Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mbewu za Choonadi Zafika Kumadera Akutali

Mbewu za Choonadi Zafika Kumadera Akutali

Mbewu za Choonadi Zafika Kumadera Akutali

DZIKO la Tuva lili kum’mwera kwenikweni kwa chigawo cha Siberia ku Russia. Ndipo kum’mwera ndi kum’mawa kwa dzikoli kuli dziko la Mongolia. Anthu ambiri a ku Tuva amakhala kumadera akumidzi ndipo n’zovuta kwambiri kuti anthu awafikire ndi uthenga wa Ufumu. Pa nthawi ina anthu ambiri ochokera m’madera osiyanasiyana a dziko la Tuva anapita ku zokambirana mumzinda wa Kyzyl womwe ndi likulu la dzikoli. Maria amachita upainiya mumzinda wa Kyzyl ndipo atamva za kufika kwa anthuwo, anaona kuti umenewu ndi mwayi woti awalalikire uthenga wabwino.

Pofotokoza zimene zinachitika, Maria anati: “Aphunzitsi a pasukulu imene ndinkaphunzitsa anakonza zoti pakhale zokambirana zokhudza kuledzera ndi kugwiritsa ntchito mankhwala m’njira zosayenera. Anthu oposa 50 ochokera m’madera akutali kwambiri a dzikoli, anaitanidwa. M’gulu la anthuwa munali aphunzitsi, akatswiri a zamaganizo, oyang’anira za kasamalidwe ka ana ndipo panalinso anthu ena.” Maria anaona kuti umenewu ndi mwayi wake komabe zinali zovutirapo. Iye anati: “Mwachibadwa ndine munthu wamanyazi ndipo kulalikira mwamwayi kumandivuta. Koma ndinapemphera kwa Yehova kuti andithandize kukhala wolimba mtima n’cholinga choti ndichitire umboni pa nthawi imeneyi.” Kodi zolinga zake zinatheka?

Maria anapitiriza kuti: “Ndinapeza Galamukani! ina imene imafotokoza za vuto la anthu ochita mantha kwambiri. Ndinaganiza kuti magazini imeneyi ingakamusangalatse katswiri wa zamaganizo ndiye ndinaitenga popita kusukulu. Tsiku limenelo mphunzitsi wina amene anabwera pa zokambiranazo analowa mu ofesi yanga ndipo ndinamupatsa magaziniyo. Iye anailandira mosangalala. Ndipo ananena kuti nayenso anali ndi vuto lochita mantha kwambiri. Tsiku lotsatira ndinamutengera buku lakuti Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba. Iye analilandiranso mosangalala. Zimenezi zinandichititsa kuganiza kuti mwina aphunzitsi ena angalikondenso. Choncho popita kusukulu ndinatenga katoni ya mabuku a Zimene Achinyamata Amafunsa komanso zofalitsa zina.” Pasanapite nthawi yaitali mabuku onse m’katoniyo anatha. Pofotokoza zimene zinachitika, Maria anati: “Anzake a mphunzitsi amene ndinamupatsa buku la Zimene Achinyamata Amafunsa anabwera mu ofesi yanga n’kumafunsa kuti, ‘Kodi mabuku amene akugawidwawa akupezeka kuti?’” Mabukuwa anafika pa nthawi yake.

Zokambiranazi zinatha Loweruka. Maria sanagwire ntchito pa tsikuli choncho anangoika mabuku pamatebulo angapo mu ofesi yake. Ndipo analemba pakabolodi kenakake kuti, “Okondedwa Aphunzitsi, mungathe kutenga mabuku amene mukufuna komanso mungatengere anzanu. Mabukuwa ndi abwino kwambiri ndipo akuthandizani pantchito yanu komanso akuthandizani kuti mabanja anu akhale olimba.” Ndiyeno kodi zotsatira zake zinali zotani? “Nditapita ku ofesi tsiku limeneli, ndinapeza kuti mabuku ambiri atengedwa. Choncho ndinakatenganso mwamsanga mabuku ndi magazini ena.” Pamene zokambiranazi zinkatha, Maria anali atagawira magazini 380, mabuku 173 ndi timabuku 34. Anthu amene anabwera ku zokambiranazi anabwerera kwawo komanso kumene amagwira ntchito atatenga mabuku ndi magaziniwa. Maria anati: “Ndine wosangalala kwambiri chifukwa chakuti mbewu za choonadi zafika kumadera akutali kwambiri a ku Tuva kuno.”​—Mlal. 11:6.

[Mapu patsamba 32]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

RUSSIA

TUVA REPUBLIC