Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 107

Tizitsanzira Chikondi cha Mulungu

Tizitsanzira Chikondi cha Mulungu

(1 Yohane 4:19)

  1. 1. Yehova M’lungu n’chitsanzo chabwino,

    Inde cha chikondi.

    Zochita zake zimatithandiza

    Kuti tizimutsanzira.

    Anatipatsa mwana wake Yesu

    Kuti tikhululukidwe zolakwa.

    Ndi umbonidi wa chikondi chake.

    M’lungu wathu ndi chikondidi.

  2. 2. Timasonyeza chikondi choona

    Potsanzira M’lungu.

    Abale onse timawathandiza

    Mosasankha aliyense.

    Chikondi chingakhale chenicheni

    Ngati timakonda M’lungu ndi anthu.

    Tizikwirira zolakwa za ena,

    Chimenechi ndicho chikondi.

  3. 3. Chikondi chathu chimatithandiza

    Kumagwirizana.

    Atate wathu akufuna kuti

    Tidzalawe mgwirizano.

    Timapeza chikondi chenicheni

    Ndipo n’chomwe chimatidziwikitsa.

    Abale athu amatikumbutsa

    Za chikondi cha M’lungu wathu.