Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Matanthauzo a Mawu Ena a m’Baibo

A B C D G K M N T U W

A

  • Afarisi.

    Kagulu kochuka ka cipembedzo ca Ciyuda ka m’nthawi ya atumwi. Afarisi sanali a m’banja la ansembe, koma anali kutsatila kwambili Cilamulo, kuphatikizapo tumfundo tung’ono-tung’ono twa m’Cilamulo. Iwo anali kuona miyambo ya makolo kukhala yofunika kwambili mofanana na Cilamulo, ndipo anali kuitsatilanso mosamalitsa kwambili. (Mt 23:23) Sanali kulola kutengela cikhalidwe ca Agiriki mwanjila ina iliyonse. Ndipo popeza anali akatswili a Cilamulo komanso miyambo, anali na ulamulilo waukulu pa anthu. (Mt 23:2-6) Afarisi ena anali mamembala a Khoti Yaikulu ya Ayuda. Nthawi zambili iwo anali kutsutsa Yesu pa nkhani yosunga Sabata, miyambo, ndiponso pa nkhani ya kugwilizana na ocimwa komanso okhometsa misonkho. Afarisi ena pambuyo pake anakhala Akhristu, kuphatikizapo Saulo wa ku Tariso.—Mt 9:11; 12:14; Mko 7:5; Lu 6:2; Mac 26:5.

  • Asaduki.

    Kagulu kochuka ka Ciyuda ka anthu olemela, olemekezeka, komanso ansembe amene anali na ulamulilo waukulu pa zocitika za pa kacisi. Iwo anali kukana miyambo yambili ya makolo imene Afarisi anali kutsatila komanso zikhulupililo zina za Afarisi. Sanali kukhulupilila kuti akufa adzauka kapena kuti kuli angelo. Asaduki anali kutsutsa Yesu.—Mt 16:1; Mac 23:8.

B

  • Belezebule.

    Dzina lina la Satana, kalonga kapena kuti wolamulila wa ziŵanda. N’kutheka kuti dzinali linacokela ku dzina la Baala wochedwa Baala-zebabu, mulungu amene Afilisiti anali kulambila ku Ekironi.—2Mf 1:3; Mt 12:24.

C

  • Cigololo.

    Mwamuna wokwatila kapena mkazi wokwatiwa kugonana mocita kufuna na munthu wina amene si mnzake wa m’cikwati.—Eks 20:14; Mt 5:27; 19:9.

  • Cimalizilo ca nthawi ino.

    Nthawi yokatifikitsa pa mapeto a dongosolo lino la zinthu, lolamulidwa na Satana. Nthawi imeneyi ndiyonso nthawi ya kukhalapo kwa Khristu. Motsogoleledwa na Yesu, angelo adzapita “kukacotsa oipa pakati pa olungama” n’kuwawononga. (Mt 13:40-42, 49) Ophunzila a Yesu anali kufuna kudziŵa kuti nthawi ya “cimalizilo” imeneyi idzakhalapo liti. (Mt 24:3) Yesu asanabwelele kumwamba, analonjeza otsatila ake kuti adzakhala nawo mpaka nthawi imeneyi.—Mt 28:20

  • Ciwelewele.

    Liwu lomasulidwa kucokela ku liwu la Cigiriki lakuti por·neiʹa. M’Malemba, liwuli limagwilitsidwa nchito ponena za mcitidwe uliwonse wa zakugonana umene Mulungu amaletsa. Ciwelewele cimaphatikizapo cigololo, uhule, kugonana kwa anthu osakwatilana, mathanyula, komanso kugona nyama. M’buku la Civumbulutso, liwu limeneli limagwilitsidwa nchito mophiphilitsa ponena za hule lauzimu lochedwa “Babulo Wamkulu” cifukwa cogwilizana na olamulila a dzikoli pofuna kukhala na ulamulilo komanso cuma.—Chv 14:8; 17:2; 18:3; Mt 5:32; Mac 15:29; Aga 5:19.

D

  • Dipo.

    Malipilo opelekedwa kuti munthu amasulidwe ku ukapolo, ku mavuto, komanso ku ucimo. Dipo lingatanthauzenso malipilo opelekedwa kuti munthu amasuke ku udindo wocita zinazake, kapenanso kuti munthu woyenela kulandila cilango asalangidwe. Malipilowo sanali kukhala ndalama nthawi zonse. (Yes. 43:3) Dipo linali kupelekedwa pa zocitika zosiyana-siyana. Mwacitsanzo, ana onse aamuna oyamba kubadwa a anthu kapena a ziŵeto mu Isiraeli anali a Yehova, ndipo anali kufunika kumagwila nchito yake basi. Conco, anali kufunika kuwapelekela dipo kuti amasuke ku utumiki umenewo. (Nu 3:45, 46; 18:15, 16) Ngati ng’ombe yaikali sinayang’anilidwe bwino ndipo yapha munthu, mwiniwake ng’ombeyo anali kufunika kupeleka dipo kuti asaphedwe. (Eks 21:29, 30) Koma panalibe dipo lowombolela munthu wopha mnzake mwadala. (Num. 35:31) Baibo imakamba za dipo lofunika kwambili limene Khristu anapeleka pololela kufa kuti amasule anthu omvela ku ucimo na imfa.—Sl 49:7, 8; Mt 20:28; Aef 1:7.

