Pitani ku nkhani yake

Kuthandiza Anthu Omwe Ali ndi Vuto Losamva ku Indonesia

Kuthandiza Anthu Omwe Ali ndi Vuto Losamva ku Indonesia

M’dziko la Indonesia lomwe nthawi zina limatchedwa mwala wa emarodi m’chigawo chapakati penipeni pa dziko lapansi, muli anthu mamiliyoni omwe ali ndi vuto losamva. Pofuna kuthandiza anthu amenewa, a Mboni za Yehova amapanga mabuku osiyanasiyana a mfundo za m’Baibulo komanso amakonza mapulogalamu othandiza anthu kuphunzira Baibulo m’Chinenero Chamanja cha ku Indonesia. Anthu ambiri akuyamikira kwambiri khama lomwe a Mboni akusonyeza.

Msonkhano Wachigawo wa Chinenero Chamanja

Mu 2016, a Mboni za Yehova anachita msonkhano wachigawo wa m’Chinenero Chamanja cha ku Indonesia pachilumba cha North Sumatra mumzinda wa Medan. M’modzi mwa akuluakulu azachitetezo m’chigawochi anapezeka nawo pamsonkhanowu ndipo anayamikira a Mboni chifukwa chochititsa msonkhanowu kwaulere. Iye anachita chidwi kwambiri ndi zomwe anaona mpaka ankayeserera kuimba nawo nyimbo potengera mmene anthu ankaimbira m’chinenero chamanja.

Mkulu wina woyang’anira malo omwe msonkhanowu unkachitikira ananena kuti msonkhanowu “unayenda bwino kwambiri ndipo panalibe chosokoneza chilichonse. Ndikukhulupirira kuti a Mboni apitiriza kukonza misonkhano yothandiza kwambiri ngati imeneyi kuti athandize anthu a vuto losamva a m’derali.” Iye ananenanso kuti mwiniwake wa malowa atadziwa kuti msonkhanowu unali wa anthu a vuto losamva “anafuna kuwachitira a Mboni chinthu chinachake chabwino. Choncho anandiuza kuti ndipereke chakudya chamasana kwa anthu [onse okwana 300] omwe anapezeka pamsonkhanowu.”

Anthu Anayamikira Mavidiyo a Chinenero Chamanja

A Mboni za Yehova amayenderanso munthu aliyense amene ali ndi vuto losamva n’cholinga chowaphunzitsa uthenga wa m’Baibulo. Nthawi zambiri a Mboniwa amagwiritsa ntchito mavidiyo a m’Chinenero Chamanja cha ku Indonesia omwe amapangidwa n’cholinga chothandiza anthu kuti azisangalala komanso kukhutira ndi moyo wawo.

A Mahendra Teguh Priswanto omwe ndi wachiwiri kwa mkulu wa bungwe lothandiza anthu a vuto losamva mumzinda wa Semarang pa chilumba cha Central Java anati: “Ntchito yothandiza anthu a vuto losamva yomwe mumagwira ndi yotamandika. Mwachitsanzo, vidiyo ya Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala ndi yothandiza kwambiri. Tidzayamikira kwambiri mukapitiriza kugwira ntchito imeneyi.”

“Amatisonyeza Chikondi”

Mayi wina yemwe ali ndi vuto losamva dzina lake Yanti anakhudzidwa kwambiri ndi ntchito yomwe a Mboni amagwira. Iye anafotokoza kuti: “Kawirikawiri anthu amanyoza anthu a vuto losamva koma a Mboni za Yehova amatisonyeza chikondi. A Mboni ambiri omwe alibe vuto losamva amaphunzira chinenero chamanja kuti athandize anthu a vuto losamva kudziwa Mlengi komanso kuti akhale ndi moyo wabwino. Ndinakhudzidwa chifukwa cha khama lawo.”

Kenako Yanti anakhala wa Mboni za Yehova ndipo panopa ali m’gulu lomwe limathandiza kumasulira mavidiyo m’Chinenero Chamanja cha ku Indonesia. Iye anati: “Zinthu za m’chinenero chamanja zomwe timapanga zimathandiza anthu ena omwe sadziwa bwino chinenero chamanja kuti awonjezere luso lawo la chinenero chamanja. Koma zinthuzi zimathandizanso anthu kudziwa mmene angakhalire ndi moyo wosangalala komanso wopindulitsa.”