Pitani ku nkhani yake

SEPTEMBER 19, 2019
GABON

Ntchito Yapadera Yolalikira ku Gabon

Ntchito Yapadera Yolalikira ku Gabon

Pofuna kufikira anthu omwe amakhala m’madera omwe salalikidwa kawirikawiri ku Gabon, ofesi ya nthambi ya Cameroon inakonza ntchito yapadera yolalikira kuyambira pa 1 June mpaka pa 31 August, 2019. Ntchitoyi inakonzedwa n’cholinga chofuna kulalikira m’mizinda 10 yomwe ili ndi anthu ambirimbiri. Mizindayi ndi: Franceville, Koulamoutou, Lambaréné, Libreville, Makokou, Moanda, Mouila, Oyem, Port-Gentil, komanso Tchibanga. Abale ndi alongo ochokera kumayiko ena anagwira nawo ntchito yapaderayi kuphatikizapo 400 ochokera ku Belgium, Canada, France, ndi ku United States.

Ku Gabon kuli anthu oposa 2 miliyoni. Pafupifupi 80 peresenti ya anthu m’dzikoli amalankhula Chifulenchi chomwe n’chinenero chimene chimagwiritsidwa ntchito kwambiri, ndipo pafupifupi 30 peresenti ya anthuwa amalankhulanso Chifang’i chomwe n’chinenero chawo chobadwira. Chifukwa cha zimenezi, abale ndi alongo ankagwiritsa ntchito zinenero zonse ziwiri polalikira.

Munthu wina wolankhula Chifang’i yemwe amakhala ku Bissegue komwe ndi mbali ina ya mzinda wa Libreville, anachita chidwi ndi Baibulo ndipo anati: “Kanali koyamba kumva uthenga wochokera kwa Mulungu m’chinenero changa!”

Mlongo wina yemwe anagwira nawo ntchitoyi anati: “Ntchito yapaderayi yapereka umboni wakuti m’gulu la Yehova timakondana komanso kugwirizana. Abale ndi alongo anali ochezeka, ochereza, opatsa, olimbikitsa komanso anasonyeza chikondi chenicheni. Zimenezi zandikumbutsa zimene Paulo ananena zokhudza mpingo wa ku Filipi kuti, tili ‘ndi maganizo amodzi, ndi chikondi chofanana. Tilinso ogwirizana mu mzimu umodzi, ndi mtima umodzi.’”—Afilipi 2:2.