Pitani ku nkhani yake

Zithunzi Zosonyeza Ntchito Yomanga ku Britain—Gawo 7 (Kuyambira mu September 2018 Mpaka mu February 2019)

Zithunzi Zosonyeza Ntchito Yomanga ku Britain—Gawo 7 (Kuyambira mu September 2018 Mpaka mu February 2019)

Zithunzi izi zikusonyeza mmene ntchito yomanga ofesi ya nthambi yatsopano ya Mboni za Yehova ku Britain inayendera kuyambira mu September 2018 mpaka mu February 2019.

  1. Nyumba Yogwirira Ntchito Zosiyanasiyana Yakumpoto

  2. Nyumba Yogwirira Ntchito Zosiyanasiyana Yakum’mwera

  3. Maofesi

  4. Nyumba Yogona A

  5. Nyumba Yogona B

  6. Nyumba Yogona C

  7. Nyumba Yogona D

  8. Nyumba Yogona E

  9. Nyumba Yogona F

25 September, 2018—Nyumba Yogona A

Magulu ogwira ntchito zosiyanasiyana akuika paipi yaikulu ya madzi pamalo ake pogwiritsa ntchito mathilakitala awiri. Nyumba yomwe ikuoneka chakutsogoloko ndi imene mudzakhale maofesi.

26 September, 2018—Nyumba Yogwirira Ntchito Zosiyanasiyana Yakum’mwera

Makontilakitala akuika makoma opangiratu kunja kwa nyumbayi. Mitundu komanso mmene makomawa asanjidwira zithandiza kuti kaonekedwe ka nyumbayi kazidzagwirizana ndi mmene malo ozungulira nyumbayi akuwonekera.

27 September, 2018—Nyumba Yogwirira Ntchito Zosiyanasiyana Yakum’mwera

Pambuyo pothira konkire pansi, makontilakitala akugwiritsa ntchito mashini kuti konkireyo ikhale yosalala, yonyezimira komanso yolimba kwambiri.

4 October, 2018—Maofesi

Chithunzichi chinajambulidwa kuchokera m’mwamba kumpoto chakum’mawa kwa malowa. Chapakati pa chithunzichi, anthu ogwira ntchito zosiyanasiyana pamalowa akuyeretsa komanso kusalaza pabwalo lomwe padzakhale malo oimika magalimoto pafupi ndi malo olandirira alendo. Chakumanzereko, ntchito yomangirira zitsulo zomwe adzamangirireko khoma ndi denga la pamalo olandirira alendo omwe ali pakati pa nyumba ziwiri za maofesi, yatha. Kutsogoloko kukuoneka nyumba yogwirira ntchito zosiyanasiyana yakumpoto komanso yakum’mwera.

10 October, 2018—Malo a ofesi ya nthambi

Pafupi ndi Nyumba Yogona A, woyeza malo akuona komanso kulemba zokhudza ntchito yomwe okonza kaonekedwe ka malo anagwira. Chifukwa choti ntchito yokonza kaonekedwe ka pamalowa inagwiridwa atangoyamba kumene kumanga, mitengo komanso zomera zina zidzakhala zitakula ntchito yomangayi ikamadzafika kumapeto.

31 October, 2018—Nyumba Yogona F

Ogwira ntchito yopenta akupaka penti pamalo oimika magalimoto. Mmodzi wavala nsapato zomwe sizisiya madindo pamalo omwe amaliza kupenta. Malo omwe apentedwa ndi penti yamtunduwu amakhala olimba kwambiri komanso sathimbirira pakagwera oilo ndipo zimenezi zimapangitsa pentiyu kukhala wabwino kwambiri kupentela pamalo omwe pazidzaimikidwa magalimoto.

6 November, 2018—Nyumba Yogwirira Ntchito Zosiyanasiyana Yakum’mwera

Mapulambala akuyeza komanso kudula matcheni okolekera mapanelo otenthetsera malo aakulu ogwirira ntchito.

6 November, 2018—Maofesi

Ogwira ntchito yopenta akupaka penti yoyambirira mkati mwa Maofesi. M’mwamba mwa ofesi iliyonse anakoleka mashini oziziritsira mpweya omwe awakutira ndi mapulasitiki a mtundu wakuda pofuna kuwateteza.

