Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MAWU A MULUNGU AMATI CHIYANI PA NKHANI YA KUSUTA FODYA?

Kodi Mawu a Mulungu Amati Chiyani pa Nkhani ya Kusuta Fodya?

Kodi Mawu a Mulungu Amati Chiyani pa Nkhani ya Kusuta Fodya?

Naoko, amene tamutchula m’nkhani yoyamba ija, anafotokoza zomwe zinamuthandiza kuti asiye kusuta fodya. Iye anati: “Ndinasiya kusuta chifukwa cha zimene ndinaphunzira zokhudza makhalidwe a Mulungu komanso cholinga chake.” Zimene Naoko anaphunzira zimapezeka m’Baibulo. Ngakhale kuti m’Baibulo mulibe mawu akuti fodya, limatithandiza kumvetsa mmene Mulungu amaonera nkhani ya kusuta fodya. * Anthu ambiri akadziwa zimenezo, zimawathandiza kuti asayambe kusuta fodya kapenanso kuti asiye, ngati amasuta. (2 Timoteyo 3:16, 17) Tiyeni tione mavuto odziwika bwino atatu amene amabwera chifukwa cha kusuta fodya. Tionanso zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi.

MUNTHU AKAYAMBA KUSUTA AMAVUTIKA KUTI ASIYE

Mu fodya muli tinthu tinatake totchedwa nikotini, timene timapangitsa kuti munthu akayamba kusuta, azivutika kuti asiye. Tinthu timeneti timachititsa kuti munthu wosuta azikhala wogalamuka. Komanso nthawi zina tinthu timeneti tikhoza kupangitsa munthu kuti asamade nkhawa ndiponso kuti agone bwino. Kusuta kumapangitsa kuti tinthu timeneti tifike mofulumira ku ubongo ndipo zimenezi zimachitika kambirimbiri. Popeza nthawi iliyonse imene munthu wakoka ndudu amalowetsa nikotini m’mapapo ake, munthu amene amasuta ngakhale paketi imodzi pa tsiku, amalowetsa nikotini wambiri koposa amene munthu yemwe amagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo amalowetsa m’thupi lake. Zimenezi n’zimene zimapangitsa kuti munthu azilephera kusiya kusuta fodya. Munthu amene ali ndi chizolowezi chosuta amakhala ndi chibaba, ndipo ngati sanasute, samva bwino. Choncho amasuta kuti athetse mavuto amenewo.

“Kodi simukudziwa kuti ngati mudziperekabe kwa winawake monga akapolo kuti muzimumvera, mumakhala akapolo ake?”—Aroma 6:16

Kodi mungathedi kumvera Mulungu ngati muli akapolo a fodya?

Baibulo limatithandiza kuti tiziona moyenera nkhani imeneyi. Limati: “Kodi simukudziwa kuti ngati mudziperekabe kwa winawake monga akapolo kuti muzimumvera, mumakhala akapolo ake chifukwa chakuti mumamumvera?” (Aroma 6:16) Ngati chibaba cha fodya chikuchititsa munthu kuti aziganiza kapena kuchita zinthu mwa njira inayake, ndiye kuti munthuyo ndi kapolo wa khalidwe lakelo. Koma Yehova Mulungu amafuna kuti timasuke ku makhalidwe amene amawononga thupi komanso maganizo athu. (Salimo 83:18; 2 Akorinto 7:1) Choncho munthu akayamba kumvetsa zimene Yehova amafuna kuti tizichita komanso akamafuna kumulemekeza, amazindikira kuti iye ndi woyenera kumutumikira ndi mtima wonse. Amazindikiranso kuti sangathe kuchita zimenezi ngati akukhalabe kapolo wa khalidwe loipa. Zimenezi zimathandiza munthuyo kuti ayambe kufunitsitsa kusiya kusuta fodya.

