Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Nyamula Mwana Wako”

“Nyamula Mwana Wako”

Yandikirani Mulungu

“Nyamula Mwana Wako”

2 MAFUMU 4:8-37

IMFA ya mwana ndi chimodzi mwa zinthu zopweteka kwambiri pamoyo wa munthu. Koma Yehova Mulungu akhoza kuthetsa kupweteka kumeneko. Tikudziwa kuti angathedi kuchita zimenezi chifukwa Baibulo limatchula za anthu angapo amene Mulungu anawapatsapo mphamvu zoukitsa akufa. Chitsanzo chimodzi ndi chimene chili pa 2 Mafumu 4:8-37 pamene mneneri Elisa anaukitsa kamnyamata.

Nkhaniyi inachitikira mumzinda wa Sunemu. Mumzindawu munkakhala mkazi wina wosabereka ndi mwamuna wake amene ankakonda kuchereza Elisa pomupatsa chakudya ndi malo ogona akafika pakhomo pawo. Pofuna kuthokoza, tsiku lina mneneriyu anauza mkaziyo kuti: “Nyengo ino chaka chikudzachi udzafukata mwana wamwamuna.” Mogwirizana ndi mawu a Elisa, mkaziyo anakhaladi ndi mwana wamwamuna, zimene poyamba ankaona ngati zosatheka. Koma chomvetsa chisoni chinali chakuti mwanayo sanakhalitse. Patangopita zaka zochepa chabe, mwanayo anadwala kwambiri mutu ali kumunda. Atamutengera kunyumba, mwanayo anamwalira ali “pa maondo [a mayi] ake.” (Mavesi 16, 19, 20) Mayi wofedwayo ananyamula mtembo wa mwana wakeyo, n’kuugoneka bwinobwino pabedi limene mneneri uja amagona akabwera kunyumba kwawo.

Ndi chilolezo cha mwamuna wake, mkaziyo ananyamuka nthawi yomweyo ndi kuyenda ulendo wa makilomita 30 kupita kuphiri la Karimeli kukaonana ndi Elisa. Atakumana ndi Elisa, mayiyu sanayambe kulira mokweza kapena mosisima kapenanso kuchita china chilichonse chosonyeza kuti ali ndi chisoni chachikulu. Kodi anachita zimenezo chifukwa anamva kuti m’mbuyomo mneneri Eliya, amene analowedwa m’malo ndi mneneri Elisa, anaukitsapo mwana wa mayi wamasiye? (1 Mafumu 17:17-23) Kodi mkazi wa ku Sunemu ameneyu anali ndi chikhulupiriro chakuti Elisa akhoza kuukitsanso mwana wake? Kaya zinali zotani, koma iye anakana kubwerera kwawo mpaka Elisa atavomera kupita naye limodzi.

Atafika ku Sunemu, Elisa analowa m’chipinda chimene amagonamo akabwera mumzindawu, ndipo anaona mtembo mwa mwana uja “pakama pake.” (Vesi 32) Mneneriyo anapemphera kwa Yehova mochonderera kwambiri. Ndiyeno, Elisa ali chiweramire, ‘mnofu wa mwanayo unafunda,’ ndipo mtima wake unayambiranso kugunda. Pamenepo Elisa anaitana mayi ake a mwanayo ndi kuwauza mawu amene anasinthiratu kupwetekedwa mtima kwawo kukhala chimwemwe chodzaza tsaya. Elisa anawauza kuti: “Nyamula mwana wako.”​—Mavesi 34, 36.

Nkhani imeneyi, yokhudza kuukitsidwa kwa mwana wamwamuna wa mkazi wa ku Sunemu imatipatsa chiyembekezo ndiponso imatitonthoza. Yehova amadziwa bwino chisoni chimene makolo amakhala nacho mwana wawo akamwalira. Kuwonjezera apo, iye ndi wofunitsitsa kuukitsa akufa. (Yobu 14:14,15) Zimene Elisa ndi anthu ena otchulidwa m’Baibulo anachita poukitsa anthu akufa, zimatipatsa chitsanzo cha zimene Yehova adzachita kwa anthu ambiri m’dziko latsopano lolungama limene likubwera. *

Lonjezo la m’Baibulo la kuukitsidwa kwa akufa silithetseratu chisoni chachikulu chimene chimakhalapo chifukwa cha imfa ya wokondedwa wathu. Mkhristu wina wokhulupirika amene mwana wake anamwalira ananena kuti: “Mtima wanga sudzasiyiratu kundipweteka mpaka ndidzamuonenso mwana wanga.” Kungoganiza kuti mudzakhalanso pamodzi ndi okondedwa anu amene anamwalira kungathandize kuti chisoni chanu chichepeko. Kodi zimenezi sizikukulimbikitsani kuti mudziwe zambiri za Mulungu amene amatipatsa chiyembekezo cha mtengo wapatali chimenechi?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Kuti mudziwe zambiri zokhudza lonjezo la m’Baibulo lakuti akufa adzaukitsidwa, werengani chaputala 7 m’buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.