8 November, 2018—Maofesi

Ogwira ntchito akumangirira zitsulo kudenga la pamalo olandirira alendo.

7 December, 2018—Maofesi

Makontilakitala akunyamula magalasi pogwiritsa ntchito mashini omwe amanyamula zinthu pogwiritsa ntchito mphamvu yokoka ya mpweya ndipo akuwaika kunja kwa chipinda chodyera ndi holo.

10 December, 2018—Maofesi

Ogwira ntchito yoika mawaya a magetsi omwe mumadutsa mauthenga a m’makompyuta akulumikiza masoketi ku mawayawa. Mawaya otalika makilomita pafupifupi 50 aikidwa pa mpata womwe uli kunsi kwa matailosi mu nsanjika zonse 4 za Maofesi. Kukhala ndi mpata pansi pa matailosi n’kothandiza kuti m’tsogolo akadzafuna kusintha kukula kwa ofesi asadzavutike.

26 December, 2018—Nyumba Yogona A

Othandiza pakachitika ngozi zadzidzidzi akuyeserera kupulumutsa munthu yemwe wagwa kuchokera pamakwerero ndipo akulendewera atadzimangirira malamba omuteteza kuti asagwe.

8 January, 2019—Maofesi

Mmodzi mwa ogwira ntchito zosiyanasiyana akuyeza kutalika kwa m’mbali mwa kanjira ka oyenda pansi asanaike matailosi a konkire. Katapila akukumba mayenje m’mbali mwa njirayi momwe mudzadzalidwe mitengo ina yomwe imamera m’derali.

9 January, 2019—Nyumba Zogwirira Ntchito Zosiyanasiyana

Chithunzi chomwe chinajambulidwa kuchokera m’mwamba. Mapanelo a sola aikidwa pamwamba pa madenga a nyumba zonse ziwiri zogwirira ntchito zosiyanasiyana, kuphatikizapo padenga la Maofesi. Mapanelowa azisintha mphamvu ya dzuwa kuti ikhale magetsi.

17 January, 2019—Maofesi

Mmodzi mwa anthu omwe amamalizitsa ntchito zosiyanasiyana akuika matailosi pabwalo la mu nsanjika yachitatu. Zinthu zachikasu zomwe zili pansi pamatailosiwa zikulekanitsa matailosiwa ndi konkire yemwe ali pansi pake ndipo zimateteza matailosiwa kuti asasweke ngati konkireyo itasuntha.

21 January, 2019—Malo omwe akugwiritsa ntchito pa nthawi yomanga

Ogwira ntchito akutenga chakudya chamasana ndipo akudyera m’chipinda chodyera chongoyembekezera. Anthu pafupifupi 1,000 amabwera kudzadya chakudya m’chipindachi m’magulu atatu tsiku lililonse mochita kusinthana.

30 January, 2019—Maofesi

Mathiraki akuchotsa zinthu kuseri kwa maofesi. Chakumanjako, maluvazi aikidwa mukolido pofuna kuteteza kuti kuwala kwa dzuwa kwamphamvu komwe kumachitika m’nyengo yozizira kusamalowe m’chipinda chodyera ndi muholo.

30 January, 2019—Maofesi

Gulu la anthu omwe amamalizitsa ntchito zosiyanasiyana akuika kapeti ndipo akuthandizidwa ndi anthu omwe anadzipereka kudzagwira nawo ntchito kwa tsiku limodzi lokha. Mipingo yonse ya ku Britain ndi ku Ireland inapemphedwa kuti izitumiza anthu odzathandiza kwa tsiku limodzi lokha. Zimenezi zinathandiza kuti anthu opitirira 5,500 agwire nawo ntchitoyi pofika kumapeto kwa mwezi wa February.

12 February, 2019—Nyumba Yogwirira Ntchito Zosiyanasiyana Yakum’mwera

Makontilakitala akumanga khoma lalitali pakati pa nyumbayi pofuna kugawa zipinda. Tizipilala tachikasu tomwe tazikidwa pansipo tikugawa malire omwe muzidutsa mashini okwerapo anthu ogwira ntchito.

20 February, 2019—Maofesi

Ogwira ntchito akusesa ndipo matailosi omwe ali ndi mpata pansi pake aikidwa pamalo olandirira alendo.