Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Masoka Achilengedwe Kodi Ndi Umboni Wakuti Mulungu Ndi Wankhanza?

Masoka Achilengedwe Kodi Ndi Umboni Wakuti Mulungu Ndi Wankhanza?

ZIMENE ANTHU ENA AMANENA: “Mulungu ndi amene akulamulira dzikoli ndipo ndi amene amachititsa masoka achilengedwe choncho iye ndi wankhanza.”

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Kodi pamenepa “woipayo” ndani? Baibulo limanena kuti ndi Satana. (Mateyu 13:19; Maliko 4:15) Taganizirani izi: Ngati Satana ndi amene akulamulira dzikoli, ndiye kuti iyeyo ndi amene amachititsa anthu kuti azikhala odzikonda, adyera komanso azichita zinthu mosaganizira zam’tsogolo. N’chifukwa chakenso anthu awononga kwambiri zachilengedwe padziko lapansili. Asayansi amati chifukwa chakuti anthu awononga kwambiri zachilengedwe, zachititsa kuti masoka achilengedwe azichitika pafupipafupi komanso kuti azikhala oopsa kwambiri.

Komano n’chiyani chinapangitsa Mulungu kulola kuti Satana azilamulira dzikoli? Chifukwa chakuti makolo athu oyambirira anakana kuti Mulungu aziwalamulira. Kuyambira nthawi imeneyo, anthu ambiri akhala akukana kuti Mulungu aziwalamulira. Zimenezi zachititsa kuti dzikoli likhale m’manja mwa Satana, yemwe ndi mdani wa Mulungu. Yesu ananena kuti Satana ndi “wolamulira wa dziko.” (Yohane 14:30) Koma n’zosangalatsa kuti Satana sadzalamulira mpaka kalekale.

Yehova * sasangalala akamaona anthu akuvutika chifukwa cha mavuto amene Satana amayambitsa. Ndipotu Yehova amamva chisoni akamaona anthu akuvutika. Mwachitsanzo, ponena za nthawi imene Aisiraeli ankavutika, Baibulo limanena kuti: “Pamene iwo anali kuvutika m’masautso awo onse, iyenso [Mulungu] anali kuvutika.” (Yesaya 63:9) Mulungu watichitira chifundo pokonza zoti posachedwapa awononge Satana. Ndipo wasankha Mwana wake, Yesu Khristu, kuti adzakhale Mfumu yolamulira mwachilungamo komanso kwamuyaya.

KODI NKHANI IMENEYI NDIYOFUNIKA BWANJI KWA INU? Satana walephera kuteteza anthu kuti asamavutike ndi masoka achilengedwe. Koma mu ulamuliro wa Yesu palibe amene azidzavutika ndi masoka achilengedwe. Nthawi ina Yesu anateteza ophunzira ake kuti asafe ndi mphepo yamphamvu. Baibulo limanena kuti: “Pamenepo . . . [Yesu anadzudzula] mphepoyo ndi kuuza nyanjayo kuti: ‘Leka! Khala bata!’ Chotero mphepoyo inaleka. Kenako panachita bata lalikulu.” Ndiyeno ophunzirawo ananena kuti: “Kodi ameneyu ndani kwenikweni, chifukwa ngakhale mphepo ndi nyanja zikumumvera?” (Maliko 4:37-41) Zimene Yesu anachitazi zimatsimikizira kuti iye akamadzalamulira adzateteza anthu onse omvera.—Danieli 7:13, 14.

^ ndime 5 Baibulo limanena kuti dzina la Mulungu ndi Yehova.