Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 144

Mukhulupirikebe

Mukhulupirikebe

(2 Akorinto 4:​18)

  1. 1. Pomwe osaona aona,

    Ovutika kumva akumva,

    Ana akuimbatu nyimbo,

    Mtendere padziko lonse.

    Pomwe akufa akuuka,

    Uchimo ndi mavuto zatha.

    (KOLASI)

    Mudzaona zinthu zonsezi,

    Mukakhulupirikabe.

  2. 2. Mimbulu ikudya ndi nkhosa,

    Mikango ikudya ndi ng’ombe,

    Mwana akuzitsogolera,

    Zikumvera mawu ake.

    Pomwe misozi yonse yatha,

    Mantha ndi zopweteka zatha.

    (KOLASI)

    Mudzaona zinthu zonsezi,

    Mukakhulupirikabe.