Pitani ku nkhani yake

Kodi Baibulo Linasinthidwa Kapena Kusokonezedwa?

Kodi Baibulo Linasinthidwa Kapena Kusokonezedwa?

 Ayi. Tikaona zimene zili m’mipukutu ya kale zikusonyeza kuti Baibulo silinasinthidwe. Zili choncho ngakhale kuti kwa zaka masauzande ambiri lakhala likukoperedwa pa zinthu zimene n’kupita kwa nthawi zimawonongeka.

Kodi zimenezi zikutanthauza kuti panalibe zolakwika pamene ankalikopera?

 Pali mipukutu ya Baibulo yambiri yomwe ndi ya kale imene yapezeka. Zimene zili m’mipukutu ina ndi zosiyana ndi zimene zili m’mipukutu ina, ndipo zimenezi zikusonyeza kuti panali zolakwika zina pamene ankakopera mipukutuyi. Zinthu zambiri zomwe ndi zosiyana m’mipukutuyi ndi zing’onozing’ono ndipo sizisintha tanthauzo la malembawo. Komabe, zikuoneka kuti malemba ena anasinthidwa kwambiri ndipo zikuoneka kuti anachita zimenezi mwadala n’cholinga chofuna kusokoneza uthenga wa m’Baibulo. Taonani zitsanzo ziwiri izi:

  1.   M’mipukutu ina ya kale ya Baibulo, lemba la 1 Yohane 5:7 analimasulira kuti: “kumwamba kuli Atate, Mawu, komanso Mzukwa Woyera: onsewa ndi mmodzi.” Komabe, mipukutu yodalirika imasonyeza kuti mawu amenewa munalibe m’mipukutu yoyambirira. Mawuwa anachita kuwonjezeredwa. a N’chifukwa chake mawuwa sanaphatikizidwe m’Mabaibulo odalirika a masiku ano.

  2.   Dzina la Mulungu limapeza maulendo masauzande ambiri m’mipukutu ya kale ya Baibulo. Koma m’Mabaibulo ambiri anachotsa dzinali n’kuika mayina aulemu monga “Ambuye” kapena “Mulungu.”

Kodi tingatsimikize bwanji kuti m’Baibulo mulibenso zolakwika zina zambiri?

 Panopa pali mipukutu yambiri imene yapezeka ndipo zimenezi zathandiza kuti zikhale zosavuta kuzindikira zinthu zomwe n’zolakwika. b Kodi kufananitsa zomwe zili m’mipukutuyi kwasonyeza zotani pa nkhani ya kulondola kwa Baibulo?

  •   Pothirira ndemanga pa Malemba Achiheberi (omwe amadziwika kwambiri kuti “Chipangano Chakale”), katswiri wamaphunziro dzina lake William H. Green ananena kuti: “Tikhoza kunena molimba mtima kuti palibenso zinthu zina zakale zimene zinakoperedwa molondola kwambiri chonchi.”

  •   Ponena za Malemba Achigiriki, kapena kuti “Chipangano Chatsopano,” katswiri wina wa Baibulo dzina lake F. F. Bruce analemba kuti: “Umboni wotsimikizira kuti nkhani zomwe zili mu Chipangano Chatsopano n’zoona ndi waukulu kwambiri kuposa umboni wa zolemba zina zili zonse zakale. Koma n’zodabwitsa kuti palibe amene amakayikira zolemba zakalezi zomwe zilibe umboni wokwanira.”

  •   Sir Frederic Kenyon, omwe ndi katswiri wodziwika bwino wa mipukutu ya Baibulo, ananena kuti munthu “akhoza kunyamula Baibulo m’manja mwake n’kunena mosaopa kapena kukayikira kuti amene wanyamulawo ndi mawu enieni a Mulungu omwe akhalapo kwa zaka zambiri popanda mfundo zofunika kwambiri kusokonekera.”

Kodi pali zifukwa zinanso ziti zotipangitsa kutsimikiza kuti Baibulo linakoperedwa molondola?

  •   Okopera Baibulo a Chiyuda komanso a Chikhristu, analemba nkhani zimene zimasonyeza machimo akuluakulu omwe atumiki a Mulungu anachita. c (Numeri 20:12; 2 Samueli 11:2-4; Agalatiya 2:11-14) Komanso iwo analemba nkhani zodzudzula mtundu wa Ayuda chifukwa chosamvera. Nkhanizi zinathandizanso anthu kuzindikira ziphunzitso zina zomwe zinali maganizo a anthu. (Hoseya 4:2; Malaki 2:8, 9; Mateyu 23:8, 9; 1 Yohane 5:21) Anthu amene anakopera nkhanizi anasonyeza kuti anali okhulupirika komanso ankalemekeza kwambiri Mawu a Mulungu chifukwa anakopera nkhanizo molondola kwambiri.

  •   Kodi si zomveka kunena kuti Mulungu amene anauzira Baibulo, angathe kuchita chilichonse kuti lipitirizebe kukhala lolondola? d (Yesaya 40:8; 1 Petulo 1:24, 25) Komanso sikuti iye ankafuna kuti Baibulo lingothandiza anthu akale, koma ankafuna kuti litithandizenso masiku ano. (1 Akorinto 10:11) Ndipotu, “zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize. Malembawa amatipatsa chiyembekezo chifukwa amatithandiza kupirira ndiponso amatilimbikitsa.”—Aroma 15:4.

  •   Yesu komanso otsatira ake ankagwiritsa ntchito nkhani zochokera m’Malemba Achiheberi ndipo sanakayikire kuti nkhanizo zinali zolondola.—Luka 4:16-21; Machitidwe 17:1-3.

a Mawuwa sapezeka mu Codex Sinaiticus, Codex Alexandrinus, Vatican Manuscript 1209, original Latin Vulgate, Philoxenian Harclean Syriac Version, kapena mu Syriac Peshitta.

b Mwachitsanzo, mipukutu ya Chigiriki yoposa 5,000 yomwe ena amaitchula kuti Chipangano Chatsopano, kapena kuti Malemba Achigiriki, inapezeka.

c Baibulo silimanena zinthu m’njira yosonyeza kuti atumiki a Mulungu sangalakwitse chilichonse, ndipo limanena momveka bwino kuti: “Palibe munthu amene sachimwa”.​—1 Mafumu 8:46.

d Baibulo limanena kuti, ngakhale kuti Mulungu sanauze mwachindunji anthu omwe analemba Baibulo mawu onse amene analemba, iye ndi amene ankatsogolera maganizo awo.—2 Timoteyo 3:​16, 17; 2 Petulo 1:21.