Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI ANTHU AMENE ANAMWALIRA ADZAKHALANSO NDI MOYO?

Tingatsimikize Bwanji Kuti Amene Anamwalira Adzakhalanso Ndi Moyo?

Tingatsimikize Bwanji Kuti Amene Anamwalira Adzakhalanso Ndi Moyo?

Kodi kukhulupirira kuti akufa adzakhalanso ndi moyo ndi kungolimbikira mtunda wopanda madzi? Tiyeni tione zimene Paulo ankakhulupirira pa nkhaniyi. Iye analemba kuti: “Ngati tayembekezera Khristu m’moyo uno wokha, ndiye kuti ndife omvetsa chisoni kuposa anthu ena onse. Komabe, Khristu anaukitsidwa kwa akufa, n’kukhala chipatso choyambirira cha amene akugona mu imfa.” (1 Akorinto 15:19, 20) Uwu ndi umboni wakuti Paulo ankaona kuti nkhani yakuti akufa adzakhalanso ndi moyo si nkhambakamwa chabe. Ndipotu kuukitsidwa kwa Yesu n’kumene kunamuthandiza kuti asamakayikire zakuti anthu amene anamwalira adzakhalanso ndi moyo. * (Machitidwe 17:31) N’chifukwa chake Paulo ananena kuti Yesu ndi “chipatso choyambirira,” kutanthauza kuti anali munthu woyamba kupatsidwa moyo wosatha pambuyo poukitsidwa. Choncho ngati Yesu anali woyamba ndiye kuti anthu enanso anayenera kudzalandira moyo woterewu.

Yobu anauza Mulungu kuti: “Mudzalakalaka ntchito ya manja anu.”—Yobu 14:14, 15

Tiyeni tione umboni wina wosonyeza kuti anthu amene anamwalira adzakhalanso ndi moyo. Baibulo limasonyeza kuti Yehova ndi Mulungu amene amanena zoona ndipo limati: “Mulungu . . . sanganame.” (Tito 1:2) Yehova sanayambe wanamapo ndipo sanganame ngakhale zitavuta bwanji. Iye sangangolonjeza kuti akufa adzakhalanso ndi moyo koma akudziwa kuti akunama. Zimenezi sizingachitike ngakhale pang’ono.

Chikondi n’chimene chinachititsa kuti Yehova akonze zoti anthu amene anamwalira adzakhalenso ndi moyo. Yobu anafunsa kuti: “Munthu akafa, kodi angakhalenso ndi moyo? . . . Inu mudzaitana ndipo ine ndidzayankha. Mudzalakalaka ntchito ya manja anu.” (Yobu 14:14, 15) Yobu sankakayikira kuti ngakhale atamwalira, Atate wake wachikondi adzalakalaka kumuukitsa. Kodi Mulungu anasintha? Iye anati: “Ine ndine Yehova, sindinasinthe.” (Malaki 3:6) Mulungu amalakalakabe kuti adzaukitse anthu amene anamwalira n’cholinga choti adzasangalale ndi moyo wathanzi. Izi ndi zimene kholo lachikondi limene mwana wake wamwalira limalakalaka. Koma kholo lingasiyane ndi Mulungu chifukwa iye ali ndi mphamvu zochitira chilichonse chimene akufuna.—Salimo 135:6.

Ngakhale kuti imfa ndi yowawa, Mulungu adzaithetsa

Yehova adzapatsa Mwana wake mphamvu zoukitsa anthu amene anamwalira ndipo zimenezi zidzachititsa kuti achibale awo adzakhale ndi chimwemwe chodzaza tsaya. Kodi Yesu amamva bwanji akamaganizira kuti adzaukitsa anthu omwe anamwalira? Asanaukitse Lazaro, Yesu anakhudzidwa ndi chisoni chimene achemwali ake a Lazaro ndi anzake anali nacho ndipo nayenso “anagwetsa misozi.” (Yohane 11:35) Nthawi inanso Yesu anakumana ndi mayi amasiye a ku Naini amene mwana wawo anamwalira. Mayiwa anali ndi mwana mmodzi yekha ndipo Yesu “anawamvera chifundo, choncho anawauza kuti: ‘Tontholani mayi.’” Nthawi yomweyo anaukitsa mwanayo. (Luka 7:13) Uwu ndi umboni wakuti Yesu samasangalala ndi imfa ndipo amakhudzidwa kwambiri akamaona kuti anthu ali ndi chisoni. Choncho adzasangalala kwambiri akamadzaukitsa anthu amene anamwalira n’kuona abale awo akusangalala.

Kodi muli ndi chisoni chifukwa cha imfa ya achibale anu? Mwina mumaganiza kuti achibale anuwo simudzawaonanso. Komatu mudzawaonanso chifukwa Yehova adzagwiritsa ntchito Mwana wake kuukitsa anthu amene anamwalira. Yehova akufuna kuti mudzadzionere nokha mmene zimenezi zidzachitikire. Iye akufuna kuti mudzalandire achibale anu pa nthawi imene azidzaukitsidwa. Imeneyitu idzakhala nthawi yosangalatsa chifukwa tidzachitira zinthu limodzi ndi achibale athu mpaka kalekale popanda kuganizira kuti tsiku linalake wina akhoza kumwalira.

Lionel, yemwe watchulidwa m’nkhani yoyambirira uja anati: “Kenako ndinaphunzira kuti akufa adzakhalanso ndi moyo. Poyamba zinali zovuta kukhulupirira ndipo ndinkaona ngati munthu amene ankandiuzayo ankandinamiza. Koma nditawerenga m’Baibulo ndinaona kuti n’zoona. Ndikuona kuchedwa kuti nthawiyi idzafike kuti ndidzaonanenso ndi agogo anga.”

Kodi mukufuna kudziwa zambiri? A Mboni za Yehova angasangalale kukusonyezani m’Baibulo lanu umboni wosonyeza kuti anthu amene anamwalira adzakhalanso ndi moyo. *

^ ndime 3 Kuti mupeze umboni woti Yesu anaukitsidwadi, werengani buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? tsamba 78-86, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 9 Ngati mukufuna kudziwa zambiri, werengani buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? mutu 7. Bukuli ndi lofalitsidwa ndi a Mboni za Yehova ndipo