Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 54

“Njira Ndi Iyi”

“Njira Ndi Iyi”

(Yesaya 30:​20, 21)

  1. 1. Pali njira imene

    Munaidziwa.

    Munaphunzira za

    Njira ya mtendere

    Pamene munamvera

    Mawu a Yesu.

    Ndi njira yopezeka

    M’mawu a M’lungu.

    (KOLASI)

    Njira yakumoyo ndi yomweyi.

    Musachoke kupita kumbali.

    Mawu a Mulungu akuti

    Musachoke njira ndi yomweyi.

  2. 2. Pali njira imene

    Ndi yachikondi.

    Tikaitsatira

    Timaona kuti

    Chikondi cha Mulungu

    Ndi chochuluka.

    Nafenso tiyesetse

    Kukonda ena.

    (KOLASI)

    Njira yakumoyo ndi yomweyi.

    Musachoke kupita kumbali.

    Mawu a Mulungu akuti

    Musachoke njira ndi yomweyi.

  3. 3. Pali njira ya moyo

    Imodzi yokha.

    Palibe inanso,

    M’lungu walonjeza.

    Ndi yokhayi

    Tingapezemo chikondi.

    Njira yakumoyotu

    Ndi imeneyi.

    (KOLASI)

    Njira yakumoyo ndi yomweyi.

    Musachoke kupita kumbali.

    Mawu a Mulungu akuti

    Musachoke njira ndi yomweyi.