Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mulungu Ni Wacifundo Zoona?

Kodi Mulungu Ni Wacifundo Zoona?

ZIMENE CILENGEDWE CIMATIPHUNZITSA

Cifundo cimatanthauza “kukhudzika na mavuto a munthu wina mwa kuganizila mmene mukanamvelela sembe ndimwe.” Katswili wa matenda a zamaganizo, Dr. Rick Hanson anati, “Cifundo timacita kubadwa naco.”

GANIZILANI IZI: N’cifukwa ciani ife anthu timaonetsa cifundo kupambana colengedwa cina ciliconse padziko lapansi? Baibo imakamba kuti Mulungu analenga anthu m’cifanizilo cake. (Genesis 1:26) Tinalengedwa m’cifanizilo ca Mulungu m’njila yakuti tingatengele makhalidwe ake na kuwaonetsa kwa ena. Conco, pamene cifundo cisonkhezela anthu okoma mtima kuthandiza ena, iwo amaonetsa cifundo ca Mlengi wawo, Yehova Mulungu.—Miyambo 14:31.

ZIMENE BAIBO IMATIPHUNZITSA PA CIFUNDO CA MULUNGU

Mulungu amaticitila cifundo, ndipo cimamuŵaŵa akaona kuti tivutika. Ponena za Aisiraeli akale, amene anapilila ukapolo wankhanza ku Iguputo, komanso zaka 40 zovuta m’cipululu, Baibo imati: “Pamene iwo anali kuvutika m’masautso awo onse, iyenso anali kuvutika.” (Yesaya 63:9) Mulungu sanali kudziŵa cabe mavuto awo. Koma nayenso anali kuvutika nawo pamodzi. Iye anati: “Ndaona nsautso ya anthu anga.” (Ekisodo 3:7) Anakambanso kuti: “Amene akukukhudzani, akukukhudza mwana wa diso langa.” (Zekariya 2:8) Pamene ena aticitila zoipa, iye cimamuŵaŵa kwambili mu mtima.

Ngakhale kuti tingamadziimbe mlandu na kudzimva wosayenela cifundo ca Mulungu, Baibo imatitsimikizila kuti, “Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu.” (1 Yohane 3:19, 20) Mulungu amatidziŵa bwino kwambili kuposa mmene ife timazidziŵila. Iye amadziŵa zonse zokhudza mavuto athu, maganizo athu, na mmene timvelela. Ndipo amaticitila cifundo.

Tingayang’ane kwa Mulungu kuti atitonthoze, kutipatsa nzelu, komanso kuticilikiza, podziŵa kuti amathandiza anthu amene ali pamavuto

Malemba amatitsimikizila kuti

  • “Inu mudzaitana ndipo Yehova adzakuyankhani. Mudzafuula popempha ndipo iye adzayankha kuti, ‘Ndikumva lankhulani!’”—YESAYA 58:9.

  • “‘Maganizo anga kwa inu ndikuwadziwa bwino. Ndikuganizila zokupatsani mtendele osati masoka, kuti mukhale ndi ciyembekezo cabwino ndiponso tsogolo labwino,’ watelo Yehova. ‘Mudzaitanila pa ine komanso mudzabwela ndi kupemphela kwa ine ndipo ine ndidzakumvetselani.’”—YEREMIYA 29:11, 12.

  • “Sungani misozi yanga m’thumba lanu lacikopa. Kodi misozi yanga sili m’buku lanu?”—SALIMO 56:8.

MULUNGU AMATIDELA NKHAWA, KUTIMVETSETSA, NA KUTIMVELELA CIFUNDO

Kodi kudziŵa kuti Mulungu amatidela nkhawa kungatithandize kupilila mavuto? Ganizilani zimene zinacitikila Maria. Iye anati:

“N’nayamba kuona kuti umoyo ni wovuta komanso wopanda cilungamo. Cinaniŵaŵa maningi pamene mwana wanga wa zaka 18 anamwalila pambuyo podwala matenda a khansa kwa zaka ziŵili. N’nakwiila Yehova cifukwa cosam’teteza na kusam’cilitsa!

“Patapita zaka 6, mlongo wina wacikondi komanso wacifundo mu mumpingo, anamvetsela pamene n’nali kumufotokozela mmene n’nali kumvelela kuti Yehova sanikonda. Pambuyo ponimvetsela kwa maawazi popanda kunidula mau, iye anagwila mau lemba la 1 Yohane 3:19, 20 imene inanikhudza mtima kwambili. Imakamba kuti: ‘Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu ndipo amadziwa zonse.’ Iye ananifotokozela kuti Yehova amamvetsetsa mavuto athu.

“Ngakhale n’conco, zinali zovuta kwa ine kuti nicotse mkwiyo wanga! Kenako n’naŵelenga Salimo 94:19, imene ikamba kuti: ‘Malingalilo osautsa atandiculukila mumtima mwanga, Mawu anu otonthoza anayamba kusangalatsa moyo wanga.’ N’namvela monga kuti mavesiwo anangolembela ine! M’kupita kwa nthawi, n’nayamba kuona kuti kuuza Yehova mavuto anga n’kotonthoza kwambili, podziŵa kuti amamvetsela na kutimvetsetsa.”

N’zolimbikitsa kwambili kudziŵa kuti Mulungu amatimvetsetsa, komanso kutimvelela cifundo! Koma n’cifukwa ciani pali mavuto ambili conco? Kodi n’cifukwa cakuti Mulungu akutilanga pa zolakwa zathu? Kodi Mulungu adzacitapo kanthu kuti athetse mavuto onse? Nkhani zokonkhapo zidzayankha mafunso amenewa.