Pitani ku nkhani yake

Dera laling’ono la Apex ku Iqaluit, pachilumba cha Baffin ku Nunavut, m’dziko la Canada

APRIL 17, 2020
CANADA

Mwambo Wokumbukira Imfa ya Khristu wa 2020—ku Canada

Kuchita Mwambo wa Chikumbutso M’madera a Kutali Kwambiri Padziko Lapansili

Mwambo Wokumbukira Imfa ya Khristu wa 2020—ku Canada

Ofalitsa 27 amumpingo wa Iqaluit, kuzilumba za Arctic Archipelago ku Canada, anachita mwambo wa Chikumbutso polumikizana kudzera pa vidiyokomfelensi. Mumpingowu muli ophunzira Baibulo 55, ndipo 12 anaonera nawo nkhani ya Chikumbutso. Iwo anasangalala kwambiri chifukwa choti anakwanitsa kuchita nawo mwambowu.

Ambiri mwa ophunzirawa sakanakwanitsa kukumana pamodzi kuti achite Chikumbutso chifukwa amakhala m’madera akutali kwambiri a gawo la mpingowu. Gawoli ndi lalikulu pafupifupi makilomita 2 miliyoni m’mbali zake zonse kuchokera ku Kimmirut kukafika ku Grise Fiord, komwe ndi kumpoto kwa dziko la Canada.

M’bale Isaac Demeester yemwe ndi mkulu mumpingo wa Iqaluit ananena kuti: “Chaka chino, kanali koyamba kulumikizana ndi anthu omwe timaphunzira nawo Baibulo kuti aonere nawo mwambo wa Chikumbutso. Mmodzi mwa ophunzira Baibulowa wa ku Grise Fiord, anaitanira anzake 4 kuti nawonso alumikizidwe moti anthu okwana 5 ochokera kuderali lomwe ndi lakutali kwambiri analumikizana nafe pamwambowu.”

Zinthu zachilendo zomwe zikuchitika chifukwa cha kubwera kwa mliri wa COVID-19, zathandiza abale ndi alongo ambiri amumpingo wa Iqaluit kuona ubwino wokhala wokonzeka kusintha zinthu pa moyo.

Mlongo Kathy Burechailo anafotokoza kuti: “Tinkalankhulana pafoni ndi anthu okhala m’madera akum’mawa kwa nyanja. Ndinasangalala kwambiri kulankhulana ndi anthu am’gawo lathu omwe amakhala kutali kwambiri. Panopa anthu akumangokhala pakhomo moti akufunika kulimbikitsidwa.”

Mlongo Laura McGregor ananena kuti: “Tikumva kuti tikupanikizika kwambiri kukhala patokha kuno ku Iqaluit chifukwa cha mliriwu. Zikutichititsa kuti tizikumana ndi mavuto azachuma ndipo tikumakhala ndi nkhawa yoti kaya mawa kugwa zotani. Koma ndinasangalala kuti ndinaphika koyamba mkate wa pa Chikumbutso womwe tinagwiritsa ntchito pabanja lathu. Zinali zosangalatsa kwambiri kuchita zinthu limodzi. Tinaona kuti mwambowu sumafuna zambiri. Kunena zoona ndi madalitso kuchita mwambo woterewu pogwiritsa ntchito zinthu zosavuta kupeza.”

M’bale Demeester anamaliza ndi kufotokoza kuti: “Ngakhale kuti mliri wa COVID-19 watilekanitsa m’njira zosiyanasiyana, n’zochititsa chidwi kuona mmene mpingo wathu ukuchitira zinthu mogwirizana m’nyengo ya Chikumbutso imeneyi. Mwambo wachaka chino wasintha mmene anthu amachitira zinthu pa moyo wawo.”

Ngati zinthu zingayende bwino, mpingo wa Iqaluit ukuyembekezera mwachidwi kumanga Nyumba ya Ufumu yawo m’tsogolomu. Koma panopa, tikukhulupirira kuti Yehova adalitsa khama lawo pofikitsa uthenga wabwino kwa anthu am’zigawo zakumpoto kwenikweni kwa Canada. Zigawozi zili m’gulu la madera omwe ali kutali kwambiri padziko lapansili.—Machitidwe 1:8.