Pitani ku nkhani yake

M’busa Anapeza Mayankho

M’busa Anapeza Mayankho

 Tsiku lina wa Mboni za Yehova wina dzina lake Eliso ankaphunzira Baibulo ndi munthu wachidwi. Kenako munthuyo analandira alendo mwadzidzidzi. Alendowo anali m’busa wina ndi mkazi wake. Eliso anali atamva zoti chaposachedwapa mwana wamwamuna mmodzi yekhayo wa banjali anamwalira.

 Eliso atapepesa banjali chifukwa cha imfa ya mwanayo m’busayo ndi mkazi wake anayamba kulira kwambiri. Kenako m’busayo ananena mokwiya kuti: “Sindikumvetsa kuti n’chifukwa chiyani Mulungu analola kuti mayesero amenewa atigwere! N’chifukwa chiyani ananditengera mwana wanga mmodzi yekhayo? Ndakhala ndikutumikira Mulungu kwa zaka 28, ndakhala ndikuchita zinthu zabwino zambiri, zoona malipiro anga n’kukhala amenewa! N’chifukwa chiyani Mulungu anapha mwana wanga?”

 Eliso anafotokozera banjali kuti Mulungu sanatenge mwana wawo. Anakambirana nawonso zokhudza dipo, kuuka kwa akufa komanso chifukwa chimene Mulungu amalolera kuti zinthu zoipa zizichitika. M’busayu ndi mkazi wake anauza Eliso kuti wawayankha mafunso amene akhala akupempherera kuti ayankhidwe.

 Mlungu wotsatira m’busayu ndi mkazi wake atapitanso kwa mayi uja anakhala nawo paphunziro la Baibulo. Pa nthawiyi, Eliso amakambirana ndi mayiyo mutu wakuti “Anthu Amene Anamwalira Adzakhalanso ndi Moyo,” m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Banjali linamvetsera phunziroli mwachidwi ndi kuyankhapo.

 Pa nthawi imene kunali msonkhano wapadera wa Mboni za Yehova ku Tbilisi, Georgia, banjali linapita nawo kumsonkhanowu ndipo linachita chidwi kwambiri litaona chikondi ndi mgwirizano. Iwowo anayesetsa kwa nthawi yaitali kulimbikitsa anthu a m’tchalitchi chawo kuti azisonyezana makhalidwe amenewa koma sizinatheke.