Olaf, yemwe amakhala ku Germany, anayamba kusuta fodya ali ndi zaka 12 ndipo anasuta kwa zaka 16. Iye anayamba kusuta ngati masewera. Koma kenako chinakhala chizolowezi, moti ankaganiza kuti sangathe kusiya. Iye anati: “Tsiku lina fodya atandithera, ndinavutika kwambiri. Ndinapita mmene ndinkatayamo zotsalira, n’kutenga zotsalira za fodya amene ndinasuta kale ndipo ndinazipanga ndudu pogwiritsa ntchito nyuzipepala. Ndikaganizira zimene ndinachitazi, ndimadzimvera chisoni kwambiri.” Komabe Olaf anakwanitsa kusiya kusuta. Kodi chinamuthandiza n’chiyani?  Iye anati: “Chimene chinandithandiza kwambiri ndi mtima wofuna kusangalatsa Yehova. Kuganizira chikondi cha Yehova pa anthu komanso zimene walonjeza kudzachita m’tsogolo, kunandithandiza kuti ndisiye kusuta fodya.”

KUSUTA KUMAWONONGA MOYO

Buku lina linanena kuti: “Akatswiri anapeza kuti kusuta fodya . . . kumawononga pafupifupi chiwalo chilichonse cha thupi. Komanso kumawonjezera chiwerengero cha odwala ndi omwalira.” (The Tobacco Atlas) Anthu ambiri amadziwa kuti kusuta kumayambitsa matenda osapatsirana monga khansa, matenda a mtima komanso matenda a m’mapapo. Koma malinga ndi zimene Bungwe Loona za Umoyo Padziko Lonse linanena, kusuta kumayambitsanso matenda opatsirana monga TB amene amapha anthu ambiri.

“Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.”—Mateyu 22:37

Ngati mukuwononga thupi lanu posuta fodya, kodi tingati mumakonda Yehova komanso kumuyamikira?

Kudzera m’Mawu ake, Baibulo, Yehova Mulungu amatiphunzitsa kuti tiziona zoti moyo wathu, thupi lathu komanso luso lathu loganiza, ndi zinthu zofunika kwambiri. Mwana wake, Yesu, anatsindika mfundo imeneyi pamene ananena kuti: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.” (Mateyu 22:37) Apatu n’zoonekeratu kuti Mulungu amafuna kuti tizigwiritsa ntchito bwino moyo ndi thupi lathu, ndipo tisamachite zinthu zomwe zingatiwononge. Tikaphunzira za Yehova komanso zomwe walonjeza, timayamba kukonda moyo wathu komanso kuona kuti zinthu zonse zimene anatipatsa ndi za mtengo wapatali. Zimenezi zimatithandiza kupewa chilichonse chimene chingawononge thupi lathu.

Dokotala wina wa ku India, dzina lake Jayavanth, ankasuta fodya ndipo anachita zimenezi kwa zaka 38. Iye anati: “Ndinawerenga magazini osiyanasiyana a zaumoyo ndipo ndinazindikira kuopsa kwa kusuta fodya. Ndinkadziwa kuti kusuta n’koipa ndipo ndinkalangiza odwala kuti asiye kusuta. Koma ineyo zinkandikanika kusiya ngakhale kuti ndinayesapo maulendo angapo.” Koma kenako Jayavanth anasiya kusuta fodya. Kodi chinamuthandiza n’chiyani? Iye anati: “Nditayamba kuphunzira Baibulo, ndinasiya kusuta. Mtima wofuna kusangalatsa Yehova ndi umene unachititsa kuti nditsimikize zofuna kusiya kusuta, ndipo ndinasiyadi.”

KUSUTA KUMAWONONGANSO MOYO WA ANTHU ENA

Utsi umene umatuluka pandudu yoyatsa komanso umene munthu amatulutsa akamasuta fodya, ndi woipa kwambiri. Munthu wina akapuma utsi umenewu akhoza kudwala khansa kapena matenda ena. Chaka chilichonse utsi oterewu umapha anthu 600,000, ndipo ambiri mwa anthuwa amakhala amayi ndi ana. Lipoti lina la Bungwe Loona  za Umoyo Padziko Lonse linati: “Ngakhale munthu atapuma utsi umenewu wochepa kwambiri, zotsatira zake zimakhalabe zoipa.”

“Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.”—Mateyu 22:39

Kodi tingati mumakondadi anthu a m’banja lanu komanso anthu ena, ngati mumasuta fodya iwowo n’kumapuma utsi wa fodyawo?

