Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO: KODI TSANKHO LIDZATHA LITI?

Tsankho Likuchitika Padziko Lonse

Tsankho Likuchitika Padziko Lonse

JONATHAN, yemwe anabadwira ku America koma makolo ake ndi a ku Korea, anakula movutika chifukwa choti anthu ankamusala. Atakula anayamba kufufuza kumene angakakhale kopanda aliyense womusala chifukwa cha maonekedwe ake kapena chifukwa cha mtundu umene anabadwira. Kenako anayamba ntchito ya udokotala kumpoto kwa mzinda wa Alaska, ku America. Anasankha dala kukagwira ntchito kumeneko chifukwa anthu ambiri amene ankabwera pachipatalacho analinso ochokera ku Korea. Iye ankaganiza kuti palibe amene azikamusala kumeneko.

Koma tsiku lina anakhumudwa kwambiri pamene ankathandiza mayi wina wazaka 25 yemwe anakomoka. Mayiyo atatsitsimuka n’kuona kuti akumuthandizayo ndi munthu wa ku Korea, anakwiya komanso analankhula mawu achipongwe osonyeza kuti amadana ndi anthu a ku Korea. Jonathan anakhumudwa kwambiri chifukwa anazindikira kuti kulikonse komwe angapite, anthu azikamusalabe chifukwa cha mtundu wake.

N’zomvetsa chisoni kuti zimene zinachitikira Jonathan zikuchitikiranso anthu ambiri. Tsankho lafala  kwambiri ndipo zikuoneka kuti vutoli likuchitika kulikonse kumene kuli anthu.

Ngakhale kuti tsankho lafala kwambiri, anthu ambiri amadana nalo. Zimenezi zimachititsa anthu kudzifunsa kuti, n’chifukwa chiyani vutoli lafala kwambiri chonsecho anthu amadana nalo? Chifukwa chimodzi n’chakuti anthu ambiri amene amadana ndi tsankho sadziwa kuti iwonso ali nalo. Kodi ndi mmenenso inuyo mulili?

DZIFUFUZENI

Kaya tikudziwa kapena sitikudziwa, mfundo yosatsutsika ndi yakuti anthufe timazindikira mosavuta ngati munthu wina ali ndi tsankho koma zimativuta kuzidziwa eni akefe. Ndipotu Baibulo limati: “Mtima ndi wonyenga kwambiri kuposa china chilichonse.” (Yeremiya 17:9) N’chifukwa chake tikhoza kumadzinamiza kuti timagwirizana ndi aliyense komanso kuti tilibe tsankho. Ndiponso tingamadziikire kumbuyo kuti tili ndi chifukwa chomveka chosagwirizana ndi mtundu kapena gulu linalake la anthu.

Kodi Inuyo Mungaganize Zotani Mutakumana ndi Anthu Ngati Awa?

Kuti titsimikiziredi kuti n’zovuta kudziwa ngati tili ndi tsankho, tayerekezerani kuti mukuyenda mumsewu nokhanokha ndipo kuli kamdima. Kenako mukuona anyamata awiri, ooneka amphamvu, akubwera kutsogolo kwanu. Winayo akuoneka kuti wanyamula chinachake m’manja.

Kodi pamenepa munganene kuti anyamatawa ndi zigawenga ndipo akufuna kukuvulazani? N’kutheka kuti nthawi ina mutakumana ndi anthu ngati amenewa anakupangani chipongwe, ndipo zimenezo zinakuchititsani kuti nthawi zonse muzichita zinthu mosamala. Koma kodi chimenecho ndi chifukwa chonenera kuti anyamatawa akufuna kukuvulazani? Funso lina ndi lakuti, kodi mukuganiza kuti anyamatawa angakhale a mtundu uti? Zimene mungayankhe zingasonyeze ngati muli ndi tsankho kapena ayi.

Kuti tinene moona mtima, tonsefe tiyenera kuvomereza kuti tili ndi tsankho, kungoti timalionetsa m’njira zosiyanasiyana. Ngakhale Baibulo limasonyeza kuti tonsefe tili ndi tsankho chifukwa limati: “Munthu amaona zooneka ndi maso.” (1 Samueli 16:7) Kunena zoona, tonsefe nthawi zina timapanga zinthu zina mwatsankho ndipo kawirikawiri zimenezi zimabweretsa mavuto aakulu. Komano kodi n’zotheka kupewa kapena kuthetseratu mtima wa tsankho? Kodi zidzatheka kuthetseratu tsankho padziko lonse?