Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YA PACIKUTO | BAIBULO—MMENE YAPULUMUKILA

Baibulo Yapulumuka Citsutso

Baibulo Yapulumuka Citsutso

VUTO LIMENE LINALIPO: Abusa ndi atsogoleli a ndale ambili anali ndi zolinga zosagwilizana ndi uthenga wa m’Baibulo. Nthawi zambili, anali kuletsa anthu kukhala ndi Baibulo, kuisindikiza, kapena kuimasulila. Tiyeni tione zitsanzo ziŵili izi:

  • Ca m’ma 167 B.C.E.: Mfumu yaciselukasi dzina lake Antiyokasi Epifanasi, amene anali kukakamiza Ayuda kuyamba cipembedzo ca Cigiriki, analamula kuti mipukutu yonse ya Malemba a Ciheberi iwonongedwe. Wolemba mbili yakale Heinrich Graetz, analemba kuti nduna za mfumuyi “zikapeza mipukutu ya Cilamulo zinali kuing’amba ndi kuitentha.” Analembanso kuti nduna zimenezi “zinali kupha anthu onse amene anali kuŵelenga malemba kuti apeze citonthozo ndi cilimbikitso.”

  • Zaka za m’ma 500 C.E. mpaka 1500 C.E.: Abusa ena Acikatolika anali kukwiya kwambili akaona mamembala awo ena akulalikila zimene Baibulo imaphunzitsa, m’malo mwa ziphunzitso za Cikatolika. Abusawo akaona anthu akuseŵenzetsa mabuku ena a m’Baibulo, kusiyapo buku la Masalimo la Cilatini, anali kuwaona ngati ampatuko. Atsogoleli a chalichi cina analamula amuna ena kuti ‘akafufuze mwakhama anthu ampatuko m’nyumba zonse zimene anali kuganizila kuti muli Mabaibulo. . . . Nyumba iliyonse imene apezamo anthu ampatuko inafunika kuwonongedwa.’

Adani amenewa akanakwanitsa kuononga Mabaibulo onse, sembe kulibe Baibulo masiku ano.

Baibulo ya Cingelezi ya William Tyndale inatetezeka ngakhale kuti atsogoleli ena anali kuletsa anthu kukhala ndi Baibulo, anali kuitentha, ndipo anapha Tyndale mu 1536

MMENE BAIBULO INATETEZEKELA: Ngakhale kuti Mfumu Antiyokasi inayesetsa kuononga Mabaibulo m’dziko la Isiraeli, panthawiyo Ayuda anali atafalikila kale m’maiko ena ambili. Ndipo akatswili amakamba kuti pofika m’nthawi ya atumwi, Ayuda oposa 60 pelesenti sanali kukhala m’dziko la Isiraeli. Ayuda anali kusunga mipukutu ya Malemba m’masunagoge awo. Patapita zaka zambili, anthu ena, kuphatikizapo Akhiristu, anayamba kugwilitsila nchito mipukutu imeneyo.—Machitidwe 15:21.

M’zaka za pakati pa 500 C.E. ndi 1500 C.E., anthu okonda Baibulo anapitiliza kuimasulila ndi kukopela Malemba ake ngakhale kuti anali kuzunzidwa kwambili. Pofika zaka za m’ma 1400 C.E., zigawo za Baibulo ziyenela kuti zinali zitamasulidwa kale m’zinenelo 33. Zimenezi zinacitika akalibe kutulukila makina opulintila. Pambuyo potulukila makina opulintila, nchito yomasulila ndi kusindikiza Mabaibulo inayamba kucitika mofulumila kwambili.

ZOTSATILAPO ZAKE: Baibulo ni buku imene yamasulidwa ndi kufalitsidwa kwambili m’mbili yonse ya anthu, ngakhale kuti mafumu amphamvu ndi abusa a cipembedzo anayesetsa kuti aiwononge. Baibulo yasintha kwambili malamulo a m’maiko ena, makhalidwe a anthu, ndi zinenelo zambili.