Pitani ku nkhani yake

MAY 6, 2016
RWANDA

Khothi Lalikulu Kwambiri Linachita Zinthu Mwachilungamo ku Rwanda

Khothi Lalikulu Kwambiri Linachita Zinthu Mwachilungamo ku Rwanda

Akuluakulu a mu mzinda wa Kigali analamula kuti nyumba ina igwetsedwe. Nyumbayo itagwetsedwa, Khoti Lalikulu linanena kuti a Mboni za Yehova ndi olakwa ndipo ayenera kupereka ndalama za chipukuta misozi kwa eni ake a nyumbayo. Komabe, ofesi yomva madandaulo a anthu inaona kuti nkhaniyi sinayende mwachilungamo ndipo inauza khotilo kuti liunikenso chigamulo chakecho. Patapita nthawi yayitali, khotilo linasintha chigamulocho n’kunena kuti a Mboni ndi osalakwa. Izi zinatheka chifukwa cha khama la mkulu wa ofesi ya omva madandaulo a anthu komanso oweruza milandu oganiza bwino omwe anaunikanso nkhaniyi.

Akuluakulu a Mzinda wa Kigali Analamula Kuti Mzindawo Ukonzedwe

M’chaka cha 2006, oyang’anira mzinda wa Kigali analamula kuti tinyumba tonse togulitsira malonda timene tinamangidwa m’mbali mwa misewu ikuluikulu tigwetsedwe pofuna kuti mzindawu uzioneka bwino. Iwo analamulanso kuti anthu ena onse akonze ndi kukongoletsa malo ozungulira nyumba zawo.

Potsatira lamulo limeneli, nyumba zonse zimene zinamangidwa mosatsatira malamulo zinkayenera kugwetsedwanso. Imodzi mwa nyumbazi ndi ya a Ngayabateranya, yomwe inali pafupi ndi maofesi a Mboni za Yehova chifukwa inamangidwa popanda chilolezo chochokera ku boma. Kuonjezera pamenepo, zipangizo zimene anagwiritsa ntchito pomanga nyumbayo zinali zosagwirizana ndi malamulo omangira a m’dziko la Rwanda. Akuluakulu a mzindawo analamula kuti aliyense amene ali ndi nyumba yosayenera aigwetse pasanathe masiku 21 koma palibe amene anatsatira lamuloli. Zimenezi zinachititsa kuti meya wa chigawo cha Gasabo alembe kalata yolamula kuti nyumbazo zigwetsedwe. Nyumbazo zitagwetsedwa, a Mboni za Yehova anakongoletsa malo ozungulira maofesi awo pokonza njira yodutsa anthu komanso kudzala kapinga ndi maluwa. Maofesiwa ali m’chigawo cha Gasabo, kudera la Remera la mzinda wa Kigali.

Khoti la M’chigawo cha Gasabo Linanena kuti Amboni ndi Olakwa

Akuluakulu oyang’anira mzinda wa Kigali atagumula nyumba ya a Ngayabateranya, iwo ndi anzawo anakadula chisamani ku khoti la mumzinda wa Gasabo chonena kuti a Mboni ndi amene anagwetsa nyumbayo. A Ngayabateranya limodzi ndi anzawowo ananena kuti a Mboni ayenera kuwapatsa ndalama za chipukuta misozi chifukwa chowagwetsera nyumbayo. Iwo ananena zimenezi ngakhale kuti sanapereke umboni womveka wotsimikiza za nkhaniyi. A Mboni za Yehova anapereka umboni poonetsa chikalata chosonyeza kuti akuluakulu oyang’anira mzindawo ndi amene anagumula nyumbayo. Koma khotilo linanyalanyaza umboniwo ndipo linagamula kuti a Mboni ndi olakwa.

Khoti Lalikulu Linasintha Chigamulocho

A Mboni za Yehova anachita apilo za nkhaniyi ku khoti lalikulu chifukwa zinali zoonekeratu kuti nkhaniyo sinayende mwachilungamo. Khoti lalikululo litaunika maumboni amene anaperekedwa, linanena kuti panalibe zifukwa zomveka zimene zinachititsa kuti khoti loyambalo ligamule kuti a Mboni anali olakwa. Pa 5 November, 2010, khoti lalikululo linanena kuti a Ngayabateranya limodzi ndi anzawo aja, anasuma nkhani yosayenera komanso yongotayitsa nthawi. Khotilo linalamula kuti anthuwo alipire ndalama zokwana 800,000 francs za ku Rwanda, zomwe ndi madola 1,360 a ku United States.

