Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 98

Malemba Anauziridwa Ndi Mulungu

Malemba Anauziridwa Ndi Mulungu

(2 Timoteyo 3:​16, 17)

  1. 1. Mawu a M’lungu ndi nyale,

    Amatiunikira.

    Tikawagwiritsa ntchito

    Tizikonda choonadi.

  2. 2. Mawu ouziridwawa

    Amatiphunzitsadi.

    Amatha kukonza zinthu

    Ndiponso kutilangiza.

  3. 3. Mawu a Mulungu wathu

    Amatitsogolera.

    Ngati timawawerenga

    Zizitiyendera bwino.