Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 29

Tizichita Zinthu Zogwirizana Ndi Dzina Lathu

Tizichita Zinthu Zogwirizana Ndi Dzina Lathu

(Yesaya 43:​10-12)

  1. 1. Yehova Mulungu wamphamvuyonse,

    Wachilungamo ndi wachikondi,

    Mwini choonadi komanso nzeru,

    Mukulamulira monga Mfumu.

    Timasangalala potumikira

    Ndi polengeza Ufumu wanu.

    (KOLASI)

    Tiyesetse kuchita zinthu zomwe

    N’zogwirizana ndi dzina lathu.

  2. 2. Tikamatumikira ndi abale

    Timakhaladi ogwirizana.

    Tikaphunzitsa anthu choonadi,

    Dzina lanu limatamandidwa.

    Ndife odziwika ndi dzina lanu,

    Tipitiriza kulitchukitsa.

    (KOLASI)

    Tiyesetse kuchita zinthu zomwe

    N’zogwirizana ndi dzina lathu.