  • Dzombe.

    Mtundu wa ziwala zimene zimayenda m’magulu akulu-akulu. M’Cilamulo ca Mose, dzombe linali cakudya cosadetsedwa. Nthawi zina, dzombe linali kuwononga zinthu kwambili mwa kudya zomela zilizonse zimene lapeza. Zikakhala telo, anthu anali kuona kuti umenewo ni mlili wa dzombe.—Eks 10:14; Mt 3:4.

G

  • Gehena.

    Dzina la Cigiriki la Cigwa ca Hinomu, comwe cinali kum’mwela komanso kum’mwela ca kumadzulo kwa mzinda wamakedzana wa Yerusalemu. (Yer 7:31) Ulosi wina unakamba kuti mitembo idzaponyedwa kumeneko. (Yer 7:32; 19:6) Palibe umboni uliwonse wakuti nyama kapena anthu anali kuponyedwa ku Gehena kuti atenthedwe kapena kuzunzika ali amoyo. Conco Gehena sitanthauza malo osaoneka kumene anthu amoyo amakazunzika m’moto weniweni kwamuyaya. Koma Yesu na ophunzila ake anagwilitsa nchito mawu akuti Gehena mophiphilitsa pokamba za cilango ca “imfa yaciŵili,” kutanthauza ciwonongeko cothelatu.—Chv 20:14; Mt 5:22; 10:28.

K

  • Kukhalapo.

    M’mavesi ena a Malemba a Cigiriki a Cikhristu, liwu limeneli limakamba za nthawi ya kukhalapo kwa Yesu Khristu monga mfumu, kucokela pamene anaikidwa kukhala Mfumu kumwamba mpaka pa mapeto a masiku otsiliza a nthawi ino. Nthawi ya kukhalapo kwa Khristu si nthawi yocepa imene iye adzabwela n’kubwelelanso mwamsanga ayi, koma ni nthawi yaitali.—Mt 24:3.

M

  • Mankhusu.

    Makoko a mbewu monga mpunga kapena tiligu amene amacotsedwa popuntha kapena pouluza mbewuzo. Liwu lakuti mankhusu limagwilitsidwa nchito mophiphilitsa potanthauza zinthu zopanda nchito komanso zosafunika.—Sl 1:4; Mt 3:12.

  • Mkulu wa ansembe.

    M’Cilamulo ca Mose, ameneyu anali wansembe wamkulu amene anali kuimila anthu pamaso pa Mulungu komanso kuyang’anila ansembe anzake. Anali kuchedwanso “wansembe wamkulu.” (2Mb 26:20; Eza 7:5) Iye yekha ndiye anali kuloledwa kuloŵa m’Malo Opatulika Koposa, kutanthauza m’cipinda camkatikati ca cihema, ndipo pambuyo pake m’cipinda camkatikati ca kacisi. Iye anali kuloŵamo kamodzi cabe pa caka pa Tsiku Lophimba Macimo. Yesu Khristu nayenso amachedwa “mkulu wa ansembe.”—Le 16:2, 17; 21:10; Mt 26:3; Ahe 4:14.

  • Mnazareti.

    Dzina limene Yesu anali kudziŵika nalo cifukwa cakuti kwawo kunali ku tauni ya Nazareti. Mwacionekele, liwuli lifanana na liwu la Ciheberi lomasulidwa kuti “mphukila” pa Yesaya 11:1. Pambuyo pake, otsatila a Yesu nawonso anayamba kuchedwa na dzinali.—Mt 2:23; Mac 24:5.

  • Mphatso za cifundo.

    Mphatso zopelekedwa kwa wosauka kuti zimuthandize. Mphatso zimenezi sizichulidwa mwacindunji m’Malemba a Ciheberi. Koma kupitila m’Cilamulo, Mulungu anapeleka malangizo omveka bwino kwa Aisiraeli ofotokoza udindo wawo pothandiza osauka.—Mt 6:2.

  • Mtengo wozunzikilapo.

