Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 149

Tiimbire Yehova Chifukwa Wapambana

Tiimbire Yehova Chifukwa Wapambana

(Ekisodo 15:1)

  1. 1. Timuimbire Yehova M’lungu wokwezeka.

    Waponya Aiguputo onyada m’nyanja.

    Mutamandeni

    Palibenso Mulungu wina.

    Yehova ndi dzina lake,

    Wapambanadi.

    (KOLASI)

    Yehova ndinu wokwezeka.

    Simunasinthe ndinudi Mfumu.

    Mudzagonjetsa adani onse

    N’kuyeretsa dzina lanu.

  2. 2. Mitundu yonse

    ikutsutsana ndi Yehova.

    Ichita manyazi Ngakhale

    ndi yamphamvu.

    Iwonongedwa Singathawe

    Aramagedo.

    Idzadziwa kuti Mulungu ndi Yehova.

    (KOLASI)

    Yehova ndinu wokwezeka.

    Simunasinthe ndinudi Mfumu.

    Mudzagonjetsa adani onse

    N’kuyeretsa dzina lanu.