Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 62

Nyimbo Yatsopano

Nyimbo Yatsopano

(Salimo 98)

  1. 1. Imbira M’lungu, imba nyimbo yatsopano.

    Unene kwa onse ntchito zake zonse.

    Umutamande, Mulungu ndi wopambana.

    Ndi wachilungamo

    Poweruza anthu.

    (KOLASI)

    Imbani

    Nyimbo yatsopano.

    Imbani,

    Yehova ndi Mfumu.

  2. 2. Mosangalala fuula kwa Mfumu yathu.

    Muzimutamanda ndi nyimbo yokoma.

    Tiyeni tonse timuimbire mokweza.

    Zeze ndi lipenga

    Ziimbe pamodzi.

    (KOLASI)

    Imbani

    Nyimbo yatsopano.

    Imbani,

    Yehova ndi Mfumu.

  3. 3. Nyanja ndi zonse mmenemo zimutamande.

    Zolengedwa zake zizimutamanda.

    Dziko lapansi nalonso limutamande.

    Mapiri ndi zigwa

    Zimutamandenso.

    (KOLASI)

    Imbani

    Nyimbo yatsopano.

    Imbani,

    Yehova ndi Mfumu.