Pitani ku nkhani yake

KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO

Aroma 10:13​—“Adzaitana pa Dzina la Ambuye”

Aroma 10:13​—“Adzaitana pa Dzina la Ambuye”

 “Aliyense amene adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.”​—Aroma 10:13, Baibulo la Dziko Latsopano.

 “Amene ali yense adzaitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.”​—Aroma 10:13, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Tanthauzo la Aroma 10:13

 Mulungu alibe tsankho ndipo amapatsa aliyense mwayi woti adzapulumuke n’kukhala ndi moyo wosatha. Amachita zimenezi mosatengera dziko limene munthu amachokera, mtundu wake, udindo wake kapena ndalama zimene ali nazo. Koma kuti tidzapulumuke, tiyenera kuitana pa dzina la Yehova, lomwe ndi dzina lenileni la Mulungu Wamphamvuyonse. a​—Salimo 83:18.

 M’Baibulo, mawu oti ‘kuitana pa dzina la Yehova’ amatanthauza zambiri osati kungodziwa chabe dzina la Mulunguli n’kumaligwiritsa ntchito pomulambira. (Salimo 116:12-14) Koma amatanthauzanso kumukhulupirira ndiponso kumudalira kuti azitithandiza.​—Salimo 20:7; 99:6.

 Dzina la Mulungu linali lofunika kwambiri kwa Yesu Khristu. Paja mawu oyambirira a m’pemphero lake lachitsanzo anali akuti: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.” (Mateyu 6:9) Yesu anasonyezanso kuti tiyenera kumudziwa Yehova, kumumvera komanso kumukonda kuti tidzapeze moyo wosatha.​—Yohane 17:3, 6, 26.

 N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova ndi “Ambuye” amene anatchulidwa mu Aroma 10:13 m’Baibulo la Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu? Tingatero chifukwa chakuti vesili likugwira mawu ochokera mu Yoweli 2:32 omwe amatchula dzina lenileni la Mulungu m’Chiheberi, osati dzina laudindo lakuti “Ambuye.” b

Nkhani Yonse ya Aroma 10:13

 Pa Aroma chaputala 10, Baibulo limasonyeza kuti munthu ayenera kukhulupirira Yesu Khristu kuti akhale pa ubwenzi ndi Mulungu. (Aroma 10:9) Mawu ambiri ochokera m’Malemba amene amadziwika kuti Chipangano Chakale anagwidwa posonyeza kuti mfundoyi ndi yoona. Munthu amasonyeza kuti ali ndi chikhulupiriro ngati “amalengeza poyera” uthenga wabwino wokhudza chipulumutso kwa anthu osakhulupirira. Akamatero, anthu ena amapatsidwa mpata wokhala ndi chikhulupiriro chimene chingawathandize kuti adzapulumuke.​—Aroma 10:10, 14, 15, 17.

Werengani Aroma chaputala 10, mawu am’munsi ndi malifalensi ake.

a Dzina la Mulungu limapezeka m’makope akalekale a Baibulo nthawi zoposa 7,000. M’Chiheberi dzinali limalembedwa ndi zilembo 4. Nthawi zambiri, dzinali limamasuliridwa kuti “Yehova” m’Chichewa koma akatswiri ena amakonda kulimasulira kuti “Yahweh.”

b Akhristu olemba Baibulo ayenera kuti ankagwiritsa ntchito dzina lenileni la Mulungu pogwira mawu okhala ndi dzinali ochokera m’Malemba amene amadziwika kuti Chipangano Chakale. Buku lina lofotokoza mawu a m’Baibulo amati: “Pali umboni wakuti dzina la Mulungu lolembedwa m’zilembo 4 za Chiheberi, kapena kuti dzina loti Yahweh, linapezeka m’mawu onse kapena m’mawu ena omwe anagwidwa m’Chipangano Chatsopano kuchokera m’Chipangano Chakale pamene Chipangano Chatsopanocho chinalembedwa.” (The Anchor Bible Dictionary, Voliyumu 6, tsamba 392) Kuti mudziwe zambiri, onani “Dzina la Mulungu M’Malemba Achigiriki” mu Kabuku Kothandiza Kuphunzira Mawu a Mulungu, mutu 2.