Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 81

Moyo wa Mpainiya

Moyo wa Mpainiya

(Mlaliki 11:6)

  1. 1. Tsiku likayamba, tulo tikukoma

    Timadzuka kupita

    Kolalikira uthenga

    Ndipo Mulungu amatitsogolera.

    Timasangalala

    Anthu akamatimvetsera.

    (KOLASI)

    Tinasankha

    Kutumikira Yehova.

    Timachita zofuna zake.

    Tipitilizabe kulalikiraku.

    Tikatero timasonyeza

    Chikondi.

  2. 2. Pofika madzulo timatopa ndithu

    Komabe timapeza

    Chimwemwe potumikira.

    Yehova Mulungu amatidalitsa.

    Nthawi zonse

    Timamuthokoza potithandiza.

    (KOLASI)

    Tinasankha

    Kutumikira Yehova.

    Timachita zofuna zake.

    Tipitilizabe kulalikiraku.

    Tikatero timasonyeza

    Chikondi.