Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Anamusonyeza Kukoma Mtima

Anamusonyeza Kukoma Mtima

BAMBO a mnyamata wina dzina lake John anabatizidwa chakumapeto kwa zaka za m’ma 1950 m’katauni kena ku Gujarat m’dziko la India. John, azichimwene ake, azichemwali ake komanso mayi ake anali akatolika olimbikira kwambiri ndipo ankadana ndi zimene abambo awo ankakhulupirira.

Tsiku lina, John anapemphedwa ndi bambo ake kuti akapereke kalata kwa mnzawo wina wa Mboni. Tsiku limenelo, John anadzicheka chala potsegula mgolo. Koma pofuna kumvera bambo akewo, anangomanga chalacho ndi kansalu kenakake n’kupita kukapereka kalatayo.

John atafika anapeza mkazi wa munthuyo yemwenso anali wa Mboni za Yehova. Polandira kalatayo, mkaziyo anaona kuti chala chake n’chovulala ndipo anamuuza kuti amuthandiza. Anatsuka balalo ndi mankhwala n’kulimanga bwinobwino ndi bandeji. Kenako anamupangira tiyi n’kumacheza naye nkhani zina zokhudza Baibulo.

Apa John anayamba kusintha maganizo ake odana ndi a Mboni. Iye anafunsa mkaziyo mafunso awiri okhudza nkhani zimene ankasiyana maganizo ndi bambo ake. Anamufunsa ngati Yesu si Mulungu komanso ngati Akhristu sayenera kupemphera kwa Mariya. Mlongoyo anagwiritsa ntchito Baibulo poyankha mafunsowo ndipo anakambirana naye m’chilankhulo chake chomwe ndi Chigujarati. Kenako anamupatsa kabuku kofotokoza za uthenga wabwino wa Ufumu.

Atawerenga kabukuko, John anazindikira kuti wapeza choonadi cha m’Baibulo. Iye anapita kwa wansembe n’kukamufunsanso mafunso awiri aja. Wansembeyo anapsa mtima kwambiri n’kumugenda ndi Baibulo uku akukalipa kuti: “Wasanduka Satana iwe eti? Tandiuze. Ndi pati m’Baibulo pamene amanena kuti Yesu si Mulungu? Nanga ndi pati pamene amati tisamalambire Mariya?” John anadabwa kwambiri ndi zimene wansembeyu anachita moti anamuuza kuti: “Sindidzapondanso mutchalitchi chachikatolika” ndipo anasiyiradi pomwepo kupita kutchalitchicho.

John anayamba kuphunzira ndi a Mboni ndipo anayamba kutumikira Yehova. Patapita nthawi, achibale ake ena anachitanso chimodzimodzi. Panopa John ali ndi chipsera pa chala chomwe anavulala zaka 60 zapitazo. Koma amakumbukira kuti kukoma mtima kumene anasonyezedwa pa nthawiyo kunamuthandiza kuti ayambe kulambira Yehova.​—2 Akor. 6:4, 6.