Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Anna Moneymaker/Getty Images

KHALANI MASO

Asayansi Asunthira Kutsogolo Wotchi Yosonyeza Nthawi ya Kutha kwa Dziko—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Asayansi Asunthira Kutsogolo Wotchi Yosonyeza Nthawi ya Kutha kwa Dziko—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

 Pa 24 January 2023, asayansi anasunthira kutsogolo muvi wa wotchi yongoyerekezera yosonyeza nthawi yakutha kwa dziko a kuti iyandikire 12 koloko ya usiku zomwe akuti zikuimira kutha kwa dziko.

  •   “‘Wotchi yongoyerekezera yosonyeza nthawi yakutha kwa dziko’ yomwe ikuimira zinthu zoopsa zimene anthu akukumana nazo, anaisunthira kwambiri kutsogolo Lachiwiri pa 24 January 2023 kuti iyandikire 12 koloko ya usiku chifukwa cha mavuto monga nkhondo ya ku Ukraine, nkhawa zimene anthu ali nazo kuti mabomba a nyukiliya akhoza kuphulitsidwa komanso mavuto obwera chifukwa cha kusintha kwa nyengo.”​—AFP International Text Wire.

  •   “Asayansi ananena kuti Lachiwiri muvi wa ‘wotchi yongoyerekezera yosonyeza nthawi yakutha kwa dziko’ anausunthira kutsogolo ndi masekondi 90 nthawi isanakwane 12 koloko usiku kusonyeza kuti dzikoli latsala pang’ono kuti liwonongekeretu.”​—ABC News.

  •   “Akatswiri asayansi achenjeza kuti moyo wa anthu uli pa chiopsezo chachikulu kwambiri kuposa kale lonse.”​—The Guardian.

 Kodi dziko lapansili ndi anthu zithadi posachedwapa? Kodi tikuyenera kuopa zimene zidzachitike m’tsogolo? Kodi Baibulo limanena zotani?

Zimene zidzachitike m’tsogolo

 Mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena, “dziko lapansi lidzakhalapobe mpaka kalekale” ndipo anthu “adzakhala mmenemo kwamuyaya.” (Mlaliki 1:4; Salimo 37:29) Zimenezi zikusonyeza kuti anthu sadzawononga dzikoli kapena kulipangitsa kuti zamoyo zisapezekemo.

 Komabe, Baibulo limanena za mapeto. Mwachitsanzo, limanena kuti “dziko likupita.”​—1 Yohane 2:17.

Khalanibe oganiza bwino

 Kodi Baibulo lingatithandize bwanji kuti tikhalebe oganiza bwino ngakhale kuti tikukumana ndi mavuto?

 Kuti muzipindula kwambiri ndi zimene Baibulo limaphunzitsa, tikukupemphani kuti muziphunzira Baibulo mwaulere mothandizidwa ndi wa Mboni za Yehova.

a “Wotchi yongoyerekezera yosonyeza nthawi yakutha kwa dziko inakonzedwa kuti izichenjeza anthu za kufupika kwa nthawi yoti dzikoli lithe chifukwa cha zida zoopsa zamakono zimene anthu akupanga. Limeneli ndi chenjezo lothandiza anthu kudziwa kuti akuyenera kupeza njira zothetsera mavuto n’cholinga choti dzikoli lisathe.”​—Bulletin of the Atomic Scientists.