Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 74

Tiimbile Limodzi Nyimbo ya Ufumu

Tiimbile Limodzi Nyimbo ya Ufumu

(Salimo 98:1)

  1. 1. Iyi ndi nyimbo yachisangalalo

    Yolemekeza M’lungu wamkulu.

    Imatipatsadi chiyembekezo.

    Imbani nafe nyimbo yathuyi.

    (KOLASI)

    Lambirani M’lungu wathu.

    Mwana wake ndiye Mfumu.

    Dzaphunzireni nyimbo ya Ufumu.

    Tamandani dzina la Mulungu.

  2. 2. Nyimboyi ikulengeza Ufumu.

    Yesu Khristu ndi wolamulira

    Ndipo mtundu watsopano wabadwa,

    Nawo ukumusangalalira.

    (KOLASI)

    Lambirani M’lungu wathu.

    Mwana wake ndiye Mfumu.

    Dzaphunzireni nyimbo ya Ufumu.

    Tamandani dzina la Mulungu.

  3. 3. Amene angaphunzire nyimboyi

    Ndi amene amadzichepetsa.

    Ambiri m’dzikoli aiphunzira

    Ndipo akuphunzitsanso ena.

    (KOLASI)

    Lambirani M’lungu wathu.

    Mwana wake ndiye Mfumu.

    Dzaphunzireni nyimbo ya Ufumu.

    Tamandani dzina la Mulungu.