonyeza kuti iye amakonda zimene analenga, kuphatikizapo anthufe. Komanso mfundo yoti Yehova wachititsa kuti dzina lake lidziwike, ikusonyeza kuti amafuna kuti timudziwe. Ndipotu iye ndi amene anayamba kutiuza dzina lake tisanadziwe n’komwe kuti pali mwayi woti tingamufunse dzina. Apa n’zoonekeratu kuti Mulungu safuna kuti tizimuona ngati ndi wosamvetsetseka kapena ngati Mulungu amene sitingathe kumufikira chifukwa choti ali kutali. Koma amafuna kuti tizimuona kuti ndi weniweni ndipo tingathe kukhala naye pa ubwenzi.​—Salimo 73:28.

Tikamagwiritsa ntchito dzina la Mulungu timasonyeza kuti timamukonda. Tiyerekeze kuti mwauza munthu amene mukufuna kuti akhale mnzanu kuti akamakuitanani azitchula dzina lanu lenileni. Kodi mungamve bwanji ngati munthuyo nthawi zonse safuna kukutchulani dzina? Mwina mungayambe kukayikira ngati akufunadi kuti mukhale mnzake. N’chimodzimodzinso ndi Mulungu. Yehova anatiuza dzina lake ndipo amatilimbikitsa kuti tizilitchula. Tikamachita zimenezi Yehova amaona kuti tikufuna kuti akhale mnzathu. Ndipotu Baibulo limasonyeza kuti ngakhale ‘tikamangoganizira za dzina lakeli,’ Yehova amadziwa.​—Malaki 3:16.

Kudziwa dzina la Mulungu n’kofunika kwambiri komanso ndi poyambira pabwino ngati tikufuna timudziwe. Koma sitiyenera kulekera pomwepo. Tiyenera kudziwa zambiri za Mwiniwake wa dzinali. Mwachitsanzo, tiyenera kudziwa kuti ndi wotani kwenikweni.

KODI DZINA LA MULUNGU NDI NDANI? Dzina la Mulungu ndi Yehova. Dzina limeneli limamusiyanitsa ndi milungu ina ndipo limasonyeza kuti angathe kukwaniritsa zimene akufuna kuchita