Pitani ku nkhani yake

Kodi Pasika ndi Chiyani?

Kodi Pasika ndi Chiyani?

Yankho la m’Baibulo

 Pasika, unali mwambo wachiyuda wokumbukira kuti Mulungu anapulumutsa Aisiraeli ku ukapolo wa ku Iguputo m’chaka cha 1513 B.C.E. Mulungu analamula kuti chaka chilichonse, Aisiraeli azikumbukira nthawi yapaderayi pa tsiku la 14 la mwezi wachiyuda wotchedwa Abibu. Mweziwu unadzayamba kudziwika ndi dzina loti Nisani.​—Ekisodo 12:42; Levitiko 23:5

N’chifukwa chiyani mwambowu unkatchedwa kuti Pasika?

 Dzina lakuti “Pasika,” linachokera pa zomwe zinachitika pa nthawi imene Mulungu anapha mwana aliyense woyamba wa ku Iguputo koma sanaphe mwana aliyense wa Aisiraeli. (Ekisodo 12:27; 13:15) Mulungu asanabweretse mliri woopsawu, anauza Aisiraeli kuti aphe mwana wa nkhosa kapena mbuzi, n’kuwaza magazi ake pafelemu la nyumba zawo. (Ekisodo 12:21, 22) Ndiyeno Mulungu anaona magaziwo pa nyumba za Aisiraeli n’kupitirirapo ndipo mwana woyamba aliyense wa Aisiraeli anapulumuka.​—Ekisodo 12:7, 13.

Kodi Aisiraeli ankachita zotani pa mwambowu?

 Mulungu anauza Aisiraeli zoyenera kuchita pa mwambo wa Pasika woyamba. a Zinthu zina zomwe zinkachitika pa mwambowu ndi izi:

  •   Nsembe: Pa tsiku la 10 la mwezi wa Abibu (Nisani), banja lililonse linkasankhiratu mwana wa nkhosa (kapena mbuzi) wa chaka chimodzi. Ndipo pa tsiku la 14 ankapha mwana wa nkhosayo. Pa Pasika woyamba, Ayuda anawaza magazi pa mafelemu a m’mbali ndi a pamwamba a khomo la nyumba zawo komanso anawotcha ndi kudya nyama yake yonse.​—Ekisodo 12:3-9.

  •   Chakudya: Kuwonjezera pa nyama ya nkhosayo (kapena mbuzi), pa mwambo wa Pasikawo, Aisiraeli anauzidwanso kuti azidya mikate yopanda chofufumitsa ndi masamba owawa.​—Ekisodo 12:8

  •   Chikondwerero: Mwambo wa Pasika ukatha, Aisiraeli ankachita chikondwerero cha mikate yopanda chofufumitsa kwa masiku 7. Choncho pa masiku onsewa sankadya mikate yokhala ndi chofufumitsa.​—Ekisodo 12:17-20; 2 Mbiri 30:21.

  •   Maphunziro: Tsiku la Pasika, linkapereka mwayi kwa makolo wophunzitsa ana awo zokhudza Yehova Mulungu.​—Ekisodo 12:25-27.

  •   Ulendo: Patapita nthawi, Aisiraeli ankafunika kupita ku Yerusalemu kukachita mwambo wa Pasika.​—Deuteronomo 16:5-7; Luka 2:41.

  •   Zinthu zina zomwe zinkachitika: M’nthawi ya Yesu, pa mwambowu pankakhala vinyo komanso pankaimbidwa nyimbo.​—Mateyu 26:19, 30; Luka 22:15-18.

Maganizo olakwika okhudza mwambo wa Pasika

 Maganizo olakwika: Aisiraeli ankadya Pasika pa Nisani 15.

 Zoona zake: Mulungu analamula Aisiraeli kuti azipha mwana wa nkhosa pa Nisani 14 dzuwa likangolowa ndipo ankafunika kudya nyama yake usiku womwewo. (Ekisodo 12:6, 8) Aisiraeli ankaona kuti tsiku linkayamba komanso kutha dzuwa likamalowa. (Levitiko 23:32) Choncho Aisiraeli ankapha mwana wa nkhosa komanso kudya nyama yake, tsiku la Nisani 14 likangoyamba.

 Maganizo olakwika: Akhristu amafunika kuchita mwambo wa Pasika.

 Zoona zake: Yesu atangomaliza kuchita mwambo wa Pasika pa Nisani 14 mu 33 C.E., anayambitsa mwambo watsopano wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye. (Luka 22:19, 20; 1 Akorinto 11:20) Mwambo watsopanowu unalowa m’malo mwa Pasika. Panopa timakumbukira ‘Khristu amene anaperekedwa monga nsembe yathu ya pasika.’ (1 Akorinto 5:7) Nsembe ya dipo ya Yesu ndi yofunika kwambiri kuposa Pasika chifukwa imapulumutsa anthu onse ku ukapolo wa uchimo komanso imfa.​—Mateyu 20:28; Aheberi 9:15.

a Pamene nthawi inkapita, zinthu zina zinasintha. Mwachitsanzo, pamene Aisiraeli ankachita mwambo woyamba, anauzidwa kuti adzauchite “mofulumira” chifukwa ankafunika kukonzekera zochoka ku Iguputo. (Ekisodo 12:11) Komabe atafika ku Dziko Lolonjezedwa, Aisiraeli sankafunikanso kuchita zinthu mofulumira ngati poyamba.