Pitani ku nkhani yake

KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO

Mateyu 6:33​—“Pitirizani Kufunafuna Ufumu Choyamba”

Mateyu 6:33​—“Pitirizani Kufunafuna Ufumu Choyamba”

 “Chotero pitirizani kufunafuna ufumu choyamba ndi chilungamo chake, ndipo zina zonsezi zidzawonjezedwa kwa inu.”​—Mateyu 6:33, Baibulo la Dziko Latsopano.

 “Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.”​—Mateyu 6:33, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Tanthauzo la Mateyu 6:33

 Ufumu wa Mulungu ndi boma lakumwamba lomwe lidzakwaniritse zimene Mulungu akufuna kuti zichitike padzikoli. (Mateyu 6:9, 10) Munthu amafunafuna Ufumu choyamba akamaona kuti Ufumuwo ndi chinthu chofunika kwambiri pa moyo wake. a Amafunitsitsanso kuphunzira za Ufumu wa Mulungu komanso kuuza anthu ena zinthu zabwino zimene Ufumuwo udzachite. (Mateyu 24:14) Munthu amene amafunafuna Ufumu amapempheranso kuti Ufumuwo ubwere.​—Luka 11:2.

 Chilungamo cha Mulungu chimaphatikizapo mfundo zake za makhalidwe abwino. (Salimo 119:172) Choncho munthu amafunafuna chilungamo cha Mulungu akamatsatira malamulo a Mulungu okhudza makhalidwe abwino. Akamachita zimenezi zinthu zimamuyendera bwino.​—Yesaya 48:17.

 Mawu oti zina zonsezi zidzawonjezedwa kwa inu ndi lonjezo la Mulungu loti iye adzasamalira anthu omwe amaika Ufumu wake komanso mfundo zake pamalo oyamba.​—Mateyu 6:31, 32.

Nkhani yonse ya Mateyu 6:33

 Yesu ananena mawu amenewa pa ulaliki wake wapaphiri womwe umapezeka mu Mateyu chaputala 5 mpaka 7. N’zosakayikitsa kuti anthu ambiri amene ankamvetsera Yesu anali osauka. Mwina ankaona kuti ankayenera kugwiritsa ntchito nthawi yawo yambiri pofunafuna zofunika pa moyo moti anali ndi nthawi yochepa yoti afunefune Ufumu. Koma Yesu anawalimbikitsa kuti aone mmene Mulungu amasamalirira zomera ndi zinyama. Mulungu amalonjeza kuti azisamaliranso anthu amene amafunafuna Ufumu wake choyamba.​—Mateyu 6:25-30.

Maganizo Olakwika Okhudza Mateyu 6:33

 Maganizo olakwika: Munthu amene amafunafuna Ufumu adzalemera.

 Zoona zake: Yesu ananena kuti anthu amene amaika Ufumu wa Mulungu pamalo oyamba adzakhala ndi zofunika zawo, monga chakudya ndi zovala. (Mateyu 6:25, 31, 32) Koma sanalonjeze kuti adzakhala ndi zinthu zapamwamba. Sananenenso kuti chuma chimene munthu ali nacho n’chimene chimasonyeza kuti Mulungu akumudalitsa. Ndipotu Yesu anachenjeza anthu kuti asamafunefune chuma chifukwa zingawalepheretse kufunafuna Ufumu choyamba. (Mateyu 6:19, 20, 24) Mtumwi Paulo ankadzipereka kwambiri pa ntchito za Ufumu wa Mulungu koma nthawi zina ankasowa zinthu. Mofanana ndi Yesu, iye anachenjeza anthu za zinthu zoopsa zimene zingachitike munthu akamayesetsa kupeza chuma.​—Afilipi 4:11, 12; 1 Timoteyo 6:6-10.

 Maganizo olakwika: Akhristu sayenera kugwira ntchito kuti azipeza zofunika pa moyo.

 Zoona zake: Baibulo limanena kuti Akhristu ayenera kumagwira ntchito kuti azipeza zofunika pa moyo za iwowo komanso za mabanja awo. (1 Atesalonika 4:11, 12; 2 Atesalonika 3:10; 1 Timoteyo 5:8) Yesu sananene kuti otsatira ake azifunafuna Ufumu wokha, koma ananena kuti azifunafuna Ufumu choyamba.

 Anthu amene amafunafuna Ufumu wa Mulungu choyamba komanso ndi ofunitsitsa kumagwira ntchito, angadalire kuti Mulungu aziwathandiza kupeza zinthu zofunika pa moyo.​—1 Timoteyo 6:17-19.

a Mawu oti “pitirizani kufunafuna” anamasuliridwa kuchokera ku mawu a Chigiriki amene amasonyeza chinthu chimene munthu sasiya kuchita. Ndiye mawuwo angamasuliridwenso kuti “muzifunafuna nthawi zonse.” Choncho Ufumu uyenera kukhala patsogolo pa moyo wathu osati chinthu chimene timachita nacho chidwi pa kanthawi kenako n’kusiya.