Pitani ku nkhani yake

Zithunzi Zosonyeza Ntchito Yomanga ku Britain—Gawo 4 (Kuyambira March Mpaka August 2017)

Zithunzi Zosonyeza Ntchito Yomanga ku Britain—Gawo 4 (Kuyambira March Mpaka August 2017)

Zithunzi izi zikusonyeza mmene ntchito yomanga ofesi ya nthambi yatsopano ya Mboni za Yehova inayendera ku Britain kuyambira mu March mpaka August 2017.

28 March, 2017​—Malo a ofesi ya nthambi

Wogwira ntchito zomanga akutsitsa kanyumba kamatabwa kokhala ndi magalasi kutsogolo kwake. Kanyumba kameneka kaikidwa pamwamba pa kanyumba kena ndipo kazigwiritsidwa ntchito poona zinthu zakutali. Kanyumbaka kali pamalo otetezeka bwino omwenso ndi otchingika. Malo ofotokoza zinthu zomwe alendo angaone komanso malo okwera oonera zinthu zakutali anawatsegulira koyamba mu May 2017, ndipo pofika m’mwezi wa August anthu oposa 17,000 anali atalembetsa kuti akufuna kudzaona mmene ntchito yomangayo ikuyendera.

29 March, 2017​—Nyumba Yogona F

Ogwira ntchito yomanga akuika konkire imene yapangidwa kale pa Nyumba Yogona F, pogwiritsa ntchito mashini okwezera zinthu m’mwamba. Imeneyi ndi nyumba yogona yoyamba kumangidwa. Chifukwa choti nyumbazi zili ndi malo ambiri m’mbali mwake, konkireyi ikhoza kuikidwanso m’malo ake oyenerera mwansanga popanda kuiphwasula.

7 April, 2017—Nyumba Zogona

Nyumba zogona 5 zikumangidwa nthawi imodzi. Chakuno pansipo, ogwira ntchito yomanga akumanga zitsulo asanaike konkire ya maziko a Nyumba Yogona B. Kutsogoloko chakumanja, ogwira ntchito yomanga akuthira konkire ya Nyumba Yogona D. Kutsogoloko chakumanzere, mashini okwezera zinthu m’mwamba akuika konkire ya njira yodutsa chikepe komanso masitepe a Nyumba Yogona E.

19 April, 2017​—Malo a ofesi ya nthambi

Mmodzi mwa ogwira ntchito akugwiritsa ntchito chipangizo chopalira mapaipi pamalo omwe paipi ya madzi ozimitsira moto inalumikizidwa. Mapaipi awiri analumikizidwa powatenthetsa ndi chipangizo chotenthetsera mapaipi a pulasitiki kenako n’kuwalumikiza. Malo amene alumikizidwawo amapalidwa kuti akhale osalala ndipo kenako amayesedwa ngati ndi olimba komanso ngati alumikizidwa bwino. Paipi ya madzi ozimitsira moto imene inalumikizidwa inali yotalika makilomita 4.

25 April, 2017—Nyumba Zogona

Wogwira ntchito akuyeretsa njira yodutsa madzi. Njira zodutsa madzi zomwe zili pamalowa zimathandiza kuti adutsitse misewu pamwamba pa njira za madzizi, komanso kuti madzi a mvula azipita ku madamu zomwe zimathandiza kuti madziwa asamasefukire.

28 April, 2017​—Nyumba Yogona F

Mwamuna ndi mkazi wake omwe ali m’gulu la opanga mapulani a zomangamanga akujambula mizere ya momwe mudzadutse khoma la kolido.

5 May, 2017​—Nyumba Zogona

Chithunzi chojambulidwira m’mwamba cha nyumba 5 zogona zomwe zikumangidwa chakum’mawa kwa malowa. Pamene unkafika mwezi wa September, ntchito yopanga zinthu zosiyanasiyana za konkire inali itatha, ndipo ntchito yomanga makoma a mkati mwa Nyumba Yogona F (kumbuyo chakumanja) inali ili mkati, komanso ntchito yopanga pulasitala ndi yopenta inali itayambika. Pa nthawiyi, ogwira ntchito anali atayamba kumanga makoma akunja komanso mawindo a Nyumba Yogona E (kumbuyo chakumanzere). Nyumba Zogona B, C, ndi D (chakutsogolo kuno), zinali zoti ogwira ntchito zopanga mapulani, a zamagetsi, oika zinthu zosiyanasiyana, komanso omanga makwerero ogwirira ntchito pamalo aatali kwambiri, akhoza kuyamba ntchito zawo.

18 May, 2017​—Malo omwe akugwiritsidwa ntchito pa nthawi yomanga

A Robert Luccioni omwe amathandiza Komiti Yoona za Ntchito Yofalitsa Mabuku ya Bungwe Lolamulira, omwenso ndi woyang’anira Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga Padziko Lonse, akulimbikitsa abale ndi alongo ogwira ntchito yomanga ndi nkhani ya m’Baibulo. Dipatimentiyi imayang’anira ntchito yopanga mapulani komanso yomanga maofesi a nthambi atsopano, ndipo imaonetsetsa kuti ntchitozi zikugwiridwa mwamsanga komanso sizikuwononga ndalama zambiri.

