Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mudziŵa?

Kodi Mudziŵa?

Ndani anali tate wake wa Yosefe?

Yosefe, kalipentala wa ku Nazareti, anali atate a Yesu omulela. Nanga ndani anali atate ake a Yosefe? Mzele wobadwila wa Yesu wolembedwa mu Uthenga Wabwino wa Mateyu umaonetsa kuti anali Yakobo winawake, koma Luka anakamba kuti Yosefe anali “mwana wa Heli.” N’cifukwa ciani analemba zosiyana?—Luka 3:23; Mateyu 1: 16.

Mateyu analemba kuti: “Yakobo anabeleka Yosefe.” Iye anagwilitsila nchito liu la Cigilika poonetsa kuti Yakobo anali atate a Yosefe omubeleka. Conco, Mateyu anaonetsa mzele wobadwila wa Yosefe, umene ndi banja lacifumu la Davide, mmene Yesu woyenelela mwalamulo kukhala pa mpando wacifumu, anali kudzacokela.

Koma Luka analemba kuti: “Yosefe, mwana wa Heli.” Mau akuti “mwana wa,” angatanthauze “mpongozi wa.” Nkhani yofanana ndi imeneyi ikupezeka pa Luka 3:27, pamene Salatiyeli, amene atate ake omubeleka anali a Yekoniya, akuchulidwa kuti “mwana wa Neri.” (1 Mbiri 3:17; Mateyu 1:12) Zikuoneka kuti Salatiyeli anakwatila mwana wamkazi wa Neri amene sanachulidwe dzina. Motelo, iye anakhala mpongozi wa Neri. N’cimodzimodzi ndi Yosefe. Iye anali “mwana” wa Heli, popeza kuti anakwatila Mariya, mwana wa Heli. Conco, Luka akuonetsa mzele wobadwila wa Yesu “monga munthu” kupitila mwa Mariya, amai ake omubeleka. (Aroma 1:3) Apa tingakambe kuti Baibulo limationetsa mizele iŵili yosiyana imene Yesu anabadwilamo.

Kodi m’nthawi za Baibulo kunali nsalu za mitundu yotani?

Ubweya wopakidwa penti anaupeza m’mphanga lina pafupi ndi Nyanja Yakufa, ndipo unaonetsa deti la m’ma 135 C.E.

Kale ku Middle East, ubweya wa nkhosa unali kugwilitsidwa nchito kwambili kupangila nsalu mofanana ndi ubweya wa mbuzi ndi ngamila. Nsalu zimene zinali zofala kwambili zinali zaubweya. Ndipo nthawi zambili, Baibulo limakambapo za nkhosa, kumeta ubweya, ndiponso zovala za ubweya. (1 Samueli 25:2; 2 Mafumu 3:4; Yobu 31:20) Mbeu za fulakesi zopangila nsalu zinali kulimidwa ku Iguputo ndi ku Isiraeli. (Genesis 41:42; Yoswa 2:6) Aisiraeli a m’nthawi za Baibulo ayenela kuti sanali kulima thonje, koma Malemba amakamba kuti thonje anali kugwilitsidwa nchito ku Perisiya. (Esitere 1:6) Nsalu zasilika zinali za mtengo wapatali, ndipo mwacionekele zinali kupezeka ndi anthu amalonda ocokela m’maiko ena a kum’maŵa kwa dziko lapansi.—Chivumbulutso 18:11, 12.

Buku lina lakuti Jesus and His World linati: “Ubweya unali kupezeka m’mitundu yosinasiyana, wina unali woyela, wina wofiilila wooneka ngati wakuda.” Kuonjezela apo, ubweya anali kuupaka penti. Penti wofiilila wokwela mtengo anali kuutenga ku nkhono zina. Zinthu monga zomela zosiyanasiyana, mizu, masamba, ndiponso tudoyo, zinali kugwilitsidwa nchito kupangila penti wofiila, wacikasu, wabulu, ndiponso wakuda.