Pitani ku nkhani yake

A Mboni za Yehova Akufuna Kusamutsa Likulu Lawo la Padziko Lonse

A Mboni za Yehova Akufuna Kusamutsa Likulu Lawo la Padziko Lonse

Mu July 2009, a Mboni za Yehova anagula malo amene ali kumpoto kwa mzinda wa New York n’cholinga chofuna kusamutsirako likulu lawo la padziko lonse. Malowa omwe ndi aakulu maekala 253, ali pamtunda wa makilomita pafupifupi 80 kuchokera kumpoto chakumadzulo kwa malo amene panopo pali likulu lawo ku Brooklyn, mzinda wa New York. A Mboni za Yehova akhala akugwiritsira ntchito malo amene panopa pali likulu lawo kuyambira 1909.

Kumalo atsopanowa, a Mboni za Yehova adzamangako maofesi komanso nyumba zogona ndipo anthu pafupifupi 800 azidzagona ndiponso kugwira ntchito kumalowa. Kumalowa adzamangakonso nyumba yosungiramo zinthu zakale zochititsa chidwi zokhudza mbiri ya Mboni za Yehova.

Nyumba zonse zimene zidzamangidwe pamalowa zidzatenga malo aakulu maekala 45 basi ndipo malo otsalawo adzakhala nkhalango. Koma malo ochepa kwambiri ozungulira nyumbazi adzakongoletsedwa.

Akatswiri olemba mapulani a nyumba akonza zoti nyumba zomwe zikhale likulu latsopanolo zikhale zosawononga kwambiri magetsi. Zimenezi zidzathandiza kuti asadzawononge kwambiri ndalama komanso chilengedwe. Mwachitsanzo, madenga a nyumbazo sadzakhala a malata kapena matailosi. M’malomwake, madengawo adzawakonza m’njira yoti pamwamba pake adzathe kudzalapo maluwa ndi tizomera tina ndipo sipadzidzafunika ndalama zambiri akafuna kukonzanso madengawo. Kuwonjezera pamenepa, madengawo adzathandiza kuti m’nyumbazo musamadzazizire kapena kutentha kwambiri, komanso adzathandiza kuti mvula ikamagwa, madzi ochokera padenga asamadzathamange ndiponso azidzakhala ochepa. Maofesi adzawamanga m’njira yoti m’kati mwake muzidzakhala mowala kwambiri popanda magetsi. Chinthu chinanso chofunika kwambiri n’choti akatswiriwa akonza zoti adzamangepo zinthu zina zothandiza kuti madzi asamadzawonongeke.

Kodi n’chifukwa chiyani a Mboni za Yehova akonza zosamutsa likulu lawo? Chifukwa chakuti ntchito yosindikiza Mabaibulo ndi mabuku yomwe inkachitika ku Brooklyn kokha inayamba kuchitikanso kumaofesi a Mboni za Yehova a m’madera ena a dziko lapansi. Mwachitsanzo mu 2004, dipatimenti yosindikiza komanso kutumiza mabuku ku United States imene inali ku Brooklyn, inasamutsidwira kutauni ya Wallkill, m’dera lomwelo la New York. Tauni imeneyi ili pa mtunda wa makilomita pafupifupi 145 kumpoto chakumadzulo kwa Brooklyn.

Chifukwa china n’chakuti a Mboni za Yehova anaona kuti pamafunika ndalama zambiri kuti azitha kugwira bwino ntchito yawo ku Brooklyn komanso kuti azitha kusamalira nyumba zawo. Choncho iwo akasamutsira likulu lawo kumalo atsopanowa, azitha kugwiritsira bwino ntchito ndalama zimene anthu amapereka zothandizira pa ntchito yawo yophunzitsa anthu Baibulo.

Akuluakulu a boma adzavomereza kuti ntchito yomanga likulu latsopano la Mboni za Yehova iyambe ngati ataona kuti ntchitoyo siidzawononga zachilengedwe. Ngati zonse zitayenda bwino, ntchitoyi idzayamba m’chaka cha 2013 ndipo idzatenga zaka zinayi kuti ithe.

Kuwonjezera pa mafakitale osindikiza mabuku amene ali ku Wallkill, New York, a Mboni za Yehova alinso ndi malo amene pali masukulu awo osiyanasiyana ku Patterson, ku New York komweko. Gulu la Mboni za Yehova lilinso ndi maofesi ena m’mayiko ambirimbiri. Padziko lonse pali anthu a Mboni za Yehova oposa 7.5 miliyoni.