Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 26

“Munachitiranso Ine”

“Munachitiranso Ine”

(Mateyu 25:​34-​40)

  1. 1. Yesu alitu ndi nkhosa zina ndipo

    Zimatumikira ndi odzozedwa.

    Zimene nkhosazo

    Zingawachitire,

    Yesu adzawabwezera zomwezo.

    (KOLASI)

    ‘Mwakuwathandiza, mwandithandiza.

    Zonse zimene munawachitira

    Munachitiranso ine amene.

    Zonse zomwe munawachitira

    Munachitiranso ine amene.’

  2. 2. Pamene ndinali wanjala ndi ludzu

    Munandithandiza mwamsanga ndithu.

    ‘Mbuye, tinachita

    Liti zimenezi?’

    Ndiye Mfumuyo idzayankha kuti:

    (KOLASI)

    ‘Mwakuwathandiza, mwandithandiza.

    Zonse zimene munawachitira

    Munachitiranso ine amene.

    Zonse zomwe munawachitira

    Munachitiranso ine amene.’

  3. 3. Mwakhulupirika pochita zabwino,

    Polalikira ndi abale anga.

    Choncho Mfumuyo

    Idzauza nkhosazo:

    ‘Landirani dziko, moyo wosatha.’

    (KOLASI)

    ‘Mwakuwathandiza, mwandithandiza.

    Zonse zimene munawachitira

    Munachitiranso ine amene.

    Zonse zomwe munawachitira

    Munachitiranso ine amene.’