25 May, 201​7—Malo a ofesi ya nthambi

Ogwira ntchito akupanga konkire ya malo omwe padzakhale zinthu zosiyanasiyana monga gasi, mafailo osiyanasiyana a pakompyuta, komanso zipangizo zamagetsi. Chakumanjako, ogwira ntchito akugwiritsa ntchito mashini pothira konkire ya maziko a mpanda womwe udzachepetsa phokoso lochokera ku zipangizo zosiyanasiyana.

7 June, 2017​—Nyumba Yogona E

Gulu la opanga mapulani a zomangamanga likuonanso zimene anajambula asanasankhe malo oti amangirirepo maferemu achitsulo.

13 June, 2017​—Nyumba Yogona F

Wogwira ntchito akumangirira maferemu achitsulo a makoma akunja.

22 June, 2017​—Nyumba Yogona E

Akumanga makwerero kuzungulira Nyumba Yogona E. Makwererowa athandiza ogwira ntchito kuti athe kugwira ntchito yawo m’makoma akunja.

11 July, 2017​—Nyumba Yogona F

Wogwira ntchito yopenta akupenta mawindo amene angoikidwa kumene ndi penti yomwe cholinga chake n’kuteteza mawindowo. Pentiyu amakhala wa pulasitiki akauma ndipo amateteza kuti mawindo asasweke pa nthawi yomanga, kenako ntchitoyo ikatha amadzamuchotsa.

13 July, 2017​—Nyumba Yogona F

Oika ndi kumangirira mapaipi amadzi ndi zinthu zina zosiyanasiyana akuyesa mphamvu ya madzi otentha m’chipinda chogona. Akamaliza kusintha zinthu zofunika kusintha, adzathira konkire yomaliza kuti abise mapaipi a madziwo.

19 July, 2017—Malo a ofesi ya nthambi

Wogwira ntchito yokongoletsa pamalo akudula mbali ina ya duwa lakutchire panja pa chipata cholowera ku ofesi ya nthambi. Duwali limachititsa kuti udzu wosafunikira usamere ndipo zimenezi zimachepetsa nthawi komanso mphamvu zosamalirira malo okongolawa omwe ali pafupi ndi msewu umene mumadutsa magalimoto ambiri.

1 August, 2017—Maofesi

Pogwiritsa ntchito chipangizo choyezera malo chokhala ndi GPS, woyeza malo akuika chizindikiro pamalo omwe padzakhale chipata cholowera ku maofesi. Iye wazika kachikhomo pamalowa ndipo kenako akukapenta n’cholinga choti kazioneka mosavuta. Mbali imeneyi ndi kumene kudzakhale khitchini komanso malo ena amene azidzagwiritsidwa ntchito ngati malo odyera komanso holo yomwe muzidzachitikira zinthu zosiyanasiyana. Nyumba zogona ndi zimene zikuoneka cha kutsogoloko.

8 August, 2017—Nyumba Zogona

Mwamuna limodzi ndi mkazi wake akupanga konkire yomwe idzagwiritsidwa ntchito kuchepetsa kuthamanga kwa madzi a mvula mu ngalande zodzutsa madzi. Cha kutsogoloko, Nyumba Zogona E ndi F zakutidwa ndi pulasitiki kuti ogwira ntchito azigwira ntchito yawo bwino makamaka m’miyezi yozizira.

9 August, 2017—Malo a ofesi ya nthambi

Wogwira ntchito akuphunzitsidwa mmene angagwiritsire ntchito mashini onyamulira katundu omwe amagwiritsa ntchito mphamvu yokoka ya mpweya ponyamula katunduyo. Mashiniwa amagwiritsidwa ntchito ponyamula komanso kuika miyala m’mphepete mwa msewu yolemera pafupifupi 70 kilogalamu mwala uliwonse. Miyalayi ikakhala m’malo ake, amaimanga pogwiritsa ntchito konkire kuti ilimbe.

16 August, 2017​—Malo a ofesi ya nthambi

Pamene paipi ya madzi ikuikidwa pa malo ake, wogwira ntchito yokonza zinthu zosiyanasiyana wagwira paipi ina yomwe yalumikizidwa ku paipi ya madziyo n’cholinga choti paipiyo isasunthe koma ikhale mmene akufunira kuti ikhalire. Ofesi ya nthambiyi idzafunika mapaipi a madzi okwana pafupifupi makilomita 5 kuwaphatikiza.

22 August, 2017​—Nyumba Yogona E

Wogwira ntchito akudula njerwa pogwiritsa ntchito mashini amagetsi. Njerwa zodula pakatizi amazimanga m’njira yochititsa chidwi kumapeto kwa nyumba yogona. Nyumba zonse zogona zidzakongoletsedwa ndi njerwa zoposa 300,000.