Pitani ku nkhani yake

Kodi Nyanja ya Moto N’chiyani? Kodi ndi Yofanana ndi Gehena?

Kodi Nyanja ya Moto N’chiyani? Kodi ndi Yofanana ndi Gehena?

Yankho la m’Baibulo

 Mawu akuti nyanja ya moto akuimira kuwonongedwa kotheratu. Mawuwa ndi ofanana ndi Gehena koma ndi osiyana ndi manda a anthu onse.

Si nyanja yeniyeni

 Mavesi onse 5 m’Baibulo amene amatchula za “nyanja ya moto” amasonyeza kuti nyanjayi si yeniyeni koma ndi yophiphiritsa. (Chivumbulutso 19:20; 20:10, 14, 15; 21:8) Mavesi osiyanasiyana amasonyeza kuti zinthu zotsatirazi zidzaponyedwa m’nyanja ya moto:

Nyanja ya moto ikuimira kuwonongedwa kotheratu

 Baibulo limanena kuti nyanja ya moto imeneyi “ikuimira imfa yachiwiri.” (Chivumbulutso 20:14; 21:8) Imfa yoyambirira imene Baibulo limatchula inayamba chifukwa cha kuchimwa kwa Adamu. Mulungu adzagonjetsa imfa imeneyi akadzaukitsa anthu amene anamwalira ndipo kenako adzaithetsa.​—1 Akorinto 15:21, 22, 26.

Anthu amene amapita kunyanja ya moto yophiphiritsa sadzaukitsidwa

 Koma nyanja ya moto ikuimira imfa ina, kapena kuti imfa yachiwiri. Ngakhale kuti anthu amene amwalira pa imfa yachiwiriyi nawonso sadziwa chilichonse, Baibulo silinena chilichonse kuti adzaukitsidwa. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti Yesu ali ndi “makiyi a imfa ndi a Manda.” Izi zikusonyeza kuti iye ali ndi mphamvu zoukitsa anthu amene anamwalira chifukwa cha tchimo la Adamu. (Chivumbulutso 1:18; 20:13) Koma Baibulo silinena kuti Yesu, kapena wina aliyense, ali ndi makiyi a kunyanja ya moto. Choncho nyanja ya moto imeneyi ikuimira chilango chachikulu chomwe ndi kuwonongedwa kotheratu.​—2 Atesalonika 1:9.

Nyanja ya moto n’chimodzimodzi ndi Gehena, kapena kuti Chigwa cha Hinomu

 Mawu akuti Gehena (m’Chigiriki geʹen·na) anatchulidwa nthawi zokwana 6 m’Baibulo. Mofanana ndi nyanja ya moto, mawu akuti Gehena akuimira chiwonongeko chotheratu. Ngakhale kuti mawu akuti Gehena anamasuliridwa kuti “helo” m’Mabaibulo ena, Gehena ndi wosiyana ndi helo (m’Chiheberi sheʼohlʹ, m’Chigiriki haiʹdes).

Chigwa cha Hinomu

 Mawu akuti “Gehena” amatanthauza “Chigwa cha Hinomu.” Chigwa chimenechi chinali kunja kwa mzinda wa Yerusalemu. Kale, anthu a mumzinda wa Yerusalemu ankataya zinyalala zawo kuchigwa chimenechi. Nthawi zonse kuchigwa chimenechi kunkayaka moto kuti uziwotcha zinyalalazo, ndipo mphutsi zinkadya chilichonse chimene sichinawotchedwe ndi moto.

 Yesu anagwiritsa ntchito mawu akuti Gehena mophiphiritsira ponena za chiwonongeko chotheratu. (Mateyu 23:33) Pofotokoza zimene zimachitika ku Gehena, Yesu anati “mphutsi za mitembo sizifa ndipo moto wake suzima.” (Maliko 9:47, 48) Zimene Yesu ananenazi zikugwirizana ndi ulosi umene Yesaya ananena, wokhudza Chigwa cha Hinomu. Ulosiwu umati: “Iwo adzapita kukaona mitembo ya anthu amene anali kuphwanya malamulo anga, pakuti mphutsi zodya mitemboyo sizidzafa. Moto woinyeketsa sudzazima.” (Yesaya 66:24) Fanizo la Yesuli likusonyezeratu kuti mawu akuti Gehena akuimira chiwonongeko chotheratu, osati kuzunzidwa. M’fanizoli, mphutsi zikudya mitembo, osati anthu amoyo. Nawonso moto ukunyeketsa mitembo, osati anthu amoyo.

 Baibulo silisonyeza kuti anthu opita ku Gehena adzaukitsidwa. Choncho “nyanja ya moto” komanso “Gehena wamoto” zikuimira chiwonongeko chotheratu.​—Chivumbulutso 20:14, 15; 21:8; Mateyu 18:9.

Kodi mawu akuti “adzazunzidwa usana ndi usiku kwamuyaya” akutanthauza chiyani?

 Ngati nyanja ya moto ikuimira chiwonongeko chotheratu, n’chifukwa chiyani Baibulo limanena kuti Mdyerekezi, chilombo, ndiponso mneneri wonyenga “adzazunzidwa usana ndi usiku kwamuyaya”? (Chivumbulutso 20:10) Taonani zifukwa 4 zosonyeza kuti kuzunzidwa kumene kukutchulidwa palembali n’kophiphiritsa:

  1.   Kuti Mdyerekezi azunzidwe kwamuyaya, zingafunike kuti akhale ndi moyo kwamuyayanso. Koma Baibulo limanena kuti iye adzawonongedwa, kapena kuti sadzakhalaponso.​—Aheberi 2:14.

  2.   Moyo wosatha ndi mphatso yochokera kwa Mulungu, osati chilango.​—Aroma 6:23.

  3.   Chilombo ndiponso mneneri wonyenga ndi zinthu zophiphiritsa, choncho sizingazunzidwe.

  4.   Baibulo limasonyeza kuti kuzunzidwa kwa Mdyerekezi kukutanthauza kuti adzawonongedwa kotheratu ndipo sadzavutitsanso anthu.

 Mawu amene m’Baibulo anawamasulira kuti “kuzunzidwa” angatanthauzenso “kulepheretsedwa kuchita zinazake.” Mwachitsanzo, mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “oyang’anira ndende” palemba la Mateyu 18:34, amawamasuliranso kuti “azunzi” m’Mabaibulo ena. Zimenezi zikusonyeza bwino kugwirizana kumene kulipo pakati pa mawu akuti “kuzunzidwa” ndi “kulepheretsedwa kuchita zinazake.” Komanso nkhani yopezeka pa Mateyu 8:29 ndi pa Luka 8:30, 31, imasonyeza kugwirizana kwa mawu akuti ‘kuzunzidwa’ ndi ‘phompho.’ Mawu onsewa akuimira malo ophiphiritsira, kumene munthu sangathe kuchita chilichonse, kapena kuti imfa. (Aroma 10:7; Chivumbulutso 20:1, 3) Ndipotu m’buku la Chivumbulutso muli mawu angapo akuti “kuzunzidwa” ndiponso “zunza” omwe anawagwiritsa ntchito mophiphiritsa.​—Chivumbulutso 9:5; 11:10; 18:7, 10.