Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 85

Tizilandilana

Tizilandilana

(Aroma 15:7)

  1. 1. Takulandirani inu nonse.

    Mwasonkhana kudzaphunzira

    Choonadi chochoka kwa M’lungu.

    Iye akaitana timavomera.

  2. 2. Tikuyamikira abalewa

    Chifukwa amatilandira.

    Tiziwasonyezatu chikondi.

    Tilandirenso ena odzasonkhana.

  3. 3. Aliyense akuitanidwa

    Kuti apeze choonadi.

    M’lungu watikokera kwa iye

    Choncho tilandirane ndi mtima wonse.