Yesu ananena kuti lamulo lachiwiri ndi loti: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.” (Mateyu 22:39) Palembali, mawu akuti “mnzako” akutanthauza anthu a m’banja lathu, anzathu komanso anthu omwe tili nawo pafupi. Choncho ngati timachita khalidwe linalake lomwe lingawononge moyo wa anthu amenewa, ndiye kuti tikusonyeza kuti sitiwakonda. Chikondi chenicheni chimatithandiza kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Aliyense asamangodzifunira zopindulitsa iye yekha basi, koma zopindulitsanso wina.”—1 Akorinto 10:24.

Armen, yemwe amakhala ku Armenia, ananena kuti: “Mkazi ndi ana anga ankandipempha kuti ndisiye kusuta chifukwa kunkawabweretsera mavuto. Koma ine ndinkakana kuvomereza kuti khalidwe langa losuta limakhudzanso iwowo.” Kenako Armen anavomereza kuti mkazi ndi ana ake ankanena zoona, ndipo anafotokoza zomwe zinamuchititsa kusintha maganizo ake. Iye anati: “Kudziwa zimene Baibulo limanena komanso kukonda Yehova, n’kumene kunandithandiza kuti ndisiye kusuta. Kunandithandizanso kuvomereza kuti khalidwe langa silinkawononga moyo wanga wokha, koma linkawononganso moyo wa ena.”

KUSUTA KUDZATHA

Zimene Baibulo limanena zinathandiza Olaf, Jayavanth komanso Armen kuti asiye kusuta fodya. Chimene chinawathandiza si kungodziwa kuti kusuta n’koipa. Koma n’chifukwa choti anayamba kukonda Yehova ndipo ankafunitsitsa kuchita zimene iye amafuna. Kufunika kwa chikondi chimenechi kwafotokozedwa bwino pa 1 Yohane 5:3. Vesili limati: “Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake, ndipo malamulo akewo ndi osalemetsa.” N’zoona kuti kutsatira mfundo za m’Baibulo sikophweka, koma ngati munthu amakonda kwambiri Mulungu, amaona kuti kumumvera si kolemetsa.

Kudzera m’ntchito yophunzitsa anthu yomwe ikuchitika padziko lonse, Yehova Mulungu akuthandiza anthu kuti asiye kusuta fodya n’cholinga choti asakhale akapolo a khalidweli. (1 Timoteyo 2:3, 4) Posachedwapa, Mulungu adzachotsa maboma komanso makampani onse omwe amalimbikitsa anthu kuti azisuta fodya, ngakhale akudziwa kuti fodya ndi woipa. Iye adzachita zimenezi pogwiritsa ntchito Ufumu wake wakumwamba, womwe wolamulira wake ndi Yesu Khristu. Zimenezi zidzathandiza kuti pasadzakhalenso anthu osuta fodya, chifukwa anthu onse amene adzatsale m’dzikoli ndi okhawo amene amamvera Mulungu. Iye adzathandizanso anthu amenewa kuti akhale angwiro.—Yesaya 33:24; Chivumbulutso 19:11, 15.

Ngati mukuyesetsa kuti musiye kusuta fodya, musataye mtima. Phunzirani kukonda Yehova ndipo yesetsani kuona kusuta fodya mmene Yehova amakuonera. Zimenezi zingakuthandizeni kuti nanunso musiye kusuta fodya. A Mboni za Yehova angakuthandizeni kuphunzira Baibulo komanso kudziwa zimene mungachite kuti muzigwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulozo pa moyo wanu kuti musiye kusuta. Dziwani kuti ngati mukufuna kuti Yehova akuthandizeni kuti musiye kusuta fodya, iye adzakuthandizani.—Afilipi 4:13.

^ ndime 3 M’nkhaniyi mawu akuti kusuta, akunena za kulowetsa utsi wa fodya m’mapapo kudzera mu ndudu, fodya wopichira, kaliwo komanso kugwiritsa ntchito chipangizo chimene chimachititsa kuti utsi wa fodya uzidutsa m’madzi, usanalowe m’thupi. Komabe mfundo zomwe zili m’nkhaniyi zikukhudzanso fodya wotafuna, wofwenkha ndi wina wotero.