Khoti Lalikulu Kwambiri Linanyalanyaza Umboni Wofunika

A Ngayabateranya sanagwirizane ndi chigamulo cha khoti lalikulu ndipo anachita apilo ku Khoti Lalikulu Kwambiri m’dzikomo. Panthawi yozenga mlanduwo, Mlembi Wamkulu wa dera la Remera anapereka umboni woti nyumba ya a Ngayabateranya inamangidwa mosatsatira malamulo ndipo inagumulidwa mogwirizana ndi cholinga cha boma chokonzanso mzindawo. Khotilo linavomereza kuti a Mboni si amene anagumula nyumbayo. Komabe, linanena kuti a Mboniwo ndi amene anachititsa kuti nyumbayo igwetsedwe. Khotilo linanyalanyaza umboni wofunika kwambiri womwe unaperekedwa ndipo linanena kuti a Mboniwo anakhala ngati apeza phindu mopanda chilungamo chifukwa choti anakongoletsa malo amene panali nyumbayo. Khotilo linagamula kuti a Mboni apereke ndalama zokwana 22,055,242 francs za ku Rwanda, zomwe ndi zoposa madola 33,000 a ku America. Ngakhale kuti a Mboniwo anali osalakwa, iwo anapereka ndalamazo pa 4 April, 2013.

Ofesi Yomva Madandaulo a Anthu Inauza Khoti Lalikulu Kwambiri Kuti Liunikenso Chigamulo Chake

A Mboni za Yehova anakadandaula za nkhaniyi ku ofesi yomva madandaulo a anthu chifukwa chowanamizira kuti ndi amene anagumula nyumba ya a Ngayabateranya. Mayi Aloysie Cyanzayire, omwe ndi mkulu womva madandaulo a anthu, anaunika dandaulo la a Mboni za Yehova komanso chigamulo chimene Khoti Lalikulu linapereka.

Mayi Cyanzayire ataunika maumboni amene anaperekedwa, anapeza kuti akuluakulu oyang’anira mzinda wa Kigali anagwetsa nyumbayo chifukwa choti a Ngayabateranya sanatsatire malamulo. Iwo ananenanso motsindika kuti panalibe chifukwa choti a Mboni alangidwe chifukwa chokongoletsa malo apafupi ndi maofesi awo popeza zimenezi ndi zimene boma linalimbikitsa anthu kuti achite. Zimene a Mboni anachita pokongoletsa komanso kupitiriza kukonza malowa zinali “zofunika kwambiri” ndipo “zinathandiza boma pantchito yake yokonza mzindawu kuti uzioneka bwino.”

Mmene nyumba zimene zinamangidwa mosatsatira malamulo zinkaonekera komanso pambuyo poti nyumbazo azigwetsa

Pa December 4, 2013, mayi Cyanzayire anapempha Khoti Lalikulu Kwambiri kuti liunikenso chigamulo chake. Khotilo linasankha oweruza milandu atsopano kuti azengenso mlanduwo ndipo pa 17 October, 2014, oweruzawo anasintha chigamulo chimene chinaperekedwa poyamba chija ponena kuti zimene a Ngayabateranya ankanena zoti a Mboni anawagwetsera nyumba yawo zinali zopanda umboni. Khotilo linalamula a Ngayabateranya kuti abweze ndalama zimene a Mboni za Yehova anawapatsa zija komanso kuti apereke ndalama zimene zinawonongedwa poyendetsa mlanduwu. Maloya amene akuyimira a Mboni za Yehova pa mlanduwo komanso munthu amene Khotilo linamusankha kuti aonetsetse kuti ndalamazo zaperekedwa, panopa akugwira ntchito yoonetsetsa kuti a Ngayabateranya apereka ndalama zonse.

Kutsatira Malamulo Kwateteza a Mboni

A Mboni za Yehova akuthokoza kukoma mtima kwa mayi Cyanzayire chifukwa chothandiza pa nkhaniyi monga mkulu womva madandaulo a anthu. Iwo akuyamikiranso zimene Khoti Lalikulu Kwambiri linachita posintha chigamulo chake chapoyamba. Mosakayikira, zimenezi zithandiza anthu okonda chilungamo m’dziko la Rwanda kuzindikira kuti dzikoli lili ndi njira zamphamvu zimene limagwiritsa ntchito pofuna kuonetsetsa kuti chilungamo chikuchitika komanso kuti malamulo akutsatiridwa.