Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 19

Chakudya Chamadzulo cha Ambuye

Chakudya Chamadzulo cha Ambuye

(Mateyu 26:​26-​30)

  1. 1. Yehova M’lungu wakumwamba,

    Lerotu ndi lapadera.

    Kale patsikuli munatisonyeza

    Chikondi, nzeru ndi mphamvu.

    Magazi a mwana wankhosa

    Anapulumutsa anthu,

    Kenako Yesu anakhetsa magazi

    Kukwaniritsa ulosiwu.

  2. 2. Tikuona mkate ndi vinyo

    Zomwe zikutikumbutsa

    Kufunika kwa Nsembe ya

    Yesu Khristu.

    Ndi mphatso yapaderadi.

    Madzulo ano tiyenera

    Kuchita chikumbutsochi

    Pokumbukira

    Zomwe zinachitika

    Kuti dipo liperekedwe.

  3. 3. Tasonkhana pamaso panu.

    Tamva kuitana kwanu.

    Titamande inu

    Ndi Mwana wanunso.

    Munatikonda kwambiri.

    Mwambowu ndi wolimbitsadi

    Chikhulupiriro chathu.

    Tiyendebe motsatira Yesu Khristu

    Ndipo tidzapezadi moyo.