Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zolemba Zakale Zimatsimikizira za Malo Amene Aisiraeli Ankakhala

Zolemba Zakale Zimatsimikizira za Malo Amene Aisiraeli Ankakhala

Baibulo limanena kuti Aisiraeli atalanda Dziko Lolonjezedwa n’kuligawa mogwirizana ndi mafuko awo, mabanja 10 a fuko la Manase anatenga magawo a kumadzulo kwa Yorodano, komwe kunali kosiyana ndi magawo a mafuko ena onse. (Yoswa 17:1-6) Kodi pali umboni uliwonse wochokera kwa akatswiri ofukula zinthu zakale wosonyeza kuti n’zimene zinachitikadi?

Mu 1910, ku Samariya kunapezeka zidutswa za mapale zomwe panalembedwa mawu. Pamapalewa, panali zolemba za m’Chiheberi zokhudza katundu wodula, kuphatikizapo vinyo ndi mafuta odzola zomwe zinkapita kunyumba yachifumu yomwe inali kulikulu la mzindawo. Mapale onse amene anapezeka analipo 102 ndipo analembedwa cha m’ma 700 B.C.E. Koma ndi mapale 63 okha amene mawu ake amawerengeka bwinobwino. Ngakhale zili choncho, mapale 63 amenewa akaikidwa pamodzi amasonyeza madeti ndi mayina a mabanja a anthu, komanso zinthu zina zokhudza anthu omwe ankatumiza malonda komanso kulandira katundu.

Chochititsa chidwi n’chakuti mabanja onse omwe analembedwa pamapale a ku Samariyawa ndi a fuko la Manase lokha basi. Buku lina limanena kuti zimene zili pa mapalewa “ndi umboni wakuti zimene Baibulo linanena zokhudza mafuko a Manase komanso dera lomwe ankakhala ndi zolondola.”—NIV Archaeological Study Bible.

Phaleli likusonyeza dzina la mayi wina wotchedwa Nowa yemwe anali wa m’banja la Manase

Mapale a ku Samariya amatitsimikiziranso kuti zimene Amosi analemba zokhudza anthu olemera a pa nthawiyo zinali zoona. Iye ananena kuti: “Inu mukumwera vinyo m’makapu akuluakulu ndipo mukudzola mafuta apamwamba kwambiri.” (Amosi 6:1, 6) Mapale a ku Samariya amasonyeza umboni wakuti zinthu zomwe zatchulidwa palembali zinkatumizidwadi ku gawo limene mabanja 10 a fuko la Manase ankakhala.