Pitani ku nkhani yake

M’bale Mark Sanderson akulankhula pamsonkhano wapadera ku Warsaw, m’dziko la Poland

3 MAY, 2022
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

“Muziganizira Kwambiri za Ubwenzi Wani Ndi Yehova”

Pulogalamu Yapadera Yomwe Inalimbikitsa Abale a ku Ukraine ndi Poland

“Muziganizira Kwambiri za Ubwenzi Wani Ndi Yehova”

Pa 26 April 2022, M’bale Mark Sanderson, amene amatumikira m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, anafika m’dziko la Poland kuti akalimbikitse mwauzimu abale ndi alongo omwe anakhudzidwa ndi nkhondo yomwe ikuchitika m’dziko la Ukraine.

Pamalo a Msonkhano ku Poland, abale akugwira ntchito pa zipangizo za mawu ndi mavidiyo

Abale ndi alongo a m’mipingo yonse ya ku Poland ndi Ukraine anaitanidwa kumsonkhano wapaderawu womwe unachitika pa 30 April 2022. Ku Poland, abale ndi alongo omwe anathawa ku Ukraine kuphatikizapo omwe amagwira ntchito yopereka chithandizo kukagwa mavuto amwadzidzidzi, anaitanidwa kuti adzapezeke pamsonkhanowu omwe unkachitikira Pamalo a Msonkhano ku Warsaw. Onse omwe anamvetsera msonkhanowu analipo oposa 250,000. Ndipo chiwerengerochi chikuphatikizapo anthu a ku Poland ndi Ukraine omwe analumikizidwa kudzera pa vidiyokomfelensi.

M’bale Sanderson anauza abale ndi alongowo kuti: “Abale ndi alongo padziko lonse akuganizira za inu ndipo amakupemphererani. Kulikulu la padziko lonse, tsiku lililonse abale amapereka mapemphero chifukwa cha abale a ku Russia ndi Ukraine. Zimenezi zikuphatikizaponso mapemphero amene amaperekedwa pamsonkhano wa abale a m’Bungwe Lolamulira.” M’bale Sanderson anatsimikizira abalewa kuti “kukumana mavuto ndi si umboni woti Yehova wasiya kutidalitsa. Iye akuona zomwe zikukuchitikirani, amakukondani ndipo ali pafupi kwambiri makamaka ndi onse omwe avutika.”

Abale ndi alongo omwe anathawa ku Mariupol m’dziko la Ukraine, akuonerera msonkhano wapadera

M’bale Sanderson anapitiriza kunena kuti: “Muziganizira kwambiri za ubwenzi wanu ndi Yehova. Cholinga chathu si chongofuna kuti tipulumuke basi, koma tikufuna kuti tithane ndi mavutowa chikhulupiriro chathu chili cholimba komanso tili pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Zimene ndi zimene Yehova akutiphunzitsa.”

Serhiy amene ndi mkulu ku Odessa m’dziko la Ukraine ananena kuti: “Mawiki apitawa sindinkagona mokwanira chifukwa cha nkhawa, chisoni komanso mantha. Komabe msonkhanowu wandilimbikitsa kwambiri kukhulupirira kuti Yehova si kuti amangotisamalira ngati gulu, koma amatisamaliranso aliyense payekhapayekha.”

Mlongo Tatiana amene anathawa kwawo ku Kyiv m’dziko la Ukraine ananena kuti: “Lero ndaona kuti Yehova ali nane pafupi kwambiri. Ndimamva ngati kuti Yehova wandihaga komanso kunditsimikizira kuti amandikonda. Kulikonse komwe tingapite, Yehova amakhala nafe.”

Timawakonda kwambiri abale ndi alongo athuwa. Ndipo tikukhulupirira kuti msonkhano wapaderawu wawathandiza kukumbukira za “kukoma mtima kosatha” komwe Yehova ali nako pa anthu ake.—Salimo 136:1.