Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 26

Tingacite Ciani Kuti Tisamalile Nyumba Yathu ya Ufumu?

Tingacite Ciani Kuti Tisamalile Nyumba Yathu ya Ufumu?

Ku Estonia

Ku Zimbabwe

Ku Mongolia

Ku Puerto Rico

Nyumba ya Ufumu iliyonse ya Mboni za Yehova imalengeza dzina loyela la Mulungu. Conco, timaona kuti ni mwai kuthandiza pa nchito yoyeletsa ndi kuisamalila kuti izioneka bwino, ndi kuti nchito imeneyi ni mbali yofunika kwambili pa kulambila kwathu koona. Tonse tili aufulu kuthandiza pa nchito yoyeletsa imeneyi.

Mungadzipeleke kuti muyeletse pambuyo pa misonkhano. Pambuyo pa msonkhano, abale ndi alongo amadzipeleka kuyeletsa Nyumba ya Ufumu patali-patali. Ndipo kamodzi pa wiki, amaiyeletsa bwino-bwino. Mkulu kapena mtumiki wothandiza amayang’anila nchito imeneyi, ndipo amatsatila mndandanda wa zinthu zofunika kucita. Malinga ndi nchito zimene zilipo, abale ndi alongo amadzipeleka kupyanga, kukolopa, kupukuta-pukuta, ndi kuika bwino mipando. Ena amayeletsa zimbudzi ndi kuthilamo mankhwala, amatsuka mawindo ndi magalasi odziyang’anapo, amataya zinyalala, kapena kuyeletsa panja. Kamodzi pa caka, pamakhala nchito yaikulu yoyeletsa malo onse. Mwa kugwila nchito imeneyi pamodzi ndi ana athu, timawaphunzitsa kuti azilemekeza malo athu olambilila.—Mlaliki 5:1.

Thandizani kukonza zinthu zoonongeka. Kamodzi pa caka, Nyumba ya Ufumu amaiona mwatsatane-tsatane kunja ndi mkati ngati pali zina zoonongeka. Malinga ndi zimene apeza, pamakhala nchito yokonza zinthu kaŵili-kaŵili kuti holo izioneka bwino. Zimenezi zimathandiza kuti asaziononga ndalama zambili. (2 Mbiri 24:13; 34:10) Nyumba ya Ufumu yaukhondo ndi yosamalidwa bwino ni malo abwino kulambililamo Mulungu wathu. Mwa kugwila nchito imeneyi, timaonetsa kuti timakonda Yehova ndi malo athu olambilila. (Salimo 122:1) Zimenezi zimapeleka cithunzi cabwino kwa anthu onse a m’dela limenelo.—2 Akorinto 6:3.

  • N’cifukwa ciani sitiyenela kunyalanyaza malo athu olambilila?

  • Kodi pamakhala makonzedwe otani kuti Nyumba ya Ufumu izikhala yaukhondo?