Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 40

Kodi Ndife A Ndani?

Kodi Ndife A Ndani?

(Aroma 14:8)

  1. 1. Iwe ndi wandani?

    Umvera m’lungu uti?

    Amene umamulambira

    Iye ndiye m’lungu wako.

    Milungu iwiri

    Sungaitumikire.

    Sungalambire iwiri yonse

    Sankhapo mmodzi yekha.

  2. 2. Iwe ndi wandani?

    Umvera m’lungu uti?

    Zili ndi iweyo kusankha

    Woona kaya wonama.

    Kodi Kaisara

    Udakamukondabe?

    Kapena udzamvera Yehova

    Ndikumutumikira?

  3. 3. Ine ndi wandani?

    Ndidzamvera Yehova.

    Ndikufuna kusangalatsa

    Atate wanga kumwamba.

    Anandigulatu.

    Ndidzamutumikira.

    Ndizimulambira iye yekha

    Ndi kumulemekeza.