    Mawu amenewa anamasulidwa kucokela ku liwu la Cigiriki lakuti stau·rosʹ, limene limatanthauza mtengo wowongoka monga umene anaphelapo Yesu. Palibe umboni uliwonse wakuti liwu la Cigiriki limeneli limatanthauza mtanda, monga umene anthu akunja anali kugwilitsa nchito ngati cizindikilo ca cipembedzo kwa zaka mahandiledi Yesu asanabwele pa dziko lapansi. Mawu akuti “mtengo wozunzikilapo” amamveketsa bwino tanthauzo la liwu la Cigiriki lakuti stau·rosʹ, cifukwa cakuti liwuli limagwilitsidwanso nchito poonetsa kuti otsatila a Yesu adzazunzidwa, kuvutika, na kucititsidwa manyazi. (Mt 16:24; Ahe 12:2).

  • Mwana wa munthu.

    Mawu amenewa amapezeka maulendo pafupifupi 80 m’mabuku a Uthenga Wabwino. Amakamba za Yesu Khristu, ndipo amaonetsa kuti iye atabadwa anakhala munthu weniweni, osati mngelo wovala thupi la munthu. Mawuwa amaonetsanso kuti Yesu anali kudzakwanilitsa ulosi wa pa Danieli 7:13, 14. M’Malemba a Ciheberi, mawu akuti mwana wa munthu anagwilitsidwa nchito pochula Ezekieli na Danieli pofuna kuonetsa kuti iwo anali cabe anthu olankhulilako Mulungu polengeza uthenga wake.—Eze 3:17; Da 8:17; Mt 19:28; 20:28.

N

  • Nthawi.

    Liwu limeneli linamasulidwa kucokela ku liwu la Cigiriki lakuti ai·onʹ likamanena za zinthu kapena zocitika za pa nyengo inayake zimene zimapangitsa nyengoyo kukhala yapadela. Baibo imagwilitsa nchito mawu akuti “nthawi ino” pofotokoza mmene zinthu zikuyendela padzikoli kuphatikizapo makhalidwe na zocita za anthu a m’dzikoli. (2Ti 4:10) Kupitila m’Cipangano ca Cilamulo, Mulungu anayambitsa nthawi imene ena angaiche nthawi ya Aisiraeli kapena kuti ya Ayuda. Pamene Yesu Khristu anapeleka moyo wake monga nsembe ya dipo, Mulungu anamugwilitsa nchito poyambitsa nthawi ina yosiyana, imene imakhudza kwambili mpingo wa Akhristu odzozedwa. Ici cinali ciyambi ca nthawi yatsopano ya zinthu zenizeni zimene zinali kuimilidwa na zinthu za m’Cilamulo. Mawu akuti nthawi angagwilitsidwenso nchito pofotokoza nyengo zosiyana-siyana, kapena mmene zinthu zakhala zikuyendela, mmene zilili pali pano, komanso mmene zidzakhalila kutsogolo.—Mt 24:3; Mko 4:19; Aro 12:2; 1Ak 10:11.

T

  • Tsiku la Ciweluzo.

    Tsiku kapena nthawi imene magulu a anthu, mitundu, kapena anthu onse adzaweluzidwa na Mulungu. Ingakhale nthawi pamene anthu oweluzidwa kuti ayenela kuphedwa, adzawonongedwa, kapena pamene anthu ena adzapatsidwa mwayi wopulumuka kuti akhale na moyo wamuyaya. Yesu Khristu na atumwi ake anakamba za “Tsiku la Ciweluzo” la kutsogolo, limene ni nthawi pamene anthu amoyo komanso amene anafa adzaweluzidwa.—Mt 12:36.

U

  • Ubatizo; Kubatiza.

    Kubatiza kumatanthauza “kumiza,” kapena kuti kuviika m’madzi. Yesu analamula kuti otsatila ake ayenela kubatizidwa. Ena mwa maubatizo amene Malemba amachula ni ubatizo wa Yohane, kubatizidwa na mzimu woyela, komanso kubatizidwa na moto.—Mt 3:11, 16; 28:19; Yoh 3:23; 1Pe 3:21.

W

  • Wansembe wamkulu.

    Mawu ena otanthauza “mkulu wa ansembe” m’Malemba a Ciheberi. Zioneka kuti m’Malemba a Cigiriki a Cikhristu, mawu akuti “ansembe aakulu” anali kutanthauza amuna a udindo waukulu m’gulu la ansembe, mwina kuphatikizapo amene kale anali akulu a ansembe komanso atsogoleli a zigawo 24 za ansembe.—2Mb 26:20; Eza 7:5; Mt 2:4; Mko 8:31.

  • Woipayo.

    Dzina la Satana Mdyelekezi, amene amatsutsa Mulungu komanso mfundo zake zolungama.—Mt 6:13; 1Yo 5:19.

  • Wokhulupilila nyenyezi.

    Munthu amene amayang’ana kayendedwe ka dzuŵa, mwezi, na nyenyezi pofuna kukambilatu zimene zidzacitika kutsogolo.—Da 2:27; Mt 2:1.