Onani zimene zilipo

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | KULELA ANA

Kuphunzitsa Mwana Wanu Nkhani Zokhudza Kugonana

Kuphunzitsa Mwana Wanu Nkhani Zokhudza Kugonana

VUTO LIMENE LIMAKHALAPO

Kale ana anali kuyambila kumva kwa makolo awo nkhani zokhudza kugonana ndipo makolowo anali kuwaphunzitsa nkhanizi mwapang’ono-pang’ono mogwilizana na msinkhu wawo.

Koma masiku ano zinthu zinasintha. Izi zili conco cifukwa ca zimene buku lina limanena. Limati: “Masiku ano ana aang’ono kwambili amatha kuona zinthu zolaula cifukwa zinthu zokhudza kugonana zayamba kuculuka mu zinthu zimene ana amaŵelenga kapena kuonelela.” (The Lolita Effect) Kodi zimenezi zimathandiza anawo kapena zimawasokoneza?

ZIMENE MUYENELA KUDZIŴA

Zinthu zolaula zili paliponse. Wolemba mabuku wina, dzina lake Deborah Roffman, analemba kuti: “Zinthu zolaula komanso mawu okhudza kugonana zikupezeka m’mafilimu, mabuku, nyimbo, mapulogalamu a pa TV, mameseji, masewela, zikwangwani, zithunzi zapakompyuta kapena pafoni komanso m’zimene anthu amalankhula akamaceza kapena kutsatsa malonda. Izi zimacititsa kuti [acinyamata ndiponso ana aang’ono] aziona kuti kugonana . . . ni kofunika kwambili pa moyo wawo kuposa ciliconse.”—Talk to Me First.

Otsatsa malonda nawonso akusokoneza acinyamata. Anthu ogulitsa zinthu amatsatsa zovala za ana zowacititsa kuti azioneka mokopa ena. Zimenezi zimaphunzitsa ana kuti aziganizila kwambili za maonekedwe awo. Buku lina limati: “Otsatsa malonda amakonda kukopa ana cifukwa amadziŵa kuti akhoza kutengeka mosavuta. Koma sikuti amagwilitsa nchito zinthu zokhudza kugonana n’colinga coti anawo azilakalaka kugonana koma kuti angogulitsa zimene akutsatsazo.”—So Sexy So Soon.

Kungodziŵa zinthu si kokwanila. Kungodziŵa mmene galimoto imagwilila nchito sikutanthauza kuti mungakhale woyendetsa wodalilika. N’cimodzi-modzinso na kudziŵa nkhani zokhudza kugonana. Kungodziŵa nkhani zimenezi sikutanthauza kuti mungasankhe zinthu mwanzelu pa nkhaniyi.

Mfundo yofunika kwambili: Masiku ano n’kofunika kwambili kuti muziphunzitsa ana anu kuti azigwilitsa nchito “mphamvu zawo za kuzindikila” n’colinga coti azitha “kusiyanitsa coyenela ndi cosayenela.”—Aheberi 5:14.

ZIMENE MUNGACITE

Muzikambilana nawo. Mwina zingakhale zovuta kukambilana na ana ŵanu nkhani zokhudza kugonana. Komabe muyenela kudziŵa kuti ni udindo wanu ndipo muyenela kuukwanilitsa.Lemba lothandiza: Miyambo 22:6.

Musamawapanikize na zinthu zambili-mbili nthawi imodzi. M’malo mokambilana kwa nthawi yaitali, muziyesetsa kulankhula nawo moceza mukamayenda kapena kugwila nchito inayake. Muziwafunsa mafunso othandiza kuti amasuke n’kumakuuzani zakukhosi kwawo. Mwacitsanzo, m’malo mongofunsa kuti, “Kodi iwe umakonda zithunzi ngati zimenezo?” ni bwino kufunsa kuti, “Kodi ukuganiza kuti n’cifukwa ciani anthu amagwilitsa nchito zithunzi ngati zimenezo potsatsa malonda?” Akayankha, mungamufunsenso kuti, “Nanga iwe umaziona bwanji?”—Lemba lothandiza: Deuteronomo 6:6, 7.

Muzikambilana nawo mogwilizana na msinkhu wawo. Mungaphunzitse ana aang’ono mayina olondola a ziwalo zogonanila komanso zimene angacite podziteteza kwa anthu ogwililila ana. Ana akamakula makolo angawaphunzitse zinthu zosavuta kumvetsa zokhudza kugonana ndiponso kubeleka ana. Koma anawo asanathe msinkhu, makolo ayenela kuwathandiza kuti amvetse bwino zinthu zambili zokhudza kugonana komanso mmene angasankhile zinthu mwanzelu pa nkhaniyi.

Muziwaphunzitsa makhalidwe abwino. Makolo ayenela kuphunzitsa ana awo kuyambila ali aang’ono makhalidwe abwino monga kulankhula zoona, kukhala okhulupilika komanso kulemekeza anthu ena. Kucita zimenezi kungathandize kuti anawo akadzaphunzitsidwa za kugonana adzamvetse zoyenela kucita na zosayenela kucita pa nkhaniyi. Makolo ayenelanso kuuza ana awo mosapita m’mbali mfundo zimene amayendela pa nkhaniyi. Mwacitsanzo, ayenela kuwauza ngati amaona kuti n’kulakwa kuti munthu agonane na wina asanalowe m’banja. Ayenelanso kuwafotokozela cifukwa cake amaona kuti kucita zimenezi n’kulakwa komanso mavuto ake. Buku lina limati: “Acinyamata ambili amene amadziŵa kuti makolo awo amaona kuti n’kulakwa kugonana asanalowe m’banja amapewa kugonana.”—Beyond the Big Talk.

Muzikhala citsanzo cabwino. Muzitsatila mfundo zimene mumaphunzitsa ana anu. Muyenela kudzifunsa kuti, Kodi nimaseka munthu wina akanena nthabwala zokhudza kugonana? Nanga kodi nimavala kapena kucita zinthu zofuna kukopa ena? Ngati mumacita zimenezi, ana anu sangatsatile mfundo zabwino zimene mumawaphunzitsa.Lemba lothandiza: Aroma 2:21.

Musamangowauze kuti kugonana n’koipa. Kugonana ni mphatso yocokela kwa Mulungu ndipo kungakhale kosangalatsa kwambili kwa anthu amene ali pa banja. (Miyambo 5:18, 19) Muziuza mwana wanu kuti iyenso adzatha kusangalala na kugonana akadzalowa m’banja popanda kukumana na mavuto omwe angabwele akagonana na munthu wina panopa.—1 Timoteyo 